JW LIBRARY
Mafunso Ofunsidwa Kawirikawiri Okhudza JW Library (Pa Zipangizo za Windows)
JW Library ingathe kugwira ntchito pa mafoni ndi zipangizo zimene zimayendera mapulogalamu awa:
Android 7.0 kapena ina yaposachedwapa
iOS 15.0 kapena ina yaposachedwapa
Windows 10 ya 1903 ena ina yaposachedwapa
Kuti JW Library ikhale yotetezeka komanso izigwira bwino ntchito, tasiya kuigwiritsa ntchito pa zipangizo zina zonse zoyendera mapulogalamu akale. Nthawi ndi nthawi tizikuuzani kuti JW Library ikufunika mapulogalamu atsopano kuti izigwira bwino ntchito. Choncho tikukulimbikitsani kuti muzionetsetsa kuti foni yanu kapena chipangizo chanu chikuyendera pulogalamu yatsopano kwambiri. Ngati simungakwanitse kuika pulogalamu yogwirizana ndi JW Library pachipangizo chanu, mukhozabe kugwiritsa ntchito JW Library pachipangizocho, koma simuzilandira zinthu zimene zasintha mu JW Library.
Mitunduyi ikugwirizana kwambiri ndi magulu 8 a mabuku a m’Baibulo omwe afotokozedwa pa Funso 19, m’kabuku kakuti Kodi M’Baibulo Muli Nkhani Zotani?
Vuto: Nditaika JW Library yatsopano, panabwera uthenga wakuti manotsi ndi zinthu zimene ndinachonga zapita. Notsi zonse zimene ndinalemba, matagi, zimene ndinachonga komanso zinthu zina sindingazionenso.
Zimene Mungachite: Ngati mwaika m’chipangizo chanu pulogalamu yatsopano vutoli likhoza kutha. Ikani pulogalamu yatsopano n’kutsatira malangizo amene angabwere pa sikirini kuti notsi ndi zinthu zina zibwerere.
Ngati mukuvutika kudawuniloda zinthu zongomvetsera komanso mavidiyo, tsatirani njira zili m’munsizi kuti mutsimikizire ngati laibulale yanu ya Mavidiyo ndi Nyimbo yakonzedwa bwino papulogalamu ya Windows komanso ngati yasankhidwa pa JW Library.
Tsegulani File Explorer, pa Windows ndi kudina pa View. Kenako dinani Navigation pane ndi kutsegula pomwe palembedwa kut Show libraries.
Chakumanzereko, sankhani ndikutambasula Libraries.
Tsopano mutha kuona foda yolembedwa Music komanso ya Videos. Ngati mafodawa sakuoneka, pangani right-click pa Libraries ndi kudina mawu akuti Restore default libraries.
Pangani right-click pafoda ya Videos n’kudina pa Properties ndipo muone foda yomwe ili pansi pa mawu akuti Library locations. Ku ma settings a JW Library mukufunika kusonyeza komwe fodayi ili. Kenako dinani pa Restore Defaults.
Pangani right-click foda ya Music, dinani Properties, ndipo muonetsetse foda yomwe ili pansi pa mawu akuti Library locations. Ku ma settings a JW Library mukufunika kusonyeza komwe fodayi ili. Kenako dinani pa Restore Defaults.
Pomaliza, tsatirani njira zotsatirazi kuti mutsimikizire ngati malaibulale a Videos ndi Music asankhidwa ku ma settings a JW Library:
Tsegulani JW Library, kenako dinani batani la Settings.
Ku ma Settings, tsimikizirani kuti mawu akuti Download audio programs to aikidwa kulaibulale ya Nyimbo komanso kuti mawu akuti Download videos to aikidwa kulaibulale ya Mavidiyo omwe munawaona poyamba mu File Explorer.
Ngati zikukuvutanibe kudawuniloda mafailo ongomvetsera kapena mavidiyo, tsimikizirani kuti muli ndi chilolezo chosunga mafailo kumafoda a Nyimbo ndi Mavidiyo popanga failo yatsopano mkati mwa foda iliyonse. Kuti mudziwe zambiri, pitani pa Microsoft support section kapena funsani mnzanu amene amadziwa bwino za Windows.
Mnzanu yemwe amadziwa bwino JW Library akhoza kukuthandizani. Ngati sangakwanitse kukuthandizani, funsani ku ofesi ya nthambi yathu yomwe ili pafupi.