Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Woweluza wa Dziko Lonse” Amacita Cilungamo Nthawi Zonse

“Woweluza wa Dziko Lonse” Amacita Cilungamo Nthawi Zonse

“Iye ndi Thanthwe, ndipo nchito yake ndi yangwilo, njila zake zonse ndi zolungama.”—DEUT. 32:4.

NYIMBO: 112, 89

1. Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kukhulupilila kuti Yehova amacita zinthu mwacilungamo? (Onani pikica pamwamba.)

“KODI Woweluza wa dziko lonse lapansi sadzacita colungama?” (Gen. 18:25) Pofunsa funso limeneli, Abulahamu anaonetsa kuti anali kukhulupilila kuti Yehova adzaŵeluza molungama mizinda ya Sodomu ndi Gomora. Anali kudziŵa kuti Yehova sangacite zinthu mopanda cilungamo mwa “kupha olungama pamodzi ndi oipa.” Iye anakamba motsimikiza kuti Mulungu ‘sangacite zimenezo ayi.’ Patapita zaka 400, Yehova anakamba mau awa ponena za iye mwini: ‘Thanthwe, nchito yake ndi yangwilo, njila zake zonse ndi zolungama. Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama. Iye ndi wolungama ndi wowongoka.’—Deut. 31:19; 32:4.

2. N’cifukwa ciani tingakambe kuti n’zosatheka Yehova kucita zinthu mopanda cilungamo?

2 N’cifukwa ciani Abulahamu anali kukhulupilila kuti Yehova amapeleka ciweluzo colungama nthawi zonse? Cifukwa Yehova ndiye mwini ciweluzo ndi cilungamo. Popeza kuti mfundo za Yehova n’zolungama nthawi zonse, n’zosatheka iye kuweluza mopanda cilungamo. Komanso, Mau ake amakamba kuti “iye amakonda cilungamo ndi ciweluzo cosakondela.”—Sal. 33:5.

3. Fotokozani citsanzo ca kupanda cilungamo kumene kumacitika m’dzikoli.

3 Anthu oona mtima amatonthozedwa akadziŵa kuti Yehova nthawi zonse amacita zinthu mwacilungamo, cifukwa kupanda cilungamo n’kofala m’dzikoli. Cifukwa ca kupanda cilungamo kumeneku, anthu ena acilitidwa nkhanza zosaneneka. Mwacitsanzo, anthu ena amaweluzidwa ndi kuikidwa m’ndende cifukwa cowanamizila kuti anapalamula mlandu winawake. Ena atawapima DNA ndi kupeza umboni wakuti ni osalakwa, anawamasula, koma pambuyo pakuti akhala kale m’ndende zaka zambili. Zinthu zopanda cilungamo ngati zimenezi zimakhumudwitsa. Koma pali zinthu zina zopanda cilungamo zimene Akhristu angaone kuti n’zovuta kwambili kuzipilila.

MUMPINGO

4. Kodi cikhulupililo ca Mkhristu cingayesedwe bwanji?

4 Akhristu amadziŵa kuti angacitilidwe zinthu zopanda cilungamo ndi munthu amene sali mumpingo wacikhristu. Koma cikhulupililo cathu cingayesedwe tikaona kapena tikacitilidwa zinthu zimene tiona kuti n’zopanda cilungamo mumpingo. Kodi mungacite bwanji ngati mwaona kuti mwacitilidwa zinthu zopanda cilungamo mumpingo kapena ngati Mkhristu mnzanu wakulakwilani? Kodi mudzakhumudwa?

5. N’cifukwa ciani Mkhristu sayenela kudabwa ngati waona kapena kucitilidwa zinthu zopanda cilungamo mumpingo?

5 Popeza kuti tonse ndise opanda ungwilo ndipo timacimwa, timadziŵa kuti wina mumpingo akhoza kutilakwila kapena ise tingalakwile ena. (1 Yoh. 1:8) Koma zimenezi sizicitika kaŵili-kaŵili, ndipo Akhristu okhulupilika sadabwa kapena kukhumudwa akacitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Yehova wapeleka malangizo m’Mau ake amene angatithandize kukhalabe okhulupilika ngati Mkhristu mnzathu watilakwila.—Sal. 55:12-14.

6, 7. Ni zinthu zopanda cilungamo ziti zimene zinacitikila m’bale wina mumpingo? Nanga ni makhalidwe ati amene anamuthandiza kuti asakhumudwe?

6 Ganizilani zimene zinacitikila m’bale Willi Diehl. Kuyambila mu 1931, M’bale Diehl anatumikila mokhulupilika pa Beteli ya ku Bern, m’dziko la Switzerland. Mu 1946, analoŵa kalasi ya namba 8 ya Sukulu ya Giliyadi, ku New York, m’dziko la United States. Atatsiliza maphunzilo, anam’tumiza ku Switzerland kukatumikila monga woyang’anila dela. M’nkhani yosimba za moyo wake, M’bale Diehl anati: “M’mwezi wa May 1949, n’nadziŵitsa ofesi ya nthambi ku Bern kuti nifuna kukwatila.” Kodi ofesi ya nthambi inamuuza ciani? Iye anati: “Sananipatse mwayi uliwonse wa utumiki kupatulapo kucita upainiya wanthawi zonse.” M’baleyo anapitiliza kukamba kuti: “Sanali kunilola kukamba nkhani . . . Ambili analeka kutipatsa moni, ndipo anali kutiona ngati ocotsedwa.”

7 Kodi M’bale Diehl anacita bwanji? Iye anati: “Ife tinadziŵa kuti Malemba saletsa kukwatila. Conco, tinapeza cilimbikitso mwa kupemphela ndi kudalila Yehova.” M’kupita kwa nthawi, abale anathandizidwa kuwongolela maganizo awo olakwika pa nkhani ya cikwati, amene anacitsa kuti M’bale Diehl ndi mkazi wake acitilidwe zinthu mopanda cilungamo, ndipo iye anapatsidwanso mautumiki amene anali nawo poyamba. Iye anadalitsidwa cifukwa cokhala wokhulupilika kwa Yehova. * Ndiyeno ife tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Ngati zinthu zopanda cilungamo zaconco zanicitikila, kodi inenso ningakhale wokhulupilika kwa Mulungu? Kodi ningayembekezele Yehova moleza mtima kapena ningayese kuthetsa vutolo panekha?’—Miy. 11:2; ŵelengani Mika 7:7.

8. N’cifukwa ciani nthawi zina tingaone zinthu molakwika n’kumaganiza kuti munthu wina mumpingo kapena ise, tacitilidwa zinthu zopanda cilungamo?

8 Komabe, nthawi zina tingaone zinthu molakwika n’kumaganiza kuti munthu wina mumpingo kapena ise, tacitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Izi zingacitike cifukwa ndise opanda ungwilo kapena cifukwa sitidziŵa bwino nkhani yonse. Kaya munthu wina anatilakwiladi kapena ise ndi amene tili na maganizo olakwika pankhaniyo, tifunika kupemphela kwa Yehova, kum’dalila, ndi kukhalabe wokhulupilika kwa iye. Kucita zimenezi kudzatithandiza kuti “tisakwiyile Yehova.”—Ŵelengani Miyambo 19:3.

9. Kodi tidzakambilana zocitika ziti m’nkhani ino ndi yotsatila?

9 Tiyeni tikambilane zocitika zitatu zoonetsa kupanda cilungamo kumene kunacitika pakati pa anthu a Yehova m’nthawi yakale. M’nkhani ino, tidzakambilana za Yosefe mdzukulu wa Abulahamu, ndi zimene abale ake anamucitila. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mmene Yehova anacitila zinthu ndi Ahabu, Mfumu ya Isiraeli, ndiponso zimene mtumwi Petulo anacita ali ku Antiokeya wa ku Siriya. Pamene tikambilana zitsanzo zimenezi, onani mmene zingakuthandizileni kuikabe maganizo anu pa zinthu zauzimu ndi kuteteza ubwenzi wanu ndi Yehova, maka-maka pamene muona kuti ena akucitilani zinthu zopanda cilungamo.

YOSEFE ANACITILIDWA ZINTHU ZOPANDA CILUNGAMO

10, 11. (a) N’zinthu zopanda cilungamo ziti zimene zinacitikila Yosefe? (b) Kodi Yosefe anali na mwayi wotani pamene anali m’ndende?

10 Yosefe, mtumiki wokhulupilika wa Yehova, anacitilidwa zinthu zopanda cilungamo ndi anthu amene sanali kutumikila Mulungu. Koma cimene cinamuŵaŵa kwambili n’cakuti ngakhale abale ake eni-eni, naonso anamucitila zinthu zopanda cilungamo. Pamene Yosefe anali na zaka pafupi-fupi 20, abale ake anamugwila ndi kum’gulitsa monga kapolo. Anthu amene anamugula anapita naye ku Iguputo. (Gen. 37:23-28; 42:21) Pamene Yosefe anali ku Iguputo, anamunamizila kuti anafuna kugwilila mkazi wa mbuye wake, ndipo anaikidwa m’ndende popanda kuzengedwa mlandu. (Gen. 39:17-20) Iye anakhala m’ndendemo kwa zaka pafupi-fupi 13. Kodi kuganizila zimene zinacitikila Yosefe kungatithandize bwanji ngati Mkhristu mnzathu waticitila zinthu zopanda cilungamo?

