Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mfundo za Kumapeto

Mfundo za Kumapeto
  1.  Kumuzindikila Babulo Wamkulu

  2.  Kodi Mesiya Anali Kudzaonekela Liti?

  3.  Njila Zothandizila Odwala Zofuna Magazi

  4.  Kusalana a pa Ukwati

  5.  Maholide na Zikondwelelo Zina

  6.  Matenda Oyambukila

  7.  Nkhani za Bizinesi Komanso Zokhudza Malamulo

 1. Kumuzindikila Babulo Wamkulu

Kodi timadziŵa bwanji kuti “Babulo Wamkulu” amaimilako zipembedzo zonse zonyenga? (Chivumbulutso 17:5) Ganizilani mfundo izi:

  • Ali kulikonse padziko lapansi. Baibo imanena kuti Babulo Wamkulu anakhala pa ‘makamu na maiko.’ Imakambanso kuti iye ‘akulamulila mafumu a dziko lapansi.’—Chivumbulutso 17:15, 18.

  • Si wandale komanso si wamalonda. Pamene iye adzawonongedwa, “mafumu a dziko lapansi” komanso “amalonda” adzapulumuka.—Chivumbulutso 18:9, 15.

  • Amaimilako Mulungu monama. Iye amachedwa mkazi wacigololo cifukwa amagwilizana na maboma, pofuna ndalama komanso mapindu ena. (Chivumbulutso 17:1, 2) Mkazi ameneyu amasoceletsa mitundu yonse ya anthu. Ndipo wacititsa imfa za anthu ambili-mbili.—Chivumbulutso 18:23, 24.

Bwelelani ku phunzilo 13 mfundo 6

 2. Kodi Mesiya Anali Kudzaonekela Liti?

Baibo inakambilatu kuti Mesiya adzafika patapita milungu 69. Ŵelengani Danieli 9:25.

  • Kodi milungu 69 imeneyo inayamba liti? Inayamba m’caka ca 455 B.C.E. Ndico caka cimene Bwanamkubwa Nehemiya anafika ku Yerusalemu kuti mzindawo ‘ukonzedwe ndi kumangidwanso.’—Danieli 9:25; Nehemiya 2:1, 5-8.

  • Kodi milungu 69 imeneyo inatenga utali wotani? M’maulosi ena a m’Baibo, tsiku limaimila caka cimodzi. (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Conco, mlungu umodzi, umaimila zaka 7. Mu ulosi umenewu, kuwonkhetsa milungu 69 kutipatsa zaka 483 (milungu 69 x masiku 7).

  • Kodi milungu 69 imeneyo inatha liti? Kuŵelengela zaka 483 kucokela mu 455 B.C.E. kumatifikitsa m’caka ca 29 C.E. a Ndico caka cimene Yesu anabatizika na kukhala Mesiya.—Luka 3:1, 2, 21, 22.

Bwelelani ku phunzilo 15 mfundo 5

 3. Njila Zothandizila Odwala Zofuna Magazi

Pali macilitso ena akucipatala ogwilitsa nchito magazi a munthu mwini. Ena mwa amenewo—monga kupeleka magazi ako, kapena magazi ako kuwasungilatu padela kuti akawagwilitse nchito pa opaleshoni—ni osaloleka kwa Akhristu.—Deuteronomo 15:23.

Komabe alipo macilitso ena akucipatala amene alibe vuto kwa Akhristu. Amenewa akupatikizapo kupimitsa magazi, kuyeletsa magazi (hemodialysis), kusungunula magazi (hemodilution), kapena kuseŵenzetsa makina obwezelanso magazi m’thupi, kapena makina ena ogwila nchito ya mtima na mapapu popanga opaleshoni. Mkhristu aliyense ayenela kupanga cisankho ca iye mwini za mmene magazi ake angagwilitsidwile nchito pomupanga opaleshoni, pomupima magazi, kapena pa njila yocilitsila iliyonse imene dokotala afuna kusewenzetsa. Dokotala aliyense angakhale na njila yocilitsila yosiyanako pang’ono. Conco, Mkhristu aliyense asanavomeleze kupimidwa kapena njila iliyonse yocilitsila, ayenela kudziŵa bwino lomwe mmene magazi ake agwilitsidwile nchito. Ganizilani mafunso aya:

  • Bwanji ngati magazi anga adzapatutsidwa kutuluka m’thupi mwanga, ndipo kuyenda kwake kudzadukizidwa kwa kanthawi? Malinga na cikumbumtima canga, kodi niona kuti magazi amenewa ni mbali ya thupi langa, yosayenela kuthilidwa “pansi”?—Deuteronomo 12:23, 24.

  • Bwanji ngati pa cithandizo ca cipatala akufuna kuti atulutse ena a magazi anga m’thupi, kuwasinthako, kenako n’kuwabwezanso m’thupi mwanga? Kodi zimenezi zingavutitse cikumbumtima canga cophunzitsidwa Baibo, kapena zingakhale zololeka kwa ine?

Bwelelani ku phunzilo 39 mfundo 3

 4. Kusalana a pa Ukwati

Mawu a Mulungu salimbikitsa kuti anthu okwatilana azisalana pa ukwati wawo. Ndipo imakamba mosapita m’mbali kuti kusalana pa ukwati sikupatsa munthu ufulu wokwatilanso. (1 Akorinto 7:10, 11) Komabe, zilipo zocika zina zimene zapangitsa Akhristu ena kusalana pa ukwati wawo.

  • Kusapeleka cisamalilo mwadala: Mwamuna akukana kusamalila zosoŵa zakuthupi za banja lake, moti banja lake likuvutika kwambili.—1 Timoteyo 5:8.

  • Nkhanza zomenya: Nkhanza zomenya zingaike pa ciopsezo thanzi la mnzake wa mu ukwati, ngakhale moyo wake weniweniwo.—Agalatiya 5:19-21.

  • Kuika pa ciopsezo ubale wa pakati pa mnzakeyo na Yehova: Mnzake wa mu ukwati akumulepheletsa kothelatu kutumikila Yehova.—Machitidwe 5:29.

Bwelelani ku phunzilo 42 mfundo 3

 5. Maholide na Zikondwelelo Zina

Akhristu satengako mbali m’maholide amene Yehova sakondwela nawo. Koma Mkhristu aliyense mwa cikumbumtima cake cophuzitsidwa Baibo, ayenela kuona mmene angacitile na mkhalidwe uliwonse wokhudza holide. Onani zitsanzo zocepa izi.

  • Bwanji ngati munthu wina wakuuzani mawu okufunilani holide yabwino? Mungangoyankha kuti, “zikomo.” Ngati munthuyo afuna kudziŵa zambili, mungamufotokozele cifukwa cake simukondwelela holide imeneyo.

  • Bwanji ngati mnzanu wa mu ukwati amene si Mboni ya Yehova, wakuitanilani ku cakudya pamodzi na acibale ake ku cikondwelelo ca holide? Ngati cikumbumtima canu cikulolani kupita, mufotokozeleni mnzanuyo pasadakhale kuti ngati kudzacitika miyambo yacikunja ku cakudya kumeneko, inuyo simudzatengako mbali.

  • Bwanji ngati bwana wanu wa kunchito wakupatsani ciwongoladzanja pa nyengo ya holide? Kodi muyenela kukana? Osati kwenikweni. Kodi bwanayo amaona ciwongoladzanja cimeneco monga njila yokondwelela holideyo, kapena colinga cacikulu ni kukuyamikilani cifukwa ca magwilidwe anu a nchito?

  • Bwanji ngati munthu wina wakupatsani mphatso pa nyengo ya holide? Wokupatsani mphatsoyo anganene kuti: “Nidziŵa kuti inuyo simukondwelelako holide imeneyi, koma nangokupatsani monga mphatso cabe.” Mwina munthuyo wangocita mokoma mtima basi. Kumbali ina, kodi akuoneka kuti akuyesa cikhulupililo canu, kapena akufuna kukupangitsani kukondwelela nawo holide imeneyo? Mukaiganizila mbali imeneyi zili kwa inu kusankha kuilandila mphatsoyo kapena ayi. Koma pa cisankho ciliconse cimene tingapange, timafuna kukhalabe na cikumbumtima coyela komanso kukhulupilikabe kwa Yehova.—Machitidwe 23:1

Bwelelani ku phunzilo 44 mfundo 1

 6. Matenda Oyambukila

Cifukwa anthu anzathu timawakonda, timasamala kwambili kuti tisayambukize ena matenda. Timacita izi pamene tikudwala matenda oyambukila, kapena pamene tikuona kuti tingakhale nawo matenda otelo. Timatelo cifukwa Baibo imalamula kuti, “uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.”—Aroma 13:8-10.

Kodi kumvela lamulo limeneli kumatanthauza ciyani maka-maka? Munthu wodwala matenda oyambukila, sayenela kuonetsa cikondi kwa ena mwa kuwakumbatila kapena kuwapsompsona. Ndipo iye sayenela kukhumudwa ngati ena sakumuitanila kumanyumba kwawo cifukwa cofuna kuteteza mabanja awo. Ndipo ngati akukonzekela zokabatizika, ayenela kudziŵitsa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu pasadakhale za matenda ake. Akuluwo adzapanga makonzedwe apadela kuti ateteze enanso amene akukabatizika. Munthu amene anakhalako pa ciwopsezo cotenga matenda opatsilana, ayenela kukapimitsa magazi mwa kufuna kwake asanayambe cibwenzi na munthu wina. Mukacita zimenezi, mumaonetsa kuti ‘simuganizila zofuna zanu zokha, koma mumaganizilanso zofuna za ena.’—Afilipi 2:4.

Bwelelani ku phunzilo 56 mfundo 2

 7. Nkhani za Bizinesi Komanso Zokhudza Malamulo

Kulembelana mapangano okhudza ndalama kumapewetsa mavuto ambili, ngakhale pamene tikucita pangano na Mkhristu mnzathu. (Yeremiya 32:9-12) Ngakhale n’conco, nthawi zina Akhristu angasemphanebe maganizo pa nkhani zing’ono-zing’ono, monga zokhudza ndalama kapena pa nkhani zina. Zikatelo, iwo ayenela kukambilana na kuzithetsa nkhanizo mwamsanga, mwamtendele, komanso mseli.

Koma bwanji ngati ni nkhani zikulu-zikulu, monga kuba mwacinyengo kapena misece? (Ŵelengani Mateyu 18:15-17.) Yesu anatilangiza kutenga masitepe atatu aya:

  1. Yesani kuithetsa nkhaniyo pa uŵili wanu.—Onani vesi 15.

  2. Ngati sitepe yoyamba siikuthandiza, pemphani munthu wofikapo kuuzimu, mmodzi kapena aŵili mu mpingo wanu, kuti akakupelekezeni.—Onani vesi 16.

  3. Ngati zikuvutabe kuithetsa nkhaniyo, m’pamene lomba mungakaitule kwa akulu.—Onani vesi 17.

Nthawi zambili, m’posafunika kutengela abale athu kukhoti, cifukwa zimapeleka cithunzi coipa ca Yehova na mpingo wake. (1 Akorinto 6:1-8) Ngakhale n’telo, zilipo nkhani zina zimene ziyenela kuthetsedwa mwa malamulo ndithu, monga izi: kuthetsa ukwati, amene ayenela kusunga ana, malipilo a cipukutamisozi kwa wosiyidwa ukwati, malipilo a inshuwalansi, kulephela kubweza nkhongole bizinesi ikangwa, kapena nkhani zokhudza ma wilu. Mkhristu akapeleka nkhani zotelezi kukhoti, n’colinga cakuti zithe mwa mtendele, si kuti akunyozela uphungu wa m’Baibo ayi.

Komanso, ngati pacitika mlandu waukulu wa upandu—monga kugona munthu mwacikakamizo, kugwilila mwana, kuvulaza munthu, kuba kwakukulu, kapena kupha munthu—Mkhristu akacitila lipoti nkhani zimenezi ku boma, sindiye kuti wanyozela uphungu wa m’Baibo ayi.

Bwelelani ku phunzilo 56 mfundo 3

a Kucokela mu 455 B.C.E. kudzafika mu 1 B.C.E. pali zaka 454. Kucokela mu 1 B.C.E. kufika mu 1 C.E. pali caka cimodzi (palibe caka ca zilo). Kucokela mu 1 C.E. kudzafika mu 29 C.E. pali zaka 28. Conco, tikawonkhetsa 454 + 1 + 28 itipatsa zaka 483.

Kuti mumve zambili pa njila zocilitsila zimenezi, onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga,” mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 2000, ya Chichewa.