Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Zimene Mungacite kuti Muthane na Nkhawa

Zimene Mungacite kuti Muthane na Nkhawa

Ngati mufuna kuthetsa nkhawa, mufunika kuganizila za thanzi lanu, mmene mumacitila zinthu ndi ena, zolinga zanu komanso zimene mumaona kuti n’zofunika kwambili mu umoyo wanu. Nkhani ino, ifotokoza mfundo zofunika zimene zingakuthandizeni kuthana nazo nkhawa, kapena kuzicepetsa.

Tsiku Lililonse Lili na Nkhawa Zake

“Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”​—MATEYU 6:34.

Tanthauzo lake: Tsiku na tsiku timakhala na nkhawa. Conco, musatenge nkhawa za mawa kuwonjezela pa za lelo. Tsiku lililonse lili na nkhawa zake.

  • Nkhawa ingapangitse munthu kupanikizika maganizo. Conco, muyenela kudziŵa izi: Coyamba, muzikumbukila kuti nkhawa zina simungazipewe. Ndipo kuganizila kwambili zinthu zimene simungazipewe, kungakuwonjezeleni nkhawa. Caciŵili, muyenela kudziŵa kuti nthawi zambili zinthu sizifika poipilatu mmene tinali kuganizila.

Dziikileni Miyezo Yoyenela

“Nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.”​—MIYAMBO 11:2.

Tanthauzo lake: Pewani kufuna kucita zinthu mwaungwilo. Musayembekezele kuti imwe kapena anthu ena angacite zonse popanda kulakwitsa ciliconse.

  • Khalani odzicepetsa na kudziikila miyezo imene mungakwanitse. Ndiponso mufunika kudziŵa zolephela zanu ndi za ena. Mukacita izi, mungacepetse nkhawa zanu ndi za anthu ena, ndipo zidzakhala zosavuta kwa inu ndi kwa ena kukwanilitsa zolinga. Komanso, muzikhala wansangala. Mukaseka, olo kuti zinthu zalakwika, mumamasuka na kukhala wokondwela.

Dziŵani Zimene Zimakubweletselani Nkhawa

“Munthu wozindikila amakhala wofatsa.”​—MIYAMBO 17:27.

Tanthauzo lake: Kusalamulila mtima kungalepheletse munthu kuganiza bwino. Conco, mufunika kukhala wofatsa.

  • Zindikilani zimene zimakubweletselani nkhawa, ndipo dziŵani zimene mumacita mukakhala na nkhawa. Mwacitsanzo, kodi kaganizidwe, mmene mumamvelela, na khalidwe lanu zimakhala bwanji mukapanikizika maganizo? Mwina mungalembe zimenezo. Kuzindikila zimene mumacita mukakhala na nkhawa, kungakuthandizeni kulimbana na nkhawazo. Komanso, ganizilani njila zina zimene mungaseŵenzetse kuti mucotse zinthu zimene zimakubweletselani nkhawa mu umoyo wanu. Ngati n’zosatheka kucotselatu zinthuzo, pezani njila za mmene mungacepetsele nkhawa. Mungacite izi mwa kuyesetsa kutsiliza msanga nchito, na kugaŵa bwino nthawi.

  • Yesani kusintha mmene mumaonela zinthu. Zimene imwe mumada nazo nkhawa, mwina n’zosadetsa nkhawa kwa wina. Zingakhale conco cifukwa cakuti mumaona zinthu mosiyana. Onani zinthu zitatu izi zimene mungacite:

    1. Musafulumile kukaikila zolinga za ena. Mwina wina angakulumphileni pa mzele. Mukakhala na maganizo akuti wakucitani cipongwe, mungakalipe. M’malo mwake, bwanji osaona kuti mwina ali na zolinga zabwino? Ndipo mwina zingakhaledi zoona!

    2. Pezani mpata pa zimene zacitika. Kuyembekezela kuonana na dokotala pa mzela wautali, kapena kuyembekezela kukwela ndeke pa eyapoti, kungakhale kosavuta ngati mungaseŵenzetse nthawiyo kuŵelenga zinthu zina, kuseŵenzela pa cipangizo ca makono, kapenanso kuŵelenga maimelo.

    3. Muziganizila zimene zacitika kuti n’zazikulu bwanji. Dzifunseni kuti, ‘Kodi vutoli lidzakula cakuti maŵa lidzakhalapo ndithu, mwina mpaka wiki ya maŵa?’ Muzisiyanitsa nkhani zing’ono-zing’ono, zosakhalitsa, komanso nkhani zikulu-zikulu kwambili.

Citani zinthu mwadongosolo

“Zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.”​—1 AKORINTO 14:40.

Tanthauzo lake: Yesani kukhala wadongosolo mu umoyo wanu.

  • Tonse timakondwela kucita zinthu mwadongosolo mu umoyo wathu. Cimodzi mwa zinthu zingapangitse munthu kukhala wopanda dongosolo komanso kukhala na nkhawa, ni kugonekeza zinthu. Bwanji osayesa kucita zinthu ziŵili izi?

    1. Pangani ndandanda imene mungakwanitse kuitsatila, ndipo itsatileni.

    2. Zindikilani na kuwongolela maganizo alionse amene amakupangitsani kugonekeza zinthu.

Muzipeza Nthawi Yopumula

“Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwila nchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.”​—MLALIKI 4:6.

Tanthauzo lake: Anthu amene amakonda nchito monyanyila, amadzimana mapindu a “kugwila nchito mwakhama.” Angakhale alibe mphamvu kapena nthawi yakuti asangalale na ndalama zimene amaseŵenzela.

