PHUNZILO 1
Kodi Mboni za Yehova Ni Anthu Otani?
Kodi ni Mboni za Yehova zingati zimene mumadziŵa? Ena a ife timakhala pafupi ndi inu, timaseŵenza pamodzi ndi inu, kapena tili m’kalasi imodzi ndi inu. Mwina tinacezapo ndi inu nkhani za m’Baibo. Kodi ndife ndani, nanga n’cifukwa ciani timauzako anthu ena zimene timakhulupilila?
Ndife anthu wamba. Tinakulila kosiyana-siyana ndipo tili ndi zikhalidwe zosiyana-siyana. Kale ena a ife tinali m’zipembedzo zina, ndipo ena sanali kukhulupilila Mulungu. Koma tikalibe kukhala Mboni, ife tonse tinapatula nthawi yofufuza bwino-bwino ziphunzitso za m’Baibo. (Machitidwe 17:11) Tinavomeleza zimene tinaphunzila, ndipo aliyense payekha anasankha kulambila Yehova Mulungu.
Kuphunzila Baibo kumatithandiza. Ife, monga anthu ena onse, timakumana ndi mavuto ndipo timalephela mbali zina. Koma cifukwa cakuti tsiku ndi tsiku timayesa-yesa kutsatila mfundo za m’Baibo paumoyo wathu, umoyo wathu umakhala wabwino kwambili. (Salimo 128:1, 2) Ici ndiye cifukwa cina cimene timauzilako ena zinthu zabwino zimene taphunzila m’Baibo.
Timatsatila mfundo za Mulungu. Mfundo za m’Baibo zimatithandiza kukhala pamtendele ndi kukhala aulemu, ndiponso kukhala ndi makhalidwe monga kuona mtima ndi cifundo. Zimathandiza anthu kukhala ndi umoyo wathanzi ndiponso akhama panchito, ndipo zimalimbikitsa mgwilizano pabanja. Timakhulupilila kuti “Mulungu alibe tsankho.” Conco, ndife banja la padziko lonse la abale auzimu, ndipo pakati pathu palibe tsankho kapena mikangano ya ndale. Ngakhale kuti ndife anthu wamba, gulu lathu ni lapadela.—Machitidwe 4:13; 10:34, 35.
-
Kodi Mboni za Yehova zimafanana bwanji ndi anthu ena?
-
Kodi ni mfundo ziti zimene Mboni zaphunzila m’Baibo?