Muzilimbikitsidwa ndi Mphatso ya Mulungu Yosatheka Kuifotokoza
“Tikuyamika Mulungu cifukwa ca mphatso yake yaulele, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.”—2 AKORINTO 9:15.
1, 2. (a) Kodi mphatso ya Mulungu ‘imene sitingathe kuifotokoza’ imaphatikizapo ciani? (b) Tikambilana mafunso ati m’nkhani ino?
YEHOVA anatipatsa mphatso yamtengo wapatali pamene anatumiza Mwana wake wokondedwa, Yesu, kuti abwele padziko lapansi. (Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9, 10) Mtumwi Paulo anakamba kuti imeneyi ndi “mphatso . . . yaulele, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akorinto 9:15) N’cifukwa ciani Paulo ananena mau amenewa?
2 Paulo anadziŵa kuti nsembe ya Yesu ndi citsimikizo cakuti Mulungu adzakwanilitsa malonjezo ake onse. (Ŵelengani 2 Akorinto 1:20.) Izi zitanthauza kuti “mphatso [ya Mulungu] yaulele imene sitingathe n’komwe kuifotokoza” imaphatikizapo nsembe ya Yesu, zinthu zonse zabwino zimene Yehova amaticitila, ndiponso kukoma mtima kwake. Mphatso imeneyi ndi yamtengo wapatali kwambili cakuti sitingathe kuifotokoza mokwanila. Kodi tiyenela kumva bwanji tikaganizila mphatso yamtengo wapatali imeneyi? Nanga iyenela kutilimbikitsa kucita ciani pamene tikukonzekela Cikumbutso ca imfa ya Kristu cimene cidzacitika pa Citatu, pa March 23, 2016?
MPHATSO YAPADELA YOCOKELA KWA MULUNGU
3, 4. (a) Mumamva bwanji munthu wina akakupatsani mphatso? (b) Kodi mphatso yapadela ingasinthe bwanji umoyo wanu?
3 Timasangalala munthu akatipatsa mphatso. Mphatso zina zimakhala zapadela kwambili moti zimaticititsa kusintha umoyo wathu. Mwacitsanzo, yelekezelani kuti mwacita colakwa cinacake cacikulu, ndipo cilango cake ndi kuphedwa. Koma mosayembekezeleka, munthu wina amene simum’dziŵa wadzipeleka kuti aphedwe m’malo mwa inu. Kodi mungamve bwanji ngati mwalandila mphatso yotelo?
4 Mphatso yapadela imeneyo ingakuthandizeni kusintha zinthu pa umoyo wanu. Mosakaikila, mudzalimbikitsidwanso kukhala woolowa manja kwambili, wacikondi, ndi wokonzeka kukhululukila ena. Pa umoyo wanu wonse, mudzayesetsa kusonyeza kuti mumayamikila mphatso imene munalandila.
5. Kodi mphatso ya dipo imaposa bwanji mphatso zina zonse?
5 Mphatso ya Mulungu ya dipo ndi yapamwamba kwambili kuposa mphatso imene tafotokoza m’citsanzo cili pamwambapa. (1 Petulo 3:18) Ganizilani izi: Tonse tinalandila ucimo kucokela kwa Adamu, ndipo cilango ca ucimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Cikondi cinasonkhezela Yehova kutumiza Yesu padziko lapansi kuti “alawe imfa m’malo mwa munthu aliyense.” (Aheberi 2:9) Koma nsembe ya Yesu idzabweletsa madalitso ena ambili. Cifukwa ca nsembeyi, imfa idzaonongedwa kwamuyaya. (Yesaya 25:7, 8; 1 Akorinto 15:22, 26) Anthu onse amene amakhulupilila Yesu adzakhala mwamtendele kwamuyaya. Ena adzasangalala kukhala mafumu ndi Kristu kumwamba, ndipo ena adzakhala padziko lapansi monga nzika za Ufumu wa Mulungu. (Aroma 6:23; Chivumbulutso 5:9, 10) Ndi madalitso ena ati amene tidzalandila cifukwa ca mphatso imene Yehova anatipatsa?
6. (a) Ndi madalitso ati amene tidzalandila cifukwa ca mphatso imene Yehova anapeleka? (b) Chulani zinthu zitatu zimene cikondi ca Mulungu cimatilimbikitsa kucita.
