Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAWO 1

Dalilani Mulungu Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe

Dalilani Mulungu Kuti Banja Lanu Likhale Lacimwemwe

“Amene analenga anthu pa ciyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi.” —Mateyu 19:4

Yehova * Mulungu ndiye anamanga cikwati coyamba. Baibulo limatiuza kuti anapanga mkazi woyamba ndi ‘kum’bweletsa kwa mwamuna.’ Adamu anakondwela kwambili cakuti anati: “Uyu tsopano ndiye fupa la mafupa anga ndi mnofu wa mnofu wanga.” (Genesis 2:22, 23) Yehova amafunabe kuti anthu okwatilana akhale acimwemwe.

Mukaloŵa m’banja, mungaziganiza kuti zinthu zonse zidzayamba kuyenda bwino. Komabe, kunena zoona, ngakhale mwamuna ndi mkazi amene amakondana kwambili nthawi zina adzakhala ndi mavuto. (1 Akorinto 7:28) M’kabuku kano, muli mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kusangalala m’cikwati canu ndi banja lanu ngati muzitsatila.—Salimo 19:8-11.

1 CITANI MBALI IMENE YEHOVA WAKUPATSANI

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: Mwamuna ndiye mutu wa banja.—Aefeso 5:23.

Ngati ndinu mwamuna wokwatila, Yehova amafuna kuti muzisamalila mkazi wanu mwacikondi. (1 Petulo 3:7) Iye anapanga mkazi monga wokuthandizani, ndipo amafuna kuti muzimulemekeza ndi kumukonda. (Genesis 2:18) Mufunika kukonda kwambili mkazi wanu cakuti muziika zofuna zake patsogolo pa zanu.—Aefeso 5:25-29.

Ngati ndinu mkazi wokwatiwa, Yehova amafuna kuti muzilemekeza kwambili mwamuna wanu ndi kum’thandiza kuti akwanilitse udindo wake. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:33) Mufunika kukhala kumbali yake pa zimene wasankha ndi kugwilizana naye ndi mtima wonse. (Akolose 3:18) Mukacita zimenezi, mudzakhala wokongola kwa mwamuna wanu ndi kwa Yehova.—1 Petulo 3:1-6.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Funsani mnzanu wa m’cikwati mmene mungakhalile mwamuna kapena mkazi wabwino. Mvetselani mwachelu, ndipo citani zimene mungathe kuti musinthe

  • Khalani woleza mtima. Padzapita nthawi kuti inu nonse aŵili mudziŵe zimene mungacite kuti muzikondweletsana

2 MUZISAMALILA KWAMBILI MKAZI KAPENA MWAMUNA WANU

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: Muyenela kusamalila kwambili zofuna za mwamuna kapena mkazi wanu. (Afilipi 2:3, 4) Muziona mnzanu wa m’cikwati kuti ndi wofunika kwambili, ndipo muzikumbukila kuti Yehova amafuna atumiki ake kukhala ‘odekha kwa onse.’ (2 Timoteyo 2:24) Baibulo limati: “Pali munthu amene amalankhula mosaganizila ndi mau olasa ngati lupanga, koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.” Conco sankhani bwino mau anu. (Miyambo 12:18) Mzimu wa Yehova udzakuthandizani kuti muzilankhula bwino ndiponso mwacikondi.—Agalatiya 5:22, 23; Akolose 4:6.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Musanakambilane nkhani zikuluzikulu ndi mkazi kapena mwamuna wanu, pemphelani kuti musapse mtima ndiponso kuti mukhale ndi maganizo ofuna kumvetsela

  • Ganizilani bwinobwino zimene mufuna kukamba ndiponso mmene mudzazikambila

3 MUZICITILA ZINTHU PAMODZI

ZIMENE BAIBULO LIMAKAMBA: Mukakwatilana mumakhala “thupi limodzi.” (Mateyu 19:5) Koma mukali anthu aŵili ndipo nthawi zina mugasiyane maganizo. Conco mufunika kuyesetsa kukhala ogwilizana pa zoganiza ndi zocita zanu. (Afilipi 2:2) Kugwilizana ndi kofunika kwambili popanga zosankha. Baibulo limati: “Zolinga zimakhazikika anthu akakambilana.” (Miyambo 20:18) Lolani kuti mfundo za m’Baibulo zizikutsogolelani pamene mupanga zosankha zikuluzikulu pamodzi.—Miyambo 8:32, 33.

ZIMENE MUNGACITE:

  • Muziuzana zakukhosi kwanu osati cabe zimene inu aŵili mukudziŵa kale

  • Coyamba muzifunsana musanacite zilizonse

^ par. 4 Baibulo limati, dzina la Mulungu ndi Yehova.