Kodi Kum’dziŵa Bwino Mulungu Kungakupindulileni Bwanji?
Podzafika pano, taphunzila kale zambili zotithandiza kupeza yankho ya funso yakuti, Kodi Mulungu n’ndani? Tinayamba na kuona m’Baibo kuti dzina lake ni Yehova ndiponso kuti khalidwe lake lalikulu ni cikondi. Tinaonanso zimene anaticitila komanso zimene adzaticitila kuti tipindule. Popeza pali zambili zofunika kudziŵa zokhudza Mulungu, mwina mungadzifunse ngati kucita zimenezi kungakupindulileni.
Yehova amalonjeza kuti, “ukam’funafuna, adzalola kuti um’peze.” (1 Mbiri 28:9) Ganizilani cabe mphatso ya mtengo wapatali imene ikuyembekezani mukam’funa-funa na kum’dziŵa bwino Mulungu. Inde “ubwenzi wolimba ndi Yehova”! (Salimo 25:14) Kodi ubwenzi umenewu ungakupindulileni bwanji?
Timapeza cimwemwe ceni-ceni. Yehova ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Kukhala naye pa ubwenzi wabwino na kutengela makhalidwe ake kudzakupatsani cimwemwe ceni-ceni, cimene cidzakuthandizani kukhala na thanzi labwino. (Salimo 33:12) Kuwonjezela apo, mudzakhala na umoyo wacimwemwe mwa kupewa makhalidwe oipa, na kukulitsa makhalidwe abwino, komanso kudziŵa kukhala bwino na anthu. Mudzafika povomeleza zimene wamasalimo anakamba kuti: “Kwa ine kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino.”—Salimo 73:28.
Amatisamalila. Yehova analonjeza atumiki ake kuti: “Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyang’anila.” (Salimo 32:8) Izi zitanthauza kuti Yehova amasamalila atumiki ake aliyense payekha-payekha malinga na zimene afunikila. (Salimo 139:1, 2) Conco, mukakhala pa ubwenzi wabwino na Yehova, mudzaona kuti iye nthawi zonse alipo kuti akuthandizeni.
Tidzakhala na tsogolo labwino kwambili. Kuwonjezela pa kukuthandizani kukhala na umoyo wacimwemwe ndi wokhutilitsa palipano, Yehova Mulungu wakupatsani mwayi wokhala na tsogolo labwino kwambili. (Yesaya 48:17, 18) Baibo imati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yohane 17:3) M’nthawi zovuta zino, ciyembekezo cimene Mulungu watipatsa cimatithandiza. Cili monga nangula ndipo “n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.”—Aheberi 6:19.
Izi n’zifukwa zocepa cabe zimene tifunika kukhalila pa ubwenzi na Mulungu komanso kum’dziŵa bwino. Kuti mudziŵe zambili, khalani womasuka kufunsa wa Mboni za Yehova aliyense, kapena yendani pa webusaiti ya jw.org.