6 Cifukwa ca mphatso ya Mulungu ya dipo, dziko lapansi lidzakhala paladaiso, matenda adzatha, ndipo akufa adzaukitsidwa. (Yesaya 33:24; 35:5, 6; Yohane 5:28, 29) Timakonda Yehova ndi Mwana wake wokondedwa cifukwa cotipatsa “mphatso . . . yaulele imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” Kodi mphatso imeneyi imatilimbikitsa kucita ciani? Imatilimbikitsa (1) kutengela citsanzo ca Yesu mosamala kwambili, (2) kukonda abale athu ndiponso (3) kukhululukila ena mocokela pansi pa mtima.
“CIKONDI CIMENE KRISTU ALI NACO CIMATIKAKAMIZA”
7, 8. Kodi tiyenela kumva bwanji tikaganizila cikondi cimene Kristu anatisonyeza? Nanga cikondi cimeneci ciyenela kutilimbikitsa kucita ciani?
7 Coyamba, cikondi ca Kristu ciyenela kutilimbikitsa kulemekeza Yesu pa umoyo wathu. Mtumwi Paulo anati: “Cikondi cimene Kristu ali naco cimatikakamiza.” (Ŵelengani 2 Akorinto 5:14, 15.) Paulo anali kudziŵa kuti ngati timayamikila cikondi cacikulu ca Yesu, tidzalimbikitsidwa kum’konda ndi kum’lemekeza. Kukamba zoona, tikamvetsetsa zimene Yehova anaticitila, cikondi cake cidzatilimbikitsa kukhala ndi umoyo woonetsa kuti timalemekeza Yesu. Tingacite bwanji zimenezi?
8 Kukonda Yehova kudzatilimbikitsa kutengela citsanzo ca Yesu kapena kuti kutsatila mapazi ake mosamala kwambili. (1 Petulo 2:21; 1 Yohane 2:6) Timaonetsa kuti timakonda Mulungu ndi Kristu mwa kukhala womvela. Yesu anati: “Amene ali ndi malamulo anga ndipo amawasunga, ameneyo ndiye amene amandikonda. Komanso wondikonda ine, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsela bwinobwino kwa iye.”—Yohane 14:21; 1 Yohane 5:3.
9. Kodi tingayesedwe kuti tiyambe kucita ciani?
9 Pa nyengo ino ya Cikumbutso, tiyenela kusinkhasinkha zimene tikucita pa umoyo wathu. Conco, dzifunseni kuti: ‘Ndi zinthu ziti zimene ndimacita zoonetsa kuti ndikutengela citsanzo ca Yesu? Nanga ndingaongolele pa mbali ziti?’ Ndi bwino kudzifunsa mafunso amenewa cifukwa cakuti anthu m’dzikoli amafuna kuti tizitengela zocita zao. (Aroma 12:2) Ngati sitisamala, tingayesedwe kuti tiyambe kutengela aphunzitsi a kudziko, anthu ochuka, ndi ngwazi za maseŵela. (Akolose 2:8; 1 Yohane 2:15-17) Kodi tingapewe bwanji zimenezi?
10. Pa nyengo ino ya Cikumbutso, ndi mafunso ati amene tiyenela kudzifunsa? Nanga mayankho ake angatilimbikitse kucita ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)
10 Pa nyengo ino ya Cikumbutso, ndi bwino kuganizila mtundu wa zovala zimene timavala, nyimbo zimene timamvetsela, ndi mafilimu amene timaonelela. Tiyenelanso kuganizila zinthu zimene zili m’kompyuta, m’foni, kapena m’tabuleti yathu. Dzifunseni kuti: ‘Ngati Yesu wabwela ndipo waona zovala zimene ndimavala, kodi ndingacite manyazi?’ (Ŵelengani 1 Timoteyo 2:9, 10.) ‘Kodi zovala zanga zimaonetsa kuti ndine wotsatila wa Kristu? Kodi Yesu angaonelele mafilimu amene ndimakonda? Kodi angamvetsele nyimbo zimene ndimakonda? Ngati Yesu wabweleka foni kapena tabuleti yanga, kodi ndingacite manyazi kuti mwina aonamo zinthu zosayenela? Kodi ndingathe kum’fotokozela cifukwa cake ndimakonda masewela ena ake a pakompyuta?’ Kukonda Yehova kuyenela kutilimbikitsa kutaya kapena kucotsa zinthu zonse zosayenela kwa Mkristu, ngakhale zitakhala zodula. (Machitidwe 19:19, 20) Pamene tinadzipeleka kwa Yehova, tinalonjeza kuti tidzayamba kucita zinthu zolemekeza Kristu pa moyo wathu. Conco, sitiyenela kukhala ndi cinthu ciliconse cimene cingatilepheletse kutengela citsanzo ca Yesu.—Mateyu 5:29, 30; Afilipi 4:8.
