Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 20

Dongosolo la Mpingo

Dongosolo la Mpingo

Yehova ni Mulungu wa dongosolo. (1 Akorinto 14:33) Ngati n’telo, nawonso anthu ake akuyembekezeka kukhala olinganizidwa mwadongosolo. Conco, kodi mpingo wacikhristu ni wokonzedwa motani? Ndipo tingathandizile motani pa dongosolo limenelo?

1. Kodi mutu wa mpingo ndani?

“Khristu [ndiye] mutu wa mpingo.” (Aefeso 5:23) Kucokela kumwamba kumene ali, iye amayang’anila nchito ya anthu a Yehova padziko lonse. Yesu anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” amene ni kagulu kocepa ka akulu okhwima kuuzimu, kochedwanso Bungwe Lolamulila. (Ŵelengani Mateyu 24:45-47.) Monga mmene atumwi komanso akulu ku Yerusalemu anali kucitila m’zaka za zana loyamba, Bungwe Lolamulila nalonso limapeleka citsogozo ku mipingo yonse padziko. (Machitidwe 15:2) Koma amuna amenewa sindiwo atsogoleli a gulu lathu. Iwonso amadalila citsogozo ca Yehova na Mawu ake, komanso amagonjela umutu wa Yesu.

2. Kodi akulu ali na udindo wanji mu mpingo?

Akulu ni amuna okwima kuuzimu. Iwo amaphunzitsa nkhosa za Yehova kucokela m’Malemba, ndipo amawathandiza na kuwalimbikitsa. Iwo salandila malipilo pa nchito yawo. Amangotumikila modzipeleka komanso “mofunitsitsa. Osatinso cifukwa cofuna kupindulapo kenakake” iyayi. (1 Petulo 5:1, 2) Akuluwo amathandizidwa na atumiki othandiza, amene m’kupita kwa nthawi, nawonso angayenelele kutumikila monga akulu.

Bungwe Lolamulila limasankha akulu ena kukhala oyang’anila madela. Iwo amayendela mipingo yosiyana-siyana kuti apeleke citsogozo na cilimbikitso. Ndipo iwo amaika akulu na atumiki othandiza amene amakwanilitsa ziyenelezo za m’Malemba.—1 Timoteyo 3:1-10, 12; Tito 1:5-9.

3. Kodi Mboni ya Yehova iliyonse ili na udindo wanji?

Onse mu mpingo ayenela ‘kutamanda dzina la Yehova.’ (Ŵelengani Salimo 148:12, 13.) Izi ziphatikizapo kupeleka ndemanga pa misonkhano ya mpingo, kukamba nkhani, kuonetsa zitsanzo, kuimba nawo nyimbo, komanso kutengako mbali m’nchito yolalikila malinga na mmene zinthu zilili pa umoyo wawo.

KUMBANI MOZAMILAPO

Dziŵani kuti Yesu ni mtsogoleli wotani, mmene akulu amatengela citsanzo cake, komanso mmene ifenso tingakhalile ogonjela kwa Yesu komanso kwa akulu.

4. Yesu ni mtsogoleli wokoma mtima

Yesu akutiitana motikomela mtima. Ŵelengani Mateyu 11:28-30, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi Yesu ni mtsogoleli wotani? Ndipo amafuna tiziumva bwanji utsogoleli wake?

Kodi akulu amatengela bwanji citsanzo ca Yesu? Tambani VIDIYO.

Baibo imaphunzitsa bwino mmene akulu ayenela kugwilila nchito yawo.

Ŵelengani Yesaya 32:2, komanso 1 Petulo 5:1-3, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi mumamva bwanji podziŵa kuti akulu amatengela citsanzo ca Yesu potsitsimula ena?

  • Kodi akulu amatengela citsanzo ca Yesu m’mbali zinanso ziti?

5. Akulu amaphunzitsa mwa citsanzo cawo

Kodi Yesu amafuna kuti akulu aziuona motani udindo wawo? Tambani VIDIYO.

Yesu anapeleka malangizo amene akulu mu mpingo ayenela kuwatsatila. Ŵelengani Mateyu 23:8-12, na kukambilana funso ili:

  • Kodi mumaona kusiyana kotani, pakati pa malangizo a m’Baibo kwa akulu, na mmene azibusa komanso atsogoleli ena a zipembedzo amacitila zinthu?

  1. Akulu na mabanja awo amayesetsa kukhalabe olimba kuuzimu

  2. Akulu amasamalila onse mu mpingo

  3. Akulu amalalikila nthawi zonse

  4. Akulu ni aphunzitsi. Amathandizilanso pa kuyeletsa na nchito zina

6. Tiyenela kuwamvela akulu

Baibo imatipatsa cifukwa cofunika cokhalila omvela kwa akulu. Ŵelengani Aheberi 13:17, na kukambilana mafunso aya:

  • Kodi kulidi kwaphindu pamene Baibo ikutilimbikitsa kumvela akulu na kuwagonjela? Nʼcifukwa ciyani mwayankha conco?

Ŵelengani Luka 16:10, na kukambilana funso ili:

  • N’cifukwa ciyani kumvela akulu n’kofunika ngakhale pa zinthu zooneka zazing’ono?

ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Sucita kufunikila kuloŵa mpingo.”

  • Kodi muganiza pali mapindu otani munthu akamalambila Mulungu pamodzi na anzake mu mpingo?

CIDULE CAKE

Yesu ndiye mutu wa mpingo. Timakondwela kukhala omvela kwa akulu amene akutumikila pansi pake. Mwa citsanzo cawo cabwino, akulu amatiphunzitsa na kutilimbikitsa.

Mafunso Obweleza

  • Kodi mutu wa mpingo ndani?

  • Kodi akulu amauthandiza bwanji mpingo?

  • Kodi aliyense wolambila Yehova ali na udindo wotani?

Colinga

FUFUZANI

Onani umboni wa mmene Bungwe Lolamulila, komanso akulu, amasamalila kwambili za Akhristu lelo lino.

Kulimbikitsa Abale pa Nthawi ya Ciletso (4:22)

Dziŵani nchito imene oyang’anila madela amacita.

Moyo wa Woyang’anira Dera Amene Amatumikira Madera a ku Midzi (4:51)

Dziŵani mmene akulu amacitila khama kulimbikitsa alambili anzawo.

“Akulu Acikhristu ni Anchito Anzathu Otipatsa Cimwemwe” (Nsanja ya Mlonda, January 15, 2013)