PHUNZILO 11
Ni Cifukwa Ciani Timacita Misonkhano Ikulu-ikulu?
N’cifukwa ciani nkhope za anthu awa zioneka zacimwemwe? Ali pa umodzi wa misonkhano yathu yaikulu. Kale atumiki a Mulungu analamulidwa kuti azisonkhana katatu pacaka. Ifenso timayembekezela mwacidwi misonkhano ikulu-ikulu. (Deuteronomo 16:16) Caka ciliconse timakhala ndi misonkhano itatu: misonkhano yadela iŵili yocita tsiku limodzi msonkhano uliwonse ndi msonkhano wa cigawo wa masiku atatu. Kodi misonkhano imeneyi imatithandiza m’njila ziti?
Imalimbitsa ubale wathu wacikristu. Aisiraeli anali kusangalala potamanda Yehova “pamsonkhano.” Ifenso timasangalala kumulambila pamisonkhano yapadela. (Salimo 26:12; 111:1) Misonkhano imeneyi imatipatsa mpata woonana ndi Mboni zocokela kumipingo ina kapena kumaiko ena ndi kuceza nazo. Masana, timadyela pamodzi cakudya pamalo a msonkhano. Zimenezi zimalimbikitsa mzimu wa ubwenzi pamaphwando auzimu amenewa. (Machitidwe 2:42) Pamisonkhano imeneyi timadzionela tokha cikondi cimene cimagwilizanitsa “gulu lonse la abale” padziko lonse lapansi.—1 Petulo 2:17.
Imatithandiza kupita patsogolo ku uzimu. Aisiraeli anapindulanso mwa ‘kumvetsa bwino mau’ a m’Malemba amene anawafotokezela. (Nehemiya 8:8, 12) Ifenso timaona kuti malangizo a m’Baibo amene timalandila pamisonkhano yathu ni ofunika kwambili. Mutu wa pulogalamu iliyonse umacokela m’Malemba. Timaphunzila mmene tingacitile cifunilo ca Mulungu pa umoyo wathu kudzela m’pulogalamu yosangalatsa ya nkhani zimene munthu amakamba yekha, nkhani zosiilana, ndi zitsanzo. Timalimbikitsidwa kumva za anzathu amene akupilila mavuto amene amakumana nao nthawi ino yovuta cifukwa cokhala Akristu. Pamisonkhano yacigao, pamakhala maseŵelo amene amatithandiza kumvetsetsa nkhani za m’Baibo ndi kutiphunzitsa mfundo zothandiza kwambili. Pamsonkhano uliwonse waukulu pamakhala ubatizo wa anthu amene afuna kuonetsa kuti anadzipeleka kwa Mulungu.
-
N’cifukwa ciani misonkhano ikulu-ikulu imakhala nthawi yosangalatsa?
-
Kodi mungapindule m’njila ziti ngati mupezeka pamsonkhano waukulu?