KUYAMBITSA MAKAMBILANO
PHUNZILO 1
Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
Mfundo Yaikulu: “Cikondi . . . sicisamala zofuna zake zokha.”—1 Akor. 13:4, 5.
Mmene Yesu Anacitila Zimenezi
1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Yohane 4:6-9. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:
Tiphunzilaponji kwa Yesu?
2. Nthawi zambili makambilano athu amayenda bwino ngati tiyamba na nkhani imene imam’khudza munthuyo.
Tengelani Citsanzo ca Yesu
3. Khalani wokonzeka kusintha. Musakhale na maganizo ongofuna kukambilana nkhani imene inuyo mwaikonzekela. Yambani na nkhani imene munthuyo ali nayo m’maganizo lelo. Conco dzifunseni kuti:
-
‘Kodi ni nkhani yanji ili m’kamwa-m’kamwa kwa anthu oyandikana nawo, ku nchito kwathu, kapena ku sukulu?’
4. Khalani oyang’anitsitsa. Dzifunseni kuti:
-
‘Kodi munthuyu namupeza akucita ciyani? Kodi mwina akuganiza ciyani?’
-
‘Kodi zimene wavala, mmene iye akuonekela, kapena pa nyumba pake, zionetsa kuti ni wacipembedzo canji, kapena ni wa mtundu wanji?’
5. Muzimvetsela.
ONANINSO MALEMBA AWA
Mat. 7:12; 1 Akor. 9:20-23; Afil. 2:4; Yak. 1:19