11 Nthawi ina, Yosefe anali na mwayi wofotokozela mkaidi mnzake zimene zinamucitikila. Mkaidiyo poyamba anali mkulu “wopelekela cikho” kwa mfumu. Pamene iye anali m’ndende pamodzi ndi Yosefe, analota maloto, ndipo Yosefe anamasulila maloto akewo mouzilidwa na Mulungu. Yosefe anakamba kuti Farao adzabwezela wopelekela cikhoyo pa udindo wake wakale. Atamasulila malotowo, Yosefe anatengelapo mwayi wofotokozela mnzakeyo za vuto lake. Tingaphunzile zambili kwa Yosefe tikaganizila zimene anakamba ndi zimene anapewa kukamba.—Gen. 40:5-13.

12, 13. (a) Kodi zimene Yosefe anakamba kwa wopelekela cikho, zinaonetsa bwanji kuti sanadzilekelele pa mavuto amene anakumana nawo? (b) Ni zinthu ziti zimene Yosefe sanakambe kwa wopelekela cikho?

12 Ŵelengani Genesis 40:14, 15. Pofotokoza zimene zinamucitikila, onani kuti Yosefe anakamba kuti anacita ‘kumuba’. Zoonadi, iye anacitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Yosefe anafotokozanso kuti sanalakwe ciliconse ngakhale kuti anali m’ndende. Pa cifukwa cimeneci, Yosefe anapempha wopelekela cikho kuti akafotokoze za iye kwa Farao. Cifukwa ciani? Iye anati: “Kuti ndidzatuluke m’ndende muno.”

13 Pofotokoza vuto lake kwa mkaidi mnzake, kodi Yosefe anakamba mwamphwayi ngati kuti safuna kutuluka m’ndendemo? Iyayi. Iye anali kudziŵa bwino kuti anacitilidwa zinthu zambili zopanda cilungamo. Komanso pokamba ndi wopelekela cikho, anafotokoza mosapita m’mbali zimene zinamucitikila podziŵa kuti mnzakeyo akanamuthandiza. Koma dziŵani kuti m’Malemba, mulibe pamene paonetsa kuti Yosefe anauzako munthu wina aliyense zakuti abale ake ndiwo anam’gulitsa. Ngakhale Farao sanamuuze. Ndipo pamene abale ake anabwela ku Iguputo ndi kugwilizananso ndi Yosefe, Farao anawalandila ndi kuwalola kukhala m’dziko la Iguputo kuti azisangalala ndi “zabwino za dziko lonse la Iguputo.”—Gen. 45:16-20.

Kukamba mau oipa okhudza munthu wina kungapangitse kuti vuto likule kwambili (Onani palagilafu 14)

14. N’ciani cingatithandize kupewa misece ngati wina watilakwila mumpingo?

14 Ngati Mkhristu waona kuti mnzake wamulakwila, ayenela kusamala kuti asayambe kumunenela misece. Koma ngati wina mumpingo wacita colakwa cacikulu, ndi bwino kupempha thandizo kwa akulu ndi kuwadziŵitsa za colakwaco. (Lev. 5:1) Komabe, ngati zolakwa n’zing’ono-zing’ono, tikhoza kuzithetsa popanda kuuzako wina aliyense, ngakhale akulu. (Ŵelegani Mateyu 5:23, 24; 18:15.) Conco, tiyeni tiziyesetsa kuthetsa nkhani zaconco mogwilizana ndi mfundo za m’Baibo. Nthawi zina pambuyo pokambilana, tingazindikile kuti mnzathuyo sanaticitile zinthu zopanda cilungamo. Zikakhala conco, tingakhale okondwa pozindikila kuti sitinakulitse nkhaniyo mwa kuipitsa mbili ya Mkhristu mnzathu. Kaya munthuyo anatilakwiladi kapena ayi, tiyenela kukumbukila kuti kukamba zinthu zimene zingaipitse mbili yake sikungathetse vutolo. Kukhala wokhulupilika kwa Yehova ndi kwa abale athu kudzatithandiza kupewa mijedo. Pokamba za munthu amene “akuyenda mosalakwitsa zinthu,” wamasalimo anati: “Sanena misece ndi lilime lake. Sacitila mnzake coipa, ndipo satonza bwenzi lake lapamtima.”—Sal. 15:2, 3; Yak. 3:5.

