Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Uthenga Wabwino Wolembedwa na Mateyo

Macaputala

Za m'Bukuli

  • 1

    • Mzele wa makolo a Yesu Khristu (1-17)

    • Kubadwa kwa Yesu (18-25)

  • 2

    • Okhulupilila nyenyezi apita kukaona Yesu (1-12)

    • Athaŵila ku Iguputo (13-15)

    • Herode akupha ana aamuna (16-18)

    • Abwelela ku Nazareti (19-23)

  • 3

    • Ulaliki wa Yohane M’batizi (1-12)

    • Ubatizo wa Yesu (13-17)

  • 4

    • Mdyelekezi ayesa Yesu (1-11)

    • Yesu ayamba kulalikila ku Galileya (12-17)

    • Yesu aitana ophunzila ake oyamba (18-22)

    • Yesu alalikila, kuphunzitsa, na kucilitsa (23-25)

  • 5

    • ULALIKI WA PA PHILI (1-48)

      • Yesu ayamba kuphunzitsa pa phili (1, 2)

      • Zinthu 9 zopangitsa anthu kukhala odala (3-12)

      • Mcele na nyale (13-16)

      • Yesu anabwela kudzakwanilitsa Cilamulo (17-20)

      • Uphungu pa nkhani ya mkwiyo (21-26), cigololo (27-30), kusudzulana (31, 32), malumbilo (33-37), kubwezela (38-42), kukonda adani athu (43-48)

  • 6

    • ULALIKI WA PA PHILI (1-34)

      • Pewani kucita zabwino modzionetsela (1-4)

      • Mmene tingapemphelele (5-15)

        • Pemphelo la citsanzo (9-13)

      • Kusala kudya (16-18)

      • Cuma padziko lapansi komanso kumwamba (19-24)

      • Lekani kuda nkhawa (25-34)

        • Pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba (33)

  • 7

    • ULALIKI WA PA PHILI (1-27)

      • Lekani kuweluza ena (1-6)

      • Pemphanibe, funa-funanibe, gogodanibe (7-11)

      • Khalidwe Lopambana (12)

      • Geti yopanikiza (13, 14)

      • Mudzawadziŵa na zipatso zawo (15-23)

      • Nyumba yomangidwa pa thanthwe, nyumba yomangidwa pa mcenga (24-27)

    • Khamu la anthu lidabwa na kaphunzitsidwe ka Yesu (28, 29)

  • 8

    • Wakhate acilitsidwa (1-4)

    • Cikhulupililo ca kapitawo wa asilikali (5-13)

    • Yesu acilitsa anthu ambili ku Kaperenao (14-17)

    • Mmene tingatsatilile Yesu (18-22)

    • Yesu aleketsa cimphepo ca mkuntho pa nyanja (23-27)

    • Yesu atumiza ziŵanda m’nkhumba (28-34)

  • 9

    • Yesu acilitsa munthu wakufa ziwalo (1-8)

    • Yesu aitana Mateyo (9-13)

    • Funso pa nkhani ya kusala kudya (14-17)

    • Mwana wamkazi wa Yairo; mayi agwila covala cakunja ca Yesu (18-26)

    • Yesu acilitsa anthu akhungu na munthu wosalankhula (27-34)

    • Zokolola n’zambili koma anchito ni ocepa (35-38)

  • 10

    • Atumwi 12 (1-4)

    • Malangizo a ulaliki (5-15)

    • Ophunzila a Yesu adzazunzidwa (16-25)

    • Opani Mulungu osati anthu (26-31)

    • Lupanga osati mtendele (32-39)

    • Kulandila ophunzila a Yesu (40-42)

  • 11

    • Yohane M’batizi atamandidwa (1-15)

    • Yesu adzudzula m’badwo wopanda cikhulupililo (16-24)

    • Yesu atamanda Atate wake cifukwa cokonda anthu odzicepetsa (25-27)

    • Joko ya Yesu ni yotsitsimula (28-30)

  • 12

    • Yesu ndiye “Mbuye wa Sabata” (1-8)

    • Munthu wa dzanja lopuwala acilitsidwa (9-14)

    • Mtumiki wa Mulungu wokondedwa (15-21)

    • Yesu atulutsa ziŵanda mwa mphamvu ya mzimu woyela (22-30)

    • Chimo limene silingakhululukidwe (31, 32)

    • Mtengo umadziŵika na zipatsa zake (33-37)

    • Cizindikilo ca Yona (38-42)

    • Mzimu wonyansa ukabwelela mwa munthu (43-45)

    • Amayi a Yesu na abale ake (46-50)

  • 13

    • MAFANIZO ONENA ZA UFUMU (1-52)

      • Wofesa mbewu (1-9)

      • Cifukwa cake Yesu anali kuseŵenzetsa mafanizo (10-17)

      • Kufotokoza tanthauzo la wofesa mbewu (18-23)

      • Tiligu na namsongole (24-30)

      • Kanjele ka mpilu na zofufumitsa (31-33)

      • Kuseŵenzetsa mafanizo kunakwanilitsa ulosi (34, 35)

      • Kufotokoza tanthauzo la tiligu na namsongole (36-43)

      • Cuma cobisika na ngale yamtengo wapatali (44-46)

      • Khoka (47-50)

      • Cuma catsopano komanso cakale (51, 52)

