Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAWO 3

Mmene Mungathetsele Mavuto

Mmene Mungathetsele Mavuto

“Khalani okondana kwambili, pakuti cikondi cimakwilila macimo oculuka.”—1 Petulo 4:8

Pamene inu ndi mnzanu wa m’cikwati muyamba umoyo watsopano, padzakhala mavuto osiyanasiyana. Cimene cingacititse mavutowo ndi kusiyana maganizo, mmene mumaonela zinthu ndi mmene mumazicitila. Mwina mavuto angacokele kwina kapena cifukwa ca zotigwela zosayembekezeka.

Nthawi zina tingayese kuthaŵa mavuto, koma Baibulo limatilangiza kuti tiyenela kulimbana nao. (Mateyu 5:23, 24) Mwa kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo mungapeze thandizo labwino kwambili pamavuto anu.

1 KAMBILANANI VUTOLO

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: ‘Pali nthawi yolankhula.’ (Mlaliki 3:1, 7) Tsimikizani kuti muli ndi nthawi yokwanila yokambilana vutolo. Musam’bise mnzanu mmene mukumvelela ndi zimene mukuganiza pankhaniyo. Nthawi zonse ‘lankhulani zoona’ kwa mnzanu wa m’cikwati. (Aefeso 4:25) Kaya pakhale kukwiyitsana kwambili muyenela kupewa maganizo ofuna kumenyana. Kuyankha mofatsa kungacititse kuti nkhani isakule ndi kuti pasakhale mkangano waukulu.—Miyambo 15:4; 26:20.

Ngakhale kuti mungasiyane maganizo, cofunika ndi kukhalabe okoma mtima, ndipo osaiŵala kusonyezana cikondi ndi ulemu. (Akolose 4:6) Yesetsani kuthetsa vutolo mwamsanga, ndipo osaleka kukambitsilana.—Aefeso 4:26.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Pezani nthawi yabwino yokambilana vutolo

  • Pamene mnzanu akamba pewani cizoloŵezi com’dula mau. Mudzakamba ikafika nthawi yanu

2 KHALANI CETE NDI KUMVETSELA KWAMBILI

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.” (Aroma 12:10) Kumvetsela kwambili n’kofunika. Yesetsani kumvetsela malingalilo a mnzanu mwa ‘kumvelana cisoni’ ndiponso mwa kukhala ndi “maganizo odzicepetsa.” (1 Petulo 3:8; Yakobo 1:19) Musanamizile kuti mukumvetsela. Ngati n’zotheka lekezani zimene mukucita ndi kumvetsala kwambili zimene mnzanu akukamba, kapena pemphani kuti mukambilane nthawi ina. Ngati muona mnzanu wa m’cikwati monga wocita naye zinthu osati monga mdani, ‘simudzafulumila kukwiya.’—Mlaliki 7:9.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Mvetselani zonse zimene mnzanu akukamba, ngakhale kuti zimene akukamba simunazikonde

  • Onani tanthauzo la zimene akukamba. Onetsetsani zimene mnzanu akucita ndipo mvetselani mmene mau akumvekela

3 CITAMPONI KANTHU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: “Kugwila nchito iliyonse kumapindulitsa, koma kungolankhula mau cabe kumasaukitsa.” (Miyambo 14:23) Kungogwilizana mmene mungathetsele vutolo sikokwanila. Muyenela kucita zimene mwagwilizana. Zimenezo zingafune kulimbikila ndipo pamapeto pake mudzapindula. (Miyambo 10:4) Mukamacitila zinthu pamodzi monga banja, mudzakhala ndi “mphoto yabwino.”—Mlaliki 4:9.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Kambilanani zimene aliyense payekha adzacita kuti muthetse vutolo

  • Nthawi ndi nthawi muziona ngati mukusintha