Mtendele—Kodi Mungaupeze Bwanji?
POPEZA tikhala m’dziko la mavuto, pamafunika khama kuti tipeze mtendele. Komabe olo tiupeze, nthawi zambili sukhalitsa. Kodi Mau a Mulungu amakamba kuti n’ciani cingatithandize kupeza mtendele weni-weni komanso wokhalitsa? Nanga anthu ena tingawathandize bwanji kupeza mtendele?
KODI COFUNIKA N’CIANI KUTI TIKHALE NA MTENDELE WENI-WENI?
Timakhala na mtendele weni-weni ngati tidzimva kuti ndise otetezeka komanso ngati palibe cimene cikutivutitsa maganizo. Tifunikanso kukhala pa ubwenzi wolimba ndi anthu ena. Ndipo cofunika maningi kuti tipeze mtendele wokhalitsa ni kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu. Kodi tingacite bwanji zimenezi?
Ngati timamvela malamulo olungama a Yehova na mfundo zake, timaonetsa kuti timam’dalila ndiponso timafuna kukhala naye pa ubwenzi wolimba. (Yer. 17:7, 8; Yak. 2:22, 23) Ndipo iye amatiyandikila na kutidalitsa potipatsa mtendele wa mumtima. Lemba la Yesaya 32:17 limati: “Nchito ya cilungamo ceniceni idzakhala mtendele, ndipo zocita za cilungamo ceniceni zidzakhala bata ndi mtendele mpaka kalekale.” Tingapeze mtendele weni-weni wa mumtima ngati timvela Yehova na mtima wonse.—Yes. 48:18, 19.
Cinanso cimene cimatithandiza kukhala na mtendele weni-weni, ni mzimu woyela, umene ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Atate wathu wakumwamba.—Mac. 9:31.
MZIMU WA MULUNGU UMATITHANDIZA KUKHALA NA MTENDELE WA MUMTIMA
Mtumwi Paulo anatomola mtendele monga khalidwe lacitatu pa makhalidwe “amene mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22, 23) Popeza kuti mtendele weni-weni ni cipatso ca mzimu wa Mulungu, tifunika kulola mzimu woyela kutitsogolela kuti tikhale na mtendele umenewu. Kodi mzimu wa Mulungu ungatithandize bwanji kupeza mtendele? Tiyeni tikambilaneko njila ziŵili.
Yoyamba, timapeza mtendele mwa kuŵelenga Sal. 1:2, 3) Pamene tisinkhasinkha uthenga wa m’Baibo, mzimu wa Mulungu umatithandiza kumvetsetsa mmene Yehova amaonela zinthu pa nkhani zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, timamvetsetsa mmene iye waonetsela kuti ni wokonda mtendele komanso cifukwa cake amaona mtendele kukhala wofunika kwambili. Pamene tiseŵenzetsa mfundo zimene taphunzila m’Baibo, timakhala na mtendele woculuka mu umoyo wathu.—Miy. 3:1, 2.
Mau ouzilidwa a Mulungu nthawi zonse. (Yaciŵili, tifunika kupempha mzimu woyela wa Mulungu. (Luka 11:13) Yehova analonjeza kuti ngati timupempha kuti atithandize, “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima [yathu] ndi maganizo [athu] mwa Khristu Yesu.” (Afil. 4:6, 7) Ngati nthawi zonse timapemphela na kudalila mzimu wa Yehova, iye adzatipatsa mtendele woculuka umene umakhala cabe ndi anthu amene ali pa ubwenzi wabwino na iye.—Aroma 15:13.
Kodi ena aseŵenzetsa bwanji malangizo amenewa na kusintha zinthu zina mu umoyo wawo kuti akhale na mtendele weniweni wa mumtima, komanso kuti akhale pa mtendele na Yehova ndi anthu ena?
MMENE ANAPEZELA MTENDELE WENI-WENI
Mu mpingo wacikhristu masiku ano, muli ena amene poyamba anali “okonda kukwiya,” koma manje ni oganizila ena, okoma mtima, oleza mtima, ndipo amacita zinthu mwamtendele na ena. * (Miy. 29:22) Onani mmene ofalitsa ena aŵili a Ufumu anasinthila khalidwe lawo lokonda kukwiya, na kuyamba kukhala mwamtendele ndi anthu ena.
David anali na khalidwe loipa ndipo anali kukamba mau oipa kwa ena. Asanadzipeleke kwa Mulungu, iye anali na vuto lopeza zifukwa anthu ena, ndiponso anali kukamba mokhadzula kwa makolo komanso abale ake. M’kupita kwa nthawi, David anaona kuti afunika kusintha, ndipo anasinthadi n’kukhala munthu wamtendele. N’ciani cinam’thandiza? Iye anati: “N’nayamba kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo mu umoyo wanga. Zotulukapo zinali zakuti, ine ndi a m’banja langa tinayamba kulemekezana.”