    • Yesu akanidwa kwawo (53-58)

  • 14

    • Yohane M’batizi adulidwa mutu (1-12)

    • Yesu adyetsa anthu 5,000 (13-21)

    • Yesu ayenda pamadzi (22-33)

    • Yesu acilitsa anthu ku Genesareti (34-36)

  • 15

    • Kuvumbula miyambo ya anthu (1-9)

    • Zodetsa munthu zimacokela mu mtima (10-20)

    • Cikhulupililo cacikulu ca mayi wa ku Foinike (21-28)

    • Yesu acilitsa matenda osiyana-siyana (29-31)

    • Yesu adyetsa anthu 4,000 (32-39)

  • 16

    • Apempha cizindikilo (1-4)

    • Zofufumitsa za Afarisi na Asaduki (5-12)

    • Makiyi a Ufumu (13-20)

      • Mpingo udzamangidwa pa thanthwe (18)

    • Yesu anenelatu za imfa yake (21-23)

    • Zimene ophunzila oona a Yesu amacita (24-28)

  • 17

    • Kusandulika kwa Yesu (1-13)

    • Cikhulupililo cocepa ngati kanjele ka mpilu (14-21)

    • Kaciŵili, Yesu anenelatu za imfa yake (22, 23)

    • Akhoma msonkho na khobili lotengedwa m’kamwa mwa nsomba (24-27)

  • 18

    • Wamkulu kwambili mu Ufumu wa kumwamba (1-6)

    • Zopunthwitsa (7-11)

    • Fanizo la nkhosa yosocela (12-14)

    • Mmene tingabwezele m’bale wathu (15-20)

    • Fanizo la kapolo wosakhululukila mnzake (21-35)

  • 19

    • Ukwati na cisudzulo (1-9)

    • Mphatso ya umbeta (10-12)

    • Yesu adalitsa ana (13-15)

    • Funso la mnyamata wacuma (16-24)

    • Kudzimana cifukwa ca Ufumu (25-30)

  • 20

    • Ogwila nchito m’munda wa mpesa komanso malipilo awo ofanana (1-16)

    • Yesu akambilatunso za imfa yake (17-19)

    • Apempha malo apamwamba mu Ufumu (20-28)

      • Yesu ni dipo lowombolela anthu ambili (28)

    • Yesu acilitsa anthu aŵili akhungu (29-34)

  • 21

    • Yesu atamandidwa poloŵa mu Yerusalemu (1-11)

    • Yesu ayeletsa kacisi (12-17)

    • Atembelela mtengo wa mkuyu (18-22)

    • Anthu akayikila mphamvu za Yesu (23-27)

    • Fanizo la ana aŵili (28-32)

    • Fanizo la alimi akupha (33-46)

      • Mwala wa pakona wofunika kwambili ukanidwa (42)

  • 22

    • Fanizo la phwando la ukwati (1-14)

    • Mulungu na Kaisara (15-22)

    • Funso pa nkhani ya kuuka kwa akufa (23-33)

    • Malamulo aŵili aakulu kwambili (34-40)

    • Kodi Khristu ni mwana wa Davide? (41-46)

  • 23

    • Musamatengele alembi na Afarisi (1-12)

    • Tsoka kwa alembi na Afarisi (13-36)

    • Yesu alilila Yerusalemu (37-39)

  • 24

    • CIZINDIKILO CA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-51)

      • Nkhondo, njala, zivomezi (7)

      • Uthenga wabwino udzalalikidwa (14)

      • Cisautso cacikulu (21, 22)

      • Cizindikilo ca Mwana wa munthu (30)

      • Mtengo wa mkuyu (32-34)

      • Mofanana na masiku a Nowa (37-39)

      • Khalanibe maso (42-44)

      • Kapolo wokhulupilika na woipa (45-51)

  • 25

    • CIZINDIKILO CA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-46)

      • Fanizo la anamwali 10 (1-13)

      • Fanizo la matalente (14-30)

      • Nkhosa na mbuzi (31-46)

  • 26

    • Ansembe akonza ciwembu cakuti aphe Yesu (1-5)

    • Yesu athilidwa mafuta onunkhila (6-13)

    • Pasika wothela komanso kupelekedwa kwa Yesu (14-25)

    • Kukhazikitsidwa kwa Mgonelo wa Ambuye (26-30)

    • Yesu akambilatu kuti Petulo adzamukana (31-35)

    • Yesu apemphela m’munda wa Getsemane (36-46)

    • Yesu agwidwa (47-56)

    • Yesu azengedwa mlandu m’Khoti Yaikulu ya Ayuda (57-68)

    • Petulo akana Yesu (69-75)

  • 27

    • Yesu apelekedwa kwa Pilato (1, 2)

    • Yudasi adzimangilila (3-10)

    • Yesu aonekela pamaso pa Pilato (11-26)

    • Yesu acitidwa zacipongwe (27-31)

    • Amukhomelela pa mtengo ku Gologota (32-44)

    • Imfa ya Yesu (45-56)

    • Yesu aikidwa m’manda (57-61)

    • Akhwimitsa citetezo pa manda a Yesu (62-66)

  • 28

    • Yesu aukitsidwa (1-10)

    • Asilikali apatsidwa ndalama kuti azikamba zabodza (11-15)

    • Lamulo la kupanga ophunzila (16-20)