MUZIKUMBUKILA KUTI UBALE WANU NA MULUNGU NI WOFUNIKA KWAMBILI

15. Kodi Yosefe anadalitsidwa bwanji kaamba kokhala pa ubale na Yehova?

15 Pa ubale umene Yosefe anali nawo na Yehova, tipezapo phunzilo lina lofunika kwambili. Pa zaka zonse 13 zimene Yosefe anakhala m’ndende, anaonetsa kuti anali kuona zinthu monga mmene Yehova amazionela. (Gen. 45:5-8) Iye sanaimbe mlandu Yehova pa zimene zinamucitikila. Ngakhale kuti Yosefe sanaiwale mavuto amene anakumana nawo, sanakhumudwe. Cacikulu, iye sanalole kuti kupanda ungwilo ndi zolakwa za ena zisokoneze ubale wake na Yehova. Kukhulupilika kwa Yosefe kunam’patsa mwayi woona mmene Yehova anakonzela zinthu zopanda cilungamo ndi kum’dalitsa pamodzi na banja lake.

16. N’cifukwa ciani tifunika kuyandikila kwambili Yehova ngati wina mumpingo watilakwila?

16 Ifenso tifunika kuona ubale wathu na Yehova kukhala wamtengo wapatali ndi kuuteteza. Tisalole kupanda ungwilo kwa abale athu kutilekanitsa ndi Mulungu amene timam’konda ndi kum’lambila. (Aroma. 8:38, 39) M’malomwake, ngati Mkhristu mnzathu watilakwila, tiyenela kutengela citsanzo ca Yosefe. Tiyenela kuyandikila kwambili Yehova ndi kuyesetsa kuona zinthu mmene iye amazionela. Tikacita zonse zimene tingathe motsatila Malemba kuti tithetse vutolo, tifunika kusiya nkhaniyo m’manja mwa Yehova pokhulupilila kuti iye adzathetsa vutolo pa nthawi yake ndiponso m’njila yoyenela.

MUZIDALILA “WOWELUZA WA DZIKO LONSE”

17. Tingaonetse bwanji kuti timakhulupilila “Woweluza wa dziko lonse lapansi”?

17 Popeza kuti tikali m’dziko loipa, nthawi iliyonse tingacitilidwe zinthu zopanda cilungamo. Nthawi zina, inu kapena munthu wina, akhoza kucitilidwa zinthu zopanda cilungamo, kapena kuona kuti zinthu zina sizinacitike mwacilungamo mumpingo. Musalole zimenezo kukukhumudwitsani. (Sal. 119:165) M’malomwake, tifunika kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu, kupempha thandizo kwa iye, ndi kum’dalila. Komanso, tiyenela kukumbukila kuti sitingadziŵe zonse zokhudza nkhaniyo. Ndiponso popeza ndife opanda ungwilo, nthawi zina timaona zinthu molakwika. Ndipo malinga n’zimene taphunzila pa nkhani ya Yosefe, tifunika kupewa kukamba zoipa za ena cifukwa kucita zimenezi sikungathetse vuto. Cotsilizila, m’malo moyesa kuthetsa tekha vuto, tifunika kuyesetsa kukhalabe okhulupilika ndi kuyembekezela Yehova moleza mtima kuti ndi amene adzathetsa vutolo. Tikacitita zimenezi, Yehova adzatiyanja ndi kutidalitsa, monga mmene anacitila ndi Yosefe. Inde, tifunika kukhulupilila kuti Yehova, “Woweluza wa dziko lonse lapansi,” nthawi zonse adzacita zinthu mwacilungamo cifukwa “njila zake zonse ndi zolungama.”—Gen. 18:25; Deut. 32:4.

18. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

18 M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zocitika zina ziŵili zoonetsa kupanda cilungamo kumene kunacitika pakati pa anthu a Yehova m’nthawi yakale. Kukambilana nkhani zimenezi, kudzatithandiza kuona mmene kudzicepetsa ndi kukhululukila ena kumagwilizanilana ndi cilungamo ca Yehova.

^ par. 7 Onani nkhani yofotokoza mbili ya moyo wa m’bale Willi Diehl, yamutu wakuti “Yehova Ndiye Mulungu Wanga, Amene Ndimkhulupirira,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1991.