NSANJA YA MLONDA—YOPHUNZILA January 2017

Magaziniyi ili na nkhani zophunzila wiki ya February 27 mpaka April 2, 2017.

Anadzipeleka na Mtima Wonse

Alongo ambili amene atumikila ku maiko ena, poyamba anacita mantha kusamukila ku dziko lacilendo. N’ciani cinawathandiza kukhala wolimba mtima? Nanga aphunzila ciani pa utumiki umenewu?

“Khulupilila Yehova Ndipo Cita Zabwino”

Yehova ni wokonzeka kutithandiza. Koma amayembekezela kuti ticite zimene tingakwanitse. Kodi lemba la caka ca 2017 litilimbikitsa bwanji kudalila Mulungu ndi kucita zimene tingakwanitse?

Muziyamikila Mphatso Yanu ya Ufulu Wosankha Zocita

Kodi ufulu wosankha zocita n’ciani nanga Baibo imaphunzitsa ciani za ufulu umenewu? Mungaonetse bwanji kuti mumalemekeza ufulu wa ena wosankha zocita?

N’cifukwa Ciani Kudzicepetsa N’kofunikabe?

Kodi kudzicepetsa n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani kukhala na khalidwe limeneli n’kofunika?

Mukhoza Kukhalabe Wodzicepetsa Ngakhale pa Ciyeso

N’ciani cingatithandize kukhalabe odzicepetsa ngati zinthu zasintha, ngati titonzedwa kapena kutamandidwa mopambanitsa, ndiponso ngati tikupanga zosankha pamene sitili otsimikiza?

“Zimenezo Uziphunzitse kwa Amuna Okhulupilika”

Kodi acikulile angathandize bwanji acinyamata kutenga maudindo aakulu? Kodi acinyamata angaonetse bwanji kuti amalemekeza abale amene atsogolela kwa zaka zambili?

Kodi Mudziŵa?

M’nthawi zakale, kodi moto unali “kunyamuliwa” bwanji kocoka pa malo ena kufika pa ena?