PHUNZILO 6
Kodi Moyo Unayamba Bwanji?
“Pakuti inu [Mulungu] ndinu kasupe wa moyo.” (Salimo 36:9) Kodi muikhulupilila mfundo imeneyi? Anthu ena amakhulupilila kuti moyo unangoyambika wokha mwa zocitika zangozi. Ngati zimenezi n’zoona, ndiye kuti tinangokhalapo mwangozi. Koma ngati moyo unacita kulengedwa na Yehova Mulungu, ndiye kuti uli na colinga, si conco kodi? a Dziŵani za ciyambi ca moyo mmene Baibo imacifotokozela, komanso cifukwa cake mungakhulupilile zimenezo.
1. Kodi kumwamba na dziko lapansi zinakhalako bwanji?
Baibo imakamba kuti: “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Asayansi ambili amavomeleza kuti kumwamba na dziko lapansi zinali na poyambila pake. Kodi Mulungu anazilenga bwanji? Anaseŵenzetsa mzimu woyela umene ni “mphamvu” yake yogwila nchito, kupanga zinthu zonse, monga milalang’amba, nyenyezi, na mapulaneti kuphatikizapo dziko lapansi.—Genesis 1:2.
2. N’cifukwa ciyani Mulungu analenga dziko lapansi?
Yehova “sanalilenge popanda colinga [dziko lapansi], . . . analiumba kuti anthu akhalemo.” (Yesaya 45:18) Iye analenga dziko lapansi kukhala mudzi wokhala anthu, malo abwino okhalapo kwamuyaya. (Ŵelengani Yesaya 40:28; 42:5.) Ngakhale asayansi atsimikizila kuti dziko lapansi n’lapadela kwambili. Ndiyo pulaneti yokha imene anthu angathe kukhalapo.
3. N’ciyani cimapangitsa anthu kukhala osiyana na zinyama?
Yehova atapanga dziko lapansi, analenganso zamoyo n’kuziikapo. Coyamba, analenga zomela na zinyama. Kenako, “Mulungu analenga munthu m’cifanizilo cake.” (Ŵelengani Genesis 1:27.) Koma kodi cimasiyanitsa munthu na nyama n’ciyani kwenikweni? Popeza kuti ife anthu tinapangidwa m’cifanizilo ca Mulungu, timatha kuonetsa makhalidwe ake monga cikondi na cilungamo. Anatilenganso kuti tizitha kuphunzila zinenelo zina, kukhumbila zinthu zokongola, na kusangalala na nyimbo. Ndipo mosiyana na zinyama, timatha kulambila Mlengi wathu.
KUMBANI MOZAMILAPO
Onani umboni woonetsa kuti moyo unacita kulengedwa, ndipo zimene Baibo imakamba za cilengedwe n’zomveka. Dziŵaninso kuti makhalidwe abwino amene anthu ali nawo amatiphunzitsa ciyani za Mulungu.
4. Moyo unacita kulengedwa
Anthu amatamandidwa popanga zinthu mokopela ku zacilengedwe. Nanga ndani ayenela kutamandidwa pa zinthu zacilengedwezo zimene anthu amakopelako? Tambani VIDIYO, na kukambilana funso ili.
-
Kodi anthu apanga zinthu zotani mokopela ku zacilengedwe?
Nyumba iliyonse inamangidwa na munthu. Nanga ndani anapanga zinthu zacilengedwe? Ŵelengani Aheberi 3:4, na kukambilana mafunso aya:
-
Ni zinthu ziti zacilengedwe zimene zimakucititsani cidwi?
-
Kodi tiyenela kukhulupilila kuti kumwamba na dziko lapansi, na zonse zili mmenemo, zinacita kulengedwa? Cifukwa ciyani?
Kodi Mudziŵa?
Nkhani na mavidiyo okhudza zacilengedwe mungayapeze pa jw.org ku chichewa pa mutu wakuti “Kodi Zinangochitika Zokha?” komanso “Zokhudza Mmene Moyo Unayambira”
“N’zoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu”
5. Zimene Baibo imakamba kuti zinthu zinacita kulengedwa n’zomveka
Mu Genesis caputala 1, Baibo imafotokoza mmene dziko lapansi na zamoyo zake zinakhalilako. Kodi mukhulupilila zimene imakambazo, kapena muona kuti ni nthano cabe? Tambani VIDIYO, na kukambilana mafunso aya.
-
Kodi Baibo imaphunzitsa kuti dziko lapansi komanso zamoyo zimene zilipo zinalengedwa m’masiku 6 cabe?
-
Kodi muganiza kuti zimene Baibo imafotokoza kuti zinthu zinacita kulengedwa n’zomveka? Cifukwa ciyani?
Ŵelengani Genesis 1:1, na kukambilana funso ili:
-
Asayansi amakamba kuti kumwamba na dziko lapansi zinali na poyambila pake. Kodi mfundo yawo imeneyi igwilizana bwanji na zimene mwangoŵelenga m’Baibo?
Anthu ena amafunsa ngati Mulungu poyamba analenga kanthu kamoyo kamene kanayamba kusandulika. Ŵelengani Genesis 1:21, 25, 27, na kukambilana funso ili:
-
Kodi Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu analenga kanthu kamoyo kamodzi kamene kanayamba kusandulika n’kukhala nsomba, zinyama, kenako anthu? Kapena kodi “mtundu” uliwonse wa camoyo anacita kuulenga mwa mtundu wake?
6. Mulungu analenga anthu m’njila yapadela kwambili
Yehova anatilenga ife anthu mosiyana na zinyama. Ŵelengani Genesis 1:26, na kukambilana funso ili:
-
Popeza ife anthu timatha kuonetsa cikondi na cifundo, ndipo tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, ndiye kuti naye Mulungu alinso na makhalidwe otani?
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Zimene Baibo imakamba kuti zinthu zinacita kulengedwa na Mulungu ni nthano cabe.”
-
Nanga inu muganiza bwanji? Cifukwa ciyani?
CIDULE CAKE
Yehova analenga kumwamba na dziko lapansi, komanso zamoyo zonse.
Mafunso Obweleza
-
Kodi Baibo imaphunzitsa kuti kumwamba na dziko lapansi zinakhalako bwanji?
-
Kodi Mulungu analenga kanthu kamoyo kamodzi kamene kanasandulika n’kukhala mitundu yosiyana-siyana ya zamoyo, kapena mtundu uliwonse anacita kuulenga?
-
Kodi cimasiyanitsa munthu na nyama n’ciyani?
FUFUZANI
Onani zinthu zacilengedwe zoonetsa kuti kuli Mlengi.
“Kodi Zamoyo Zimatiphunzitsa Ciani?” (Galamuka!, September 2006)
Onani mmene kholo lingafotokozele mwana wake zimene Baibo imakamba za mmene zinthu zonse zinakhalilako.
Onani ngati ciphunzitso ca cisanduliko cimagwilizana na Baibo.
“Kodi Mulungu Anaseŵenzetsa Cisanduliko Polenga Zamoyo Zosiyanasiyana?” (Nkhani ya pawebusaiti)
Onani ngati mafupa opezeka akale-kale, kapena umboni wasayansi, ukuonetsa kuti moyo unacita kulengedwa kapena unangoyambika wokha.
a Phunzilo 25 idzafotokoza colinga ca Mulungu polenga anthu.