  • Muziona nchito na ndalama moyenela. Kukhala na ndalama zoculuka sikubweletsa cimwemwe coculuka, kapena kucepetsa nkhawa. Ndipo m’ceni-ceni zingalande munthu cimwemwe na kuwonjezela nkhawa. Mlaliki 5:12 imati: “Zambili zimene munthu wolemela amakhala nazo zimamulepheletsa kugona.” Conco, muzikhala okhutila na zimene muli nazo.

  • Pezani nthawi yopumula. Mungacepetse nkhawa mwa kucita zinthu zimene mumakondwela nazo. Komabe, zosangalatsa zimene simucitapo kanthu monga kutamba TV, sizingakhale zothandiza.

  • Muzikhala na malile pa kaseŵenzetsedwe ka zipangizo zamakono. Pewani kungokhalila kuona maimelo, mameseji, kapena kuyenda pa mawebusaiti a maceza. Ngati zingatheke, osaona mameseji okhudzana na nchito pa nthawi imene simuseŵenza.

Samalilani Thanzi Lanu

“Kucita masewela olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”​—1 TIMOTEYO 4:8.

Tanthauzo lake: Maseŵela olimbitsa thupi amathandiza kukhala na thanzi labwino.

  • Khalani na zizoloŵezi zabwino. Maseŵela olimbitsa thupi angakuthandizeni kukhala wokondwela, na kulimbana na nkhawa mosavuta. Muzidya zakudya zopatsa thanzi, ndipo muzidya mokwanila. Cina, muzipumula mokwanila.

  • Pewani “njila” zowononga zothetsela nkhawa, monga kukoka fodya kapena kumwa moŵa kwambili. Cifukwa m’kupita kwa nthawi, izi zingakuwonjezeleni nkhawa, kuwononga thanzi na ndalama zanu.

  • Ngati muli na nkhawa yaikulu kwambili, kaonaneni na dokotala. Musacite manyazi kupempha cithandizo ca ku cipatala.

Ikani Zinthu Zofunika pa Malo Oyamba

“Muzitsimikizila kuti zinthu zofunika kwambili ndi ziti.”​—AFILIPI 1:10.

Tanthauzo lake: Mosamala, onani zinthu zimene mumaika patsogolo.

  • Lembani mndandanda wa nchito zimene mufunika kugwila malinga na kufunika kwake. Izi zingakuthandizeni kuika maganizo pa nchito zofunika kwambili, ndiponso zidzakuthandizani kudziŵa nchito zimene mungazicite nthawi ina, zimene mungapatseko ena, kapena zimene mungazicotse pa mndandanda.

  • Kwa wiki imodzi, lembani mmene mumaseŵenzetsela nthawi yanu. Ndiyeno pezani njila za mmene mungaseŵenzetsele bwino nthawi. Ngati museŵenzetsa bwino nthawi, simudzapanikiza kwambili.

  • Muzipatula nthawi yopumula. Olo kupumulako pang’ono kungakupatseni mphamvu na kucepetsa nkhawa.

Pemphani Thandizo

“Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.”​—MIYAMBO 12:25.

Tanthauzo lake: Mawu acifundo ndi okoma mtima ocokela kwa ena angakuthandizeni kumvelako bwino.

  • Pa zimene zikuvutitsani maganizo, uzankoni munthu wina amene amakumvetsetsani. Munthu amene mumam’dalila angakuthandizeni kuona zinthu m’njila ina. Mwina angakuthandizeni kuona njila yothetsela vuto imene imwe simunaione.

  • Pemphani thandizo. Kodi mungapemphe wina kugwila nchito imene munali kufunika kuigwila, kapena kupempha kuti akuthandizeni?

  • Ngati munthu amene mumaseŵenza naye amakuvutitsani, pezani zimene mungacite kuti mucepetse vutolo. Mwacitsanzo, kodi mungayese kukambilana na munthuyo mokoma mtima komanso mosamala, za mmene mumamvelela pa zimene amacita? (Miyambo 17:27) Ngati mwacita zimenezo koma zavuta, kodi mungacepetseko nthawi imene mumacitila zinthu pamodzi?

Muzisamalila Zofunikila Zanu Zauzimu

“Odala [acimwemwe] ndi anthu amene amazindikila zosowa zawo zauzimu.”—MATEYU 5:3.

Tanthauzo lake: Ife anthu timafunikila zakudya, zovala, na pogona. Koma si izi cabe, timafunikilanso zinthu zauzimu. Kuti tikhale acimwemwe, tiyenela kudziŵa zimene tifunikila kuuzimu, na kuyesetsa kuzipeza.

  • Pemphelo lingakhalenso lothandiza ngako. Mulungu akupemphani kuti ‘mum’tulile nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Kupemphela na kusinkha-sinkha pa zinthu zabwino, kungathandizeni kukhala na mtendele waukulu wa mu mtima.—Afilipi 4:6, 7.

  • Ŵelengani zinthu zimene zingakuthandizeni kulimbitsa ubwenzi wanu na Mulungu. Mfundo zimene takambilana m’nkhani ino n’zocokela m’Baibo, imene inalembedwa kuti ikwanilitse zofunikila zathu zauzimu. Mfundo zimenezi zingathandize munthu kukhala na “nzelu zopindulitsa ndiponso kuganiza bwino.” (Miyambo 3:21) Bwanji osakhala na colinga coŵelenga Baibo? Mungacite bwino kuyamba na kuŵelenga buku la Miyambo.