Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

October 28–November 3

MASALIMO 103-104

October 28–November 3

Nyimbo 30 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Iye Amakumbukila “Kuti Ndife Fumbi”

(Mph. 10)

Khalidwe la cifundo limapangitsa Yehova kukhala wololela (Sal. 103:8; w23.07 21 ¶5)

Iye samatisiya tikalakwitsa (Sal. 103:9, 10; w23.09 6-7 ¶16-18)

Iye satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse (Sal. 103:14; w23.05 26 ¶2)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimakhala wololela pocita zinthu na mnzanga wa mu ukwati potengela citsanzo ca Yehova?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 104:24​—Kodi vesiyi itiphunzitsa ciyani za mphamvu za kulenga za Yehova? (cl-CN 55 ¶18)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 104:1-24 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Kambilanani vidiyo yakuti Takulandilani ku Phunzilo Lanu la Baibo na munthu amene anavomela kuphunzila Baibo. (th phunzilo 9)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 6​—Mutu: Mwamuna ayenela kukonda mkazi wake “mmene amadzikondela yekha.” (th phunzilo 1)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 44

7. Kodi Mumadziŵa Zimene Simungakwanitse Kucita?

(Mph. 15) Kukambilana.

Yehova amakondwela tikamacita zonse zimene tingathe pomutumikila ndipo nafenso timasangalala. (Sal. 73:28) Komabe, pamene tikuyesetsa kucita zimene tingathe, tiyenelanso kukumbukila kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse. Tikatelo, tidzapewa kukhala na nkhawa komanso kukhumudwa.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Tingacite Zambili mwa Kuyembekezela Zinthu Zotheka. Ndiyeno funsani omvela kuti:

  • Kodi Yehova amafuna kuti tizicita ciyani? (Mika 6:8)

  • N’ciyani cinathandiza mlongo wacitsikana kuti acepetseko nkhawa imene anali nayo yofuna kukwanilitsa colinga cake?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 55 na Pemphelo