Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 15

Kodi Yesu Ndani?

Kodi Yesu Ndani?

Yesu ni mmodzi mwa anthu ochuka kopambana m’mbili ya anthu. Ngakhale n’telo, anthu amangodziŵa dzina lake cabe, sadziŵa zambili za iye. Komanso ambili amamuganizila mosiyana-siyana. Kodi Baibo imakamba ciyani za iye?

1. Kodi Yesu ndani?

Yesu ni munthu wauzimu wamphamvu amene akhala kumwamba. Yehova Mulungu ndiye anamulenga asanalenge cina ciliconse. Pa cifukwa cimeneci, iye amachedwa “woyamba kubadwa wa cilengedwe conse.” (Akolose 1:15) Baibo imachulanso Yesu kuti “mwana wake wobadwa yekha” wa Mulungu, cifukwa ni yekhayo amene analengedwa mwacindunji na Yehova. (Yohane 3:16) Yesu anaseŵenza na Atate wake Yehova mogwilizana kwambili, pomuthandiza kulenga zinthu zonse. (Ŵelengani Miyambo 8:30.) Ndipo mpaka pano, Yesu ali pa ubale wokondana ngako na Yehova. Iye amatumikila mokhulupilika monga wolankhulila Mulungu, kapena kuti “Mawu.” Amapeleka mauthenga na malangizo a Mulungu.—Yohane 1:14.

2. N’cifukwa ciyani Yesu anabwela padziko lapansi?

Zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo, mwa cozizwitsa Yehova anaseŵenzetsa mzimu wake kusamutsa moyo wa Yesu kucoka kumwamba, kuuika m’mimba mwa namwali wacitsikana Mariya. Umu ni mmene Yesu anabadwila monga munthu padziko lapansi. (Ŵelengani Luka 1:34, 35.) Yesu anabwela padziko lapansi kudzakhala Mesiya wolonjezedwayo, kapena kuti Khristu, kuti adzapulumutse mtundu wa anthu. a Maulosi onse a m’Baibo onena za Mesiya anakwanilitsidwa mwa iye. Mwa ici, anthu anamuzindikila Yesu kukhala “Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”Mateyu 16:16.

3. Kodi Yesu ali kuti pali pano?

Yesu atamwalila, pambuyo pake anaukitsidwa monga munthu wauzimu na kubwelela kumwamba. Kumeneko, “Mulungu anamukweza n’kumuika pamalo apamwamba.” (Afilipi 2:9) Conco, Yesu ali na udindo waukulu kwambili. Iye yekhayo ndiye waciŵili kwa Yehova Mulungu.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani zambili pa mfundo yakuti Yesu n’ndani kwenikweni, komanso cifukwa cake kuphunzila za iye n’kofunika.

4. Yesu si Mulungu Wamphamvuzonse

Baibo imaphunzitsa kuti ngakhale kuti Yesu ni munthu wauzimu wamphamvu kumwamba, iye amagonjela kwa Atate wake, Yehova Mulungu. Tikunena zimenezi cifukwa ciyani? Tambani VIDIYO kuti muone zimene Baibo imakamba zokhudza udindo wa Yesu pouyelekezela na udindo wa Mulungu Wamphamvuzonse.

Malemba otsatilawa adzatithandiza kumvetsa ubale umene ulipo pakati pa Yehova na Yesu. Pambuyo poŵelenga lemba lililonse, kambilanani mafunso ali pansi pake.

Ŵelengani Luka 1:30-32.

  • Kodi mngelo anaufotokoza motani ubale uli pakati pa Yesu na Yehova Mulungu “Wam’mwambamwamba”?

Ŵelengani Mateyu 3:16, 17.

  • Pa ubatizo wa Yesu, kodi mawu ocokela kumwamba anati ciyani?

  • Nanga muganiza mawuwo anali a ndani?

Ŵelengani Yohane 14:28.

  • Kodi pakati pa tate na mwana wake, amakhala wamkulu ndani, pa msinkhu na ulamulilo?

  • Pamene Yesu anachula Yehova kuti Atate, kodi zitiuza ciyani?

Ŵelengani Yohane 12:49.

  • Kodi Yesu amaganiza kuti iye na Atate wake ni olingana? Nanga inu muganiza bwanji?

5. Zimene zinatsimikizila kuti Yesu ndiye anali Mesiya

Baibo ili na maulosi ambili amene anathandiza anthu kumuzindikila Mesiya, wosankhidwa na Mulungu kuti adzapulumutse mtundu wa anthu. Tambani VIDIYO kuti mudziŵe maulosi ena amene Yesu anakwanilitsa ali padziko lapansi.

Ŵelengani maulosi a m’Baibo aya, kenako kambilanani mafunso ali pansi pake:

Ŵelengani Mika 5:2 kuti mudziŵe kumene Mesiya anayela kubadwila. b

  • Kodi kubadwa kwa Yesu kunakwanilitsa ulosi umenewu?—Mateyu 2:1.

Ŵelengani Salimo 34:20, komanso Zekariya 12:10, kuti muone zimene zinaloseledwa zokhudza imfa ya Mesiya.

  • Kodi maulosi amenewa anakwanilitsidwa?—Yohane 19:33-37.

  • N’cifukwa ciyani sitinganene kuti maulosi amenewa Yesu anacita kuwapangitsa kuti akwanilitsidwe?

  • Kodi mukuona kuti izi zikutsimikizila ciyani ponena za Yesu?

6. Kuphunzila za Yesu kumatipindulitsa kwambili

Baibo imatsindika kuti kuphunzila za Yesu na udindo wake n’kofunika ngako. Ŵelengani Yohane 14:6, komanso 17:3, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi kuphunzila za Yesu n’kofunika cifukwa ciyani?

Yesu anatsegulila njila yokhalila bwenzi la Mulungu. Anaphunzitsa coonadi ponena za Yehova, ndipo mwa iye tingathe kupeza moyo wosatha

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “A Mboni za Yehova sakhulupilila mwa Yesu.”

  • Kodi inu mungakambepo ciyani?

CIDULE CAKE

Yesu ni munthu wauzimu wamphamvu. Iye ni Mwana wa Mulungu komanso Mesiya.

Mafunso Obweleza

  • N’cifukwa ciyani Yesu amachedwa “woyamba kubadwa wa cilengedwe conse”?

  • Kodi Yesu asanabwele padziko lapansi anali na udindo wanji kumwamba?

  • Timadziŵa bwanji kuti Yesu ndiye Mesiya?

Colinga

FUFUZANI

Pezani ngati Baibo imaphunzitsa kuti Mulungu anacita kum’bala Yesu mmene anthu amabalila ana.

“N’cifukwa Ciyani Yesu Amachedwa Mwana wa Mulungu?” (Nkhani ya pawebusaiti)

Onani cifukwa cake Utatu wa Mulungu si ciphunzitso ca m’Baibo.

“Kodi Yesu Ni Mulungu?” (Nsanja ya Mlonda, April 1, 2009)

Ŵelengani za mmene mzimayi wina anasinthila moyo wake atafufuza zimene Baibo imakamba pa Yesu.

“Mzimayi Waciyuda Anafufuzanso Mozama Cikhulupililo Cake” (Galamuka! May 2013)

a Maphunzilo 26 na 27 adzaonetsa cifukwa cake mtundu wa anthu ufunikila kupulumutsidwa, komanso mmene Yesu adzatipulumutsila.

b Onani Mfundo Yakumapeto 2 kuti mudziŵe ulosi umene unanenelatu kuti Mesiya adzaonekela liti kwenikweni padziko lapansi.