11. (a) Kodi kukonda Yehova ndi Yesu kumatilimbikitsa kucita ciani pa nchito yathu yolalikila? (b) Kodi kukonda Mulungu kudzatilimbikitsa kucitila ciani abale athu mumpingo?
11 Kukonda Yesu kumatilimbikitsa kulalikila ndi kuphunzitsa anthu mwakhama. (Mateyu 28:19, 20; Luka 4:43) Pa nyengo ino ya Cikumbutso, kodi mungakonze zakuti muciteko upainiya wothandiza wa maola 30 kapena 50? M’bale wina wa zaka 84 amene mkazi wake anamwalila, anali kuona kuti sangathe kucita upainiya cifukwa ca ukalamba ndi mmene thanzi lake linalili. Koma apainiya a m’dela lake anamuthandiza. Iwo anamupezela thilansipoti ndiponso anamusankhila gawo limene angathe kulalikila mosavuta. Zotsatilapo zake zinali zakuti m’baleyo anakwanilitsa colinga cake cocita upainiya wa maola 30. Kodi mungathandize m’bale kapena mlongo winawake mumpingo wanu kucita upainiya wothandiza mwezi wa March kapena wa April? N’zoona kuti si tonse amene tingaciteko upainiya, koma tikhoza kuonjezela nthawi imene timathela mu utumiki wa Yehova. Tikatelo, tidzasonyeza kuti cikondi ca Yesu n’cimene cimatilimbikitsa kucita zimenezi monga mmene cinacitila kwa Paulo. Kodi cikondi ca Mulungu cidzatilimbikitsanso kucita ciani?
TIYENELA KUKONDANA
12. Kodi cikondi ca Mulungu ciyenela kutilimbikitsa kucita ciani?
12 Caciŵili, cikondi ca Mulungu ciyenela kutilimbikitsa kukonda abale athu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Okondedwa, ngati Mulungu anatikonda conci, ndiye kuti 1 Yohane 4:7-11) Cotelo, ngati timayamikila cikondi ca Mulungu, tiyenela kukonda abale athu. (1 Yohane 3:16) Kodi tingaonetse bwanji kuti timakonda abale athu?
ifenso tiyenela kukondana.” (13. Kodi Yesu anapeleka citsanzo cotani pa nkhani yokonda anthu ena?
13 Yesu anapeleka citsanzo ca mmene tingaonetsele cikondi kwa ena. Ali padziko lapansi, anali kuthandiza anthu makamaka odzicepetsa. Anacilitsa odwala, olemala, osaona, ogontha ndi osalankhula. (Mateyu 11:4, 5) Mosiyana ndi atsogoleli a zipembedzo, Yesu anali kuphunzitsa anthu amene anali kufuna kudziŵa za Mulungu. (Yohane 7:49) Iye anali kukonda anthu odzicepetsa amenewo, ndipo anali kuwathandiza mmene angathele.—Mateyu 20:28.
14. Tingaonetse bwanji kuti timakonda abale athu?
14 Nyengo ya Cikumbutso ndi nthawi yabwino yoganizila mmene tingathandizile abale ndi alongo mumpingo wathu, makamaka okalamba. Mungawacezeleko abale okondedwa amenewa. Kapena mungawapatseko zakudya, kuwathandiza nchito za panyumba, ndi kuwanyamula pa galimoto popita kumisonkhano. Kapenanso mungawapemphe kuti muyende nao mu utumiki wa kumunda. (Ŵelengani Luka 14:12-14.) Ndithudi, cikondi ca Mulungu ciyenela kutilimbikitsa kukonda abale athu.
TIZICITILA CIFUNDO ABALE NDI ALONGO ATHU
15. Kodi tiyenela kukumbukila mfundo iti?
15 Cacitatu, cikondi ca Yehova cimatilimbikitsa kukhululukila abale ndi alongo athu. Tonse tinalandila ucimo kucokela kwa Adamu. Conco, palibe aliyense wa ife amene angakambe kuti, “Dipo ndilibe nalo nchito.” Ngakhale atumiki okhulupilika kwambili a Mulungu amafunikila dipo. Aliyense wa ife anakhululukidwa nkhongole yaikulu ya ucimo. N’cifukwa ciani kukumbukila mfundo imeneyi n’kofunika? Yankho likupezeka m’fanizo limene Yesu anakamba.
16, 17. (a) Tingaphunzile ciani pa fanizo la Yesu la mfumu ndi akapolo? (b) Pambuyo poganizila fanizo la Yesu, kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani?
16 Yesu anakamba fanizo la mfumu imene inakhululukila kapolo amene anakongola ndalama zambili zokwana madinari 60 miliyoni. Koma pambuyo pake, kapoloyo sanakhululukile kapolo mnzake amene iye anam’kongoza ndalama zocepa zokwana madinari 100. Kapoloyo anayenela kukhululukila kapolo mnzake cifukwa cakuti mfumu inamucitila cifundo. Mfumuyo inakwiya kwambili itamva kuti kapolo wake sanakhululukile kapolo mnzake nkhongole yaing’ono imene anam’kongoza. Iyo inati: “Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukila ngongole yonse ija utandidandaulila. Kodi nawenso sukanam’citila cifundo kapolo mnzako, monga momwe ine ndinakucitila cifundo?” (Mateyu 18:23-35) Monga mfumu imeneyi, Yehova watikhululukila nkhongole yaikulu. Kodi cikondi ndi cifundo cimene Yehova watisonyeza ciyenela kutilimbikitsa kucita ciani?
17 Pamene tikonzekela Cikumbutso, tingadzifunse kuti: ‘Kodi pali m’bale amene anandikhumudwitsa? Kodi ndimalephela kumukhululukila? Ngati zili conco, ino ndiyo nthawi yotengela citsanzo ca Yehova amene ndi “wokonzeka kukhululuka.” (Nehemiya 9:17; Salimo 86:5) Ngati timayamikila cifundo ca Yehova, nafenso tidzacitila cifundo anthu ena mwa kuwakhululukila mocokela pansi pamtima. Koma ngati sitikonda ndi kukhululukila abale athu, Yehova nayenso sangatikonde ndi kutikhululukila. (Mateyu 6:14, 15) Kukhululukila anthu ena, sikutanthauza kuti zimene anacita zinali zabwino, koma kumatithandiza kuti tikhale ndi umoyo wosangalala.
18. Kodi cikondi ca Mulungu cinalimbikitsa mlongo wina kucita ciani?
18 Nthawi zina, pamafunika khama kuti tizinyalanyaza zofooka za abale ndi alongo athu. (Ŵelengani Aefeso 4:32; Akolose 3:13, 14.) Mlongo wina dzina lake Lily anayesetsa kucita zimenezi. [1] (Onani mau akumapeto.) Mlongoyu anali kuthandiza mlongo wina wamasiye dzina lake Carol. Mwacitsanzo, iye anali kunyamula Carol pa galimoto ndi kum’pelekeza kumene wafuna. Anali kumuthandizanso kugula zinthu ndi kumucitila zinthu zina zambili. Koma Carol anali wovuta ndipo sanali kuyamikila ngakhale kuti Lily anali kumucitila zinthu zambili zabwino. Nthawi zina, cinali covuta kuti Lily amuthandize. Komabe, Lily anali kuganizila makhalidwe abwino amene Carol anali nao, moti anamuthandiza kwa zaka zambili mpaka pamene Carol anadwala ndi kumwalila. Ngakhale kuti zinali zovuta kuti Lily athandize Carol, Lily anati: “Ndikuyembekezela mwacidwi kudzaona Carol ataukitsidwa. Ndifuna kuti ndikam’dziwe bwino ali wangwilo.” Mwacionekele, cikondi ca Mulungu cingatilimbikitse kukhululukila abale ndi alongo athu ndi kuyembekezela nthawi pamene tonse tidzakhala angwilo kwamuyaya.
19. Kodi mphatso yaulele ya Mulungu ‘imene sitingathe kuifotokoza’ imakulimbikitsani kucita ciani?
19 Kukamba zoona, mphatso yaulele imene Yehova watipatsa “sitingathe n’komwe kuifotokoza.” Nthawi zonse, tiyeni tizisonyeza kuti timayamikila mphatso imeneyi. Nyengo ya Cikumbutso ndi nthawi yabwino yosinkhasinkha zimene Yehova ndi Yesu anaticitila. Cotelo, popeza Yehova ndi Yesu atisonyeza cikondi, tiyeni tizitengela citsanzo ca Yesu, kukonda abale athu, ndi kuwakhululukila mocokela pansi pa mtima.
^ [1] (ndime 18) Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.