NKHANI YOPHUNZILA 20
NYIMBO 67 “Lalikila Mawu”
Pitilizani Kulalikila Cifukwa ca Cikondi!
“Coyamba uthenga wabwino ukuyenela kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.”—MALIKO 13:10.
ZOFUNIKA KUMVETSETSA
Mmene cikondi cimatilimbikitsila kugwila nchito yolalikila mokangalika komanso na mtima wonse.
1. Tinaphunzila ciyani pa msonkhano wa pacaka wa mu 2023?
PA MSONKHANO wa pacaka wa 2023, a tinalandila kamvedwe katsopano kosangalatsa pa zina mwa zimene timakhulupilila, ndipo tinalandila zilengezo zosangalatsa zokhudza ulaliki wathu. Mwa citsanzo, tinaphunzila kuti anthu ena angadzakhale na mpata wogwilizana na anthu a Mulungu ngakhale pambuyo pakuti Babulo Wamkulu wawonongedwa. Tinauzidwanso kuti kuyambila mu November 2023, ofalitsa a Ufumu sadzafunikilanso kucitila lipoti zonse zimene amacita mu ulaliki. Kodi masinthidwe amenewa akupangitsa ulaliki wathu kukhala wosafunika kwenikweni, kapena wosafunikila cangu? M’pangono pomwe!
2. N’cifukwa ciyani tsiku lililonse likadutsa tifunika kuwonjezela cangu pa nchito yathu? (Maliko 13:10)
2 Tsiku lililonse likadutsa, tifunika kuwonjezela cangu cathu pa nchito yolalikila. Cifukwa ciyani? Cifukwa nthawi ikutha. Ganizilani zimene Yesu ananenelatu zokhudza nchito yolalikila m’masiku otsiliza. (Ŵelengani Maliko 13:10.) Malinga na uthenga wa Mateyu pa nkhani imeneyi, Yesu anakamba kuti uthenga wabwino udzalalikidwa pa dziko lonse kumene kuli anthu “mapeto” asanafike. (Mat. 24:14) Mawu akuti mapeto amatanthauza kuthelatu kwa dongosolo loipali la Satana. Yehova anaikilatu “tsiku . . . ndi ola” limene zinthu zimenezi zidzacitika. (Mat. 24:36; 25:13; Mac. 1:7) Tsiku lililonse limene ladutsa limatiyandikizitsa ku tsiku limenelo. (Aroma 13:11) Koma pakali pano tiyenela kupitiliza kulalikila mpaka mapeto adzafike.
3. N’ciyani cimatilimbikitsa kulalikila uthenga wabwino?
3 Pamene tikuganizila ulaliki wathu, tingacite bwino kudzisanthula na funso ili: N’cifukwa ciyani timalalikila uthenga wabwino? Kuyankha mwacidule, cikondi n’cimene cimatilimbikitsa. Zimene timacita pa nchito yolalikila zimaonetsa cikondi cathu pa uthenga wabwino, pa anthu, koma maka-maka pa Yehova na dzina lake. Tiyeni tikambilane zinthu zimenezi ciliconse pacokha.
TIMALALIKILA CIFUKWA COKONDA UTHENGA WABWINO
4. Kodi timacita bwanji tikamva nkhani yosangalatsa?
4 Kodi mukumbukila mmene munamvela mutamva nkhani yosangalatsa—monga kubadwa kwa mwana, kapena mutamva kuti nchito yapezeka imene munali kuifunitsitsa? N’zosacita kufunsa kuti nthawi yomweyo munauzako a m’banja lanu, komanso mabwenzi anu. Kodi si mmenenso zinacitikila kwa inu mutamva uthenga woposa ulionse—uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu?
5. Munamva bwanji mutamva uthenga wa coonadi kwa nthawi yoyamba? (Onaninso cithunzi.)
5 Kumbukilani mmene munamvela mutamva uthenga wa m’Baibo koyamba. Mwa zina zimene munaphunzila, munadziŵa kuti Atate wanu wa kumwamba amakukondani, komanso kuti amafuna mukhale m’banja la alambili ake. Munaphunzilanso kuti adzacotsapo zoŵaŵa na mavuto, komanso kuti muli na ciyembekezo codzaonananso na okondedwa anu amene anamwalila m’dziko latsopano. (Maliko 10:29, 30; Yoh. 5:28, 29; Aroma 8:38, 39; Chiv. 21:3, 4) Mfundo za coonadi zimenezi zinakufikani pa mtima. (Luka 24:32) Munakonda zimene munali kuphunzila, ndipo munafunitsitsa kuuzako munthu aliyense zimenezo!—Yelekezelani na Yeremiya 20:9.
