Mulungu Analonjeza Kuti Dziko Lapansi Lidzakhalapo Kwamuyaya
“Dziko Lapansi n’lolimba kuposa mmene timaganizila.”
Izi n’zimene gulu lina la ofufuza a padziko lonse anapeza pambuyo pocita kafukufuku pa kusintha kwa nyengo. Ngati mumakhulupilila kuti kuli Mlengi amene amasamalila anthu, mfundo ili pamwambapa ingakukumbutseni kuti Mulungu analenga dziko lapansi kuti lizitha kudzikonza lokha.
Komabe, cifukwa anthu acita zinthu zambili zowononga dziko, zakhala zovuta kuti dziko lapansi lizidzikonza lokha. N’cifukwa ciyani ndife otsimikiza kuti Mulungu adzacitapo cina cake kuti alikonze?
Onani malemba ali m’bokosi otitsimikizila kuti dziko lapansi lidzapulumuka na kukhalapo kwamuyaya.
Mulungu ndiye analenga dziko lapansi. “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1
Mulungu amati dziko lapansi ni lake. “Dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi za Yehova. a”—Salimo 24:1
Mulungu analenga dziko lapansi kuti likhalepo kwamuyaya. “Mwakhazikitsa dziko lapansi pamaziko olimba. Silidzagwedezeka mpaka kalekale, mpaka muyaya.”—Salimo 104:5
Mulungu analonjeza kuti padziko lapansi padzakhala zamoyo kwamuyaya. “Mulungu woona, amene anaumba dziko lapansi ndi kulipanga, . . . sanalilenge popanda colinga, [koma] analiumba kuti anthu akhalemo.”—Yesaya 45:18
Mulungu analonjeza kuti anthu adzakhala na moyo padziko lapansi kwamuyaya. “Olungama adzalandila dziko lapansi, Ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29
Mulungu anapanga dziko lapansi kuti anthu azisangalala na umoyo popanda kuliwononga. Baibo inakambilatu kuti Mulungu, pa nthawi yake yoikika, adzathetsa zoipa zonse zowonoga dziko zimene anthu amacita.—Chivumbulutso 11:18
Baibo imalonjeza kuti pa nthawiyo Mulungu adzasintha dziko lapansi kukhala malo abwino, paradaiso wokongola, ndipo adzatambasula dzanja lake na “kukhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.”—Salimo 145:16
a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.