Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Aheberi 4:12—“Mawu a Mulungu Ndi Amoyo Komanso Amphamvu”

Aheberi 4:12—“Mawu a Mulungu Ndi Amoyo Komanso Amphamvu”

 “Chifukwa mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu, ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse. Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu komanso mafupa ndi mafuta amʼmafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.”—Aheberi 4:12, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Pakuti mau a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugawira moyo ndi mzimu, ndi zimfundo ndi mafuta a m’mafupa, nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.”—Ahebri 4:12, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Aheberi 4:12

 Mogwirizana ndi zomwe Baibulo limanena, uthenga wa Mulungu womwe anapereka kwa anthu, uli ndi mphamvu yodziwa maganizo athu enieni komanso zolinga zathu. Ndipo umathanso kusintha anthu kuti akhale ndi makhalidwe abwino.

 “Mawu a Mulungu ndi amoyo.” Mogwirizana ndi zomwe Baibulo a limanena, “mawu a Mulungu,” amatanthauza zomwe Mulungu analonjeza kapena cholinga chake chomwe anachifotokoza. Ndipo mbali yofunika kwambiri ya cholingacho ndi yakuti anthu omvera adzakhale padziko lapansi mwamtendere komanso mogwirizana mpaka kalekale.​—Genesis 1:28; Salimo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4.

 Kodi mawu kapena cholinga cha Mulungu chimakhala bwanji ‘chamoyo’? Chifukwa chimodzi ndi chakuti mawuwa kapena cholinga cha Mulungu, zimakhala ndi mphamvu yokhudza mitima ya anthu omwe amavomereza kutsogoleredwa ndi mawu kapena cholingacho. Ndipo zimenezi zimawathandiza kukhala ndi chiyembekezo komanso kukhala osangalala. (Deuteronomo 30:14; 32:47) Zomwe Mulungu analonjeza, zimakhalanso mawu “amoyo” m’njira yakuti Mulungu wamoyo amakhala akugwira ntchito kuti akwaniritse zomwe analonjeza. (Yohane 5:17) Mosiyana ndi anthufe, Mulungu salonjeza zinthu kenako n’kuziiwala kapena kudzazindikira nthawi ina kuti sangathe kuzikwaniritsa. (Numeri 23:19) Mawu ake “sadzabwerera kwa [iye] popanda kukwaniritsa cholinga chake.”​—Yesaya 55:10, 11.

 “Mawu a Mulungu . . . ndi amphamvu.” Mawu akuti “ndi amphamvu,” angatanthauzenso “kukwaniritsa chilichonse chomwe (mawuwo) akufuna kuti chikwaniritsidwe.” Choncho, chilichonse chimene Yehova b Mulungu wanena kapena kulonjeza sichidzalephera kukwaniritsidwa. (Salimo 135:6; Yesaya 46:10) Ndipotu Mulungu angathe kukwaniritsa zomwe analonjeza m’njira imene sitikuiganizira n’komwe.​—Aefeso 3:20. c

 Mawu a Mulungu amakhalanso “amphamvu” m’njira yakuti amathandiza anthu omwe amawalemekeza, kuti asinthe zochita ndi makhalidwe awo. Anthuwa amayamba kuyendera mfundo za Mulungu pa moyo wawo ndipo zimenezi zimakhudza kaganizidwe, zochita komanso zolinga zawo. (Aroma 12:2; Aefeso 4:24) Mwanjira imeneyi tingati ‘mawu a Mulungu amakhala akugwira ntchito’ mwa anthu amenewa.​—1 Atesalonika 2:13.

 “Mawu a Mulungu . . . ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.” Mophiphiritsira, tingati mawu a Mulungu ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lomwe anthu amapanga chifukwa ali ndi mphamvu zolowa mpaka mkatikati. Uthenga wa Mulungu ungathe kufika munthu mumtima kapena kusintha umunthu wake wamkati, zomwe sizingatheke ndi maphunziro a sukulu zanzeru za anthu. Zimenezi zikuonekera bwino mu zomwe lemba la Aheberi 4:12 likupitiriza kunena kuti:

 “Mawu a Mulungu . . . amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu komanso mafupa ndi mafuta amʼmafupa.” M’Baibulo mawu akuti “moyo,” angatanthauze mmene munthu winawake amaonekera. Pomwe mawu akuti “mzimu,” angatanthauze mmene munthuyo alilidi mumtima mwake. (Agalatiya 6:18) Mophiphiritsira, “mawu a Mulungu” amalowa mpaka mkati mwa “mafuta am’mafupa.” Zomwe zikutanthauza mmene timamvera kapena zomwe timaganiza mkatikati mwenimweni mwa mtima mwathu. Chifukwa chakuti mawu a Mulungu amatha kuzindikira mmene tilili mkati mwamtima wathu, momwe ena sangathe kuonamo, angathe kutithandiza kusintha kuti tikhale anthu abwino. Zimenezi zimasangalatsa Mlengi wathu komanso zimatithandiza kukhala osangalala.

 “Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake.” Zimene munthu amachita akamva mawu a Mulungu, zimasonyeza zimene zili mumtima mwake komanso zolinga zake zenizeni zomwe zimakhudzanso khalidwe lomwe amasonyeza. Mwachitsanzo, munthu akamatsatira zimene mawu a Mulungu amaphunzitsa, n’kusintha zinthu zina pa moyo wake, amasonyeza kuti ndi wodzichepetsa komanso kuti ndi wokhulupirika. Iye amachita zimenezi pofuna kusangalatsa Mlengi wake. Koma ngati amapezera zifukwa mawu a Mulungu, amasonyeza kuti ali ndi mtima wonyada kapena wodzikonda. Kapena amachita zimenezi ndi cholinga chofuna kuikira kumbuyo makhalidwe amene Mulungu amadana nawo.​—Yeremiya 17:9; Aroma 1:24-27.

 Buku lina limati, mawu a Mulungu “angathe kulowa mpaka kukafika m’maganizo obisika a mumtima mwathu.” Palibe mbali iliyonse ya umunthu wathu wamkati yomwe Mulungu sangathe kuyiona kapena yomwe mawu ake sangathe kuonetsa poyera. Lemba la Aheberi 4:13 limanena kuti, “zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.”

Nkhani yonse ya pa Aheberi 4:12

 Buku la m’Baibulo la Aheberi ndi kalata youziridwa imene mtumwi Paulo analembera Akhristu a Chiyuda omwe ankakhala ku Yerusalemu ndi ku Yudeya cha m’ma 61 C.E.

 Muchaputala 3 ndi 4, Paulo anagwiritsa ntchito chitsanzo cha Aisiraeli akale, ngati chenjezo lopita kwa Akhristu. (Aheberi 3:8-12; 4:11) Yehova analonjeza Aisiraeli kuti adzawapulumutsa ku ukapolo n’kuwapatsa dziko lomwe ‘adzakhalemo motetezeka.’ (Deuteronomo 12:9, 10) Komabe atachoka ku Iguputo ankasonyeza mobwerezabwereza kuti sankakhulupirira malonjezo a Mulungu ndipo nthawi zambiri sankamvera malamulo ake. Zotsatirapo zake, iwo ‘sanalowe nawo mumpumulo wake (wa Mulungu)’ komanso kukhala naye pa ubwenzi ndipo anafera m’chipululu. Ngakhale kuti m’badwo wotsatira ndi womwe unadzalandira Dziko Lolonjezedwalo, koma nawonso anayamba kuchita zinthu zosonyeza kusamvera malamulo ake. Zimenezi zinachititsa kuti akumane ndi mavuto ambiri.​—Nehemiya 9:29, 30; Salimo 95:9-11; Luka 13:34, 35.

 Paulo anafotokoza kuti Akhristu ayenera kuphunzirapo kanthu pa chitsanzo choipa cha Aisiraeli osakhulupirikawa. Mosiyana ndi iwowo, tikhoza kulowa mumpumulo wa Mulungu ngati timamvera mawu ake komanso kukhulupirira kwambiri malonjeza ake.​—Aheberi 4:1-3, 11.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti mumvetse bwino nkhani ya m’buku la Aheberi.

a Pa Aheberi 4:12, mawu akuti, “mawu a Mulungu” sanena kwenikweni za Baibulo. Komabe popeza Mulungu anakonza zoti malonjezo ake alembedwenso m’bukuli, zimenezi zikusonyeza kuti lemba la Aheberi 4:12 lingagwirenso ntchito ponena za Baibulo.

b Yehova ndi dzina lenileni la Mulungu. (Salimo 83:18) Werengani nkhani yakuti “Kodi Yehova Ndi Ndani?