6. Mwaphunzila ciyani pa nkhani ya Ernest na Rose?
6 Ganizilani cocitika ca m’bale Ernest b amene anataikilidwa atate ake mu imfa ali na zaka 10. Iye anati: “N’nali kudzifunsa kuti: ‘Kodi anapita kumwamba? Kodi sadzabwelanso?’ N’nali kukhumbila kuona anzanga ali na atate awo.” Ernest nthawi zambili anali kupita ku manda, n’kugwada pa manda a atate ake, na kupemphela kuti: “Conde Mulungu, nifuna kudziŵa kumene atate ali.” Patapita zaka 17 cimwalilileni atate ake, Ernest anapemphedwa kuti aziphunzila Baibo, ndipo anavomela. Anasangalala kudziŵa kuti akufa sadziŵa ciliconse monga munthu ali m’tulo tofa nato, komanso kuti Baibo imalonjeza za kuuka kwa akufa. (Mlal. 9:5, 10; Mac. 24:15) Pamapeto pake anapeza mayankho pa mafunso amene anamuvutitsa maganizo kwa nthawi yaitali! Ernest anasangalala na mfundo za coonadi zimene anali kuphunzila. Nayenso mkazi wake, Rose, anayamba kuphunzila Baibo, ndipo anakonda zimene anali kuphunzila. Iwo anabatizika mu 1978. Iwo anali kulalikila mokangalika zinthu za mtengo wapatali zimene anali kukhulupilila kwa a m’banja lawo, mabwenzi awo, komanso aliyense amene akanamvetsela. Zotsatila zake n’zakuti, pofika pano Ernest na Rose athandiza anthu oposa 70 kupita patsogolo mpaka kubatizika.
7. Timasonkhezeleka kutani coonadi ca m’Baibo cikazika mizu m’mitima yathu? (Luka 6:45)
7 Kunena zoona, coonadi ca m’Baibo cikazika mizu m’mitima yathu sitingaleke kulalikila. (Ŵelengani Luka 6:45.) Timamva monga anamvela ophunzila a Yesu a m’zaka za zana loyamba pomwe anati: “Ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.” (Mac. 4:20) Coonadi timacikonda ngako moti timafuna kugaŵilako anthu ambili mmene tingathele.
TIMALALIKILA CIFUKWA COKONDA ANTHU
8. N’ciyani cimatisonkhezela kuuzako ena uthenga wabwino? (Onani bokosi lakuti “ Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila.”) (Onaninso cithunzi.)
8 Timakonda anthu mmene Yehova na Yesu amacitila. (Miy. 8:31; Yoh. 3:16) Timawamvela cisoni kwambili anthu amene sadziŵa “Mulungu,” komanso amene alibe “ciyembekezo.” (Aef. 2:12) Zili ngati anagwela m’dzenje lalitali, ndipo ife tili na nthambo yowathandiza kutulukamo—uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Cikondi na cifundo cimene tili naco pa anthu amenewa, cimatisonkhezela kucita zonse zotheka kuti tiwauzeko uthenga wabwino. Uthenga wa mtengo wapatali umenewu umawapatsa ciyembekezo, kuwathandiza kukhala na umoyo wabwino pali pano, komanso kuwapatsa ciyembekezo codzakhala na “moyo weniweniwo”—moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu.—1 Tim. 6:19.
9. Timacenjeza ciyani za m’tsogolo? Ndipo cifukwa ciyani? (Ezekieli 33:7, 8)
9 Cikondi cathu pa anthu cimatisonkhezela kuwacenjeza za mapeto a dziko loipali omwe ayandikila. (Ŵelengani Ezekieli 33: 7, 8.) Timawamvela cisoni anthu ena komanso acibale athu osakhulupilila. Ambili amangokhala osadziŵa kuti kutsogