Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 20

Mmene Bungwe Lolamulila Limagwilila Nchito Masiku Ano

Mmene Bungwe Lolamulila Limagwilila Nchito Masiku Ano

Bungwe lolamulila la m’zaka za zana loyamba

Aŵelenga kalata yocokela ku bungwe lolamulila

M’zaka za zana loyamba, kagulu kocepa ka “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,” kanatumikila monga bungwe lolamulila ndipo kanali kupanga zosankha zazikulu m’malo mwa mpingo wonse wa Akristu odzozedwa. (Machitidwe 15:2) Kuti agwilizane pa cosankha cimodzi, anali kukambitsilana Malemba ndi kutsatila citsogozo ca mzimu wa Mulungu. (Machitidwe 15:25) Njila imeneyi ni imene imatsatilidwa masiku ano.

Mulungu amaligwilitsila nchito kucita cifunilo cake. Abale odzozedwa amene ali m’Bungwe Lolamulila amakonda kwambili Mau a Mulungu ndipo ali ndi cidziŵitso coculuka pa kayendetsedwe ka nchito yathu ndiponso pa kusamalila nkhani zauzimu. Iwo amakhala ndi miting’i wiki iliyonse kukambitsilana zosoŵa za gulu lonse la abale padziko lapansi. Monga mmene zinalili m’zaka za zana loyamba, io amapeleka malangizo a m’Baibo kupitila m’makalata kapena oyang’anila oyendela ndi anthu ena. Zimenezi zimathandiza anthu a Mulungu kukhala ndi maganizo amodzi ndi kucita zinthu mogwilizana. (Machitidwe 16:4, 5) Bungwe Lolamulila limayang’anila nchito yokonza cakudya ca ku uzimu, limalimbikitsa onse kuika nchito yolalikila za Ufumu patsogolo, ndipo limayang’anila nchito yoika abale pa maudindo.

Limatsatila citsogozo ca mzimu wa Mulungu. Bungwe Lolamulila limadalila citsogozo ca Yehova, Mfumu ya Cilengedwe Conse, ndiponso ca Yesu, Mutu wa mpingo. (1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23) Abale a m’bungwe limeneli sadziona kuti ni atsogoleli a anthu a Mulungu. Iwo, pamodzi ndi odzozedwa onse, “amatsatila [Yesu] Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.” (Chivumbulutso 14:4) Bungwe Lolamulila limayamikila mapemphelo athu.

  • Kodi ndani amene anali m’bungwe lolamulila m’zaka za zana loyamba?

  • Kodi Bungwe Lolamulila limacita ciani kuti lipeze citsogozo ca Mulungu masiku ano?