4-B
Zocitika Zazikulu Paumoyo wa Yesu wa Padziko—Ciyambi ca Utumiki wa Yesu
NTHAWI |
MALO |
COCITIKA |
MATEYU |
MALIKO |
LUKA |
YOHANE |
---|---|---|---|---|---|---|
Ca kumapeto kwa 29 |
Mtsinje wa Yorodano, mwina pafupi ndi kapena kuoloka Yorodano |
Yesu abatizika ndi kudzozedwa; Yehova amulengeza kuti ndi Mwana wake ndi kumuvomeleza |
1:32-34 |
|||
Cipululu ca ku Yudeya |
Ayesedwa ndi Mdyelekezi |
|||||
Betaniya kutsidya la Yorodano |
Yohane M’batizi azindikila Yesu kuti ndi Mwanawankhosa wa Mulungu; ophunzila oyambilila akhala ndi Yesu |
1:15, 29-51 |
||||
Kana wa ku Galileya; Kaperenao |
Cozizwitsa coyamba pacikwati, asandutsa madzi kukhala vinyo; acezela Kaperenao |
2:1-12 |
||||
30, Pasika |
Yerusalemu |
Ayeletsa kacisi |
2:13-25 |
|||
Akamba ndi Nekodemo |
3:1-21 |
|||||
Yudeya; Ainoni |
Apita kudela la ku Yudeya, ophunzila ake abatizika; ulaliki womaliza wa Yohane wonena za Yesu |
3:22-36 |
||||
Tiberiyo; Yudeya |
Yohane aikidwa m’ndende; Yesu apita ku Galileya |
4:1-3 |
||||
Sukari, wa ku Samariya |
Paulendo wa ku Galileya, aphunzitsa Asamariya |
4:4-43 |