Rachel anali wamkali cifukwa ca mmene analeledwela. Iye anati: “Ngakhale lomba, nthawi zina zimanivuta kulamulila mkwiyo cifukwa makolo
anga anali kukalipa-kalipa.” Kodi n’ciani cinamuthandiza kuti ayambe kukhala mwamtendele ndi ena? Iye anati: “N’nali kupemphela kwa Yehova nthawi zonse kuti anithandize.”David na Rachel ni zitsanzo ziŵili cabe zoonetsa mmene kuseŵenzetsa mfundo za m’Malemba ouzilidwa na kudalila mzimu wa Mulungu kungatithandizile kukhala mwamtendele ndi ena. Conco, olo tili m’dziko loipa, tingathe kukhala na mtendele wa mumtima umene ungacititse kuti tizikhala ogwilizana ndi anthu a m’banja lathu komanso Akhristu anzathu. Komabe, Yehova amatilimbikitsa kuti ‘tizikhala mwamtendele ndi anthu onse.’ (Aroma 12:18) Kodi zimenezi n’zotheka? Nanga tingapeze mapindu anji ngati tiyesetsa kukhala mwamtendele ndi anthu onse?
YESETSANI KUKHALA MWAMTENDELE NDI ENA
Pamene tilalikila, timathandiza anthu kupindula na uthenga wathu wa mtendele wokamba za Ufumu wa Mulungu. (Yes. 9:6, 7; Mat. 24:14) Cokondweletsa n’cakuti anthu ambili amamvetsela. Zotulukapo zake, iwo sakhumudwa kapena kutaya mtima na mavuto amene amakumana nawo. M’malomwake, amakhala na ciyembekezo ceni-ceni ca m’tsogolo ndipo izi zimawalimbikitsa ‘kufunafuna mtendele ndi kuusunga.’—Sal. 34:14.
Komabe, si onse amene amamvetsela uthenga wathu tikawalalikila. (Yoh. 3:19) Ngakhale n’conco, mzimu wa Mulungu umatithandiza kuti tizilalikila uthenga wabwino mwamtendele ndi mwaulemu. Mwanjila imeneyi, timatsatila malangizo a Yesu okhudza ulaliki, amene ali pa Mateyu 10:11-13, akuti “Pamene mukuloŵa m’nyumba, pelekani moni kwa a m’banja limenelo. Ngati nyumbayo ili yoyenela, mtendele umene mukuifunila ukhale panyumbayo, koma ngati si yoyenela, mtendele wanu ubwelele kwa inu.” Tikamatsatila malangizo amenewa a Yesu, tingacoke pa khomo la mwininyumba tili na mtendele wathu, ndipo timakhala na mwayi wokamulalikilanso m’tsogolo.
Timalimbikitsanso mtendele mwa kukamba mwaulemu kwa akulu-akulu a boma, olo amene amatsutsa nchito yathu. Mwacitsanzo, cifukwa ca tsankho boma ya dziko lina mu Africa inali kuletsa Mboni za Yehova kumanga Nyumba za Ufumu. Pofuna kuthetsa nkhaniyi mwamtendele, m’bale wina amene kumbuyoku anatumikilako monga mmishonale m’dziko limenelo anatumiwa kuti akaonane na Kazembe wa dzikolo ku London, m’dziko la England. Iye anapita kuti akamufotokozele za nchito ya mtendele imene Mboni za Yehova zimacita m’dziko lake. Kodi zotulukapo zinali zotani?
M’baleyo anati: “N’tafika pa malo olandilila alendo na kuona mmene wolandila alendo anavalila, n’nazindikila kuti ni wa mtundu umene umakamba cinenelo cimene n’naphunzila. Conco, n’namupatsa moni m’citundu cakeco. Iye anadabwa, ndipo ananifunsa kuti: ‘Tikuthandizeni ciani?’ Mwaulemu, n’namuuza kuti nifuna kuonana ndi Kazembe. Iye anatumila foni Kazembeyo, ndipo anabwela na kunipatsa moni m’citundu ca kwawo. Pambuyo pake, anamvetsela mwachelu pamene n’nali kumufotokozela za nchito ya mtendele ya Mboni za Yehova.”
Cifukwa cakuti m’baleyo anali kufotokoza mwaulemu, zinathandiza kuti kazembeyo aziiona moyenela nchito yathu na kuleka kuizonda. Patapita nthawi, boma ya dziko lake inayamba kulola a Mboni kumanga Nyumba za Ufumu. Abale anakondwela ngako na zotulukapo zabwino zimenezi! Ndithudi, kucita zinthu mwaulemu ndi anthu ena kumabweletsa madalitso, kuphatikizapo mtendele.
MUNGATHE KUKHALA NA MTENDELE KWAMUYAYA
Masiku ano, anthu a Yehova amakondwela kukhala m’paladaiso wauzimu, mmene muli mtendele woculuka. Na imwe mungawonjezele mtendele umenewu mwa kuyesetsa kukulitsa khalidwe limeneli, lomwe ndi mbali ya cipatso ca mzimu. Koposa zonse, mudzakhala pa ubwenzi wabwino na Yehova ndipo mudzapeza mtendele woculuka komanso wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.—2 Pet. 3:13, 14.
^ par. 13 Khalidwe la kukoma mtima tidzalikambilana m’tsogolo, m’nkhani ina yofotokoza cipatso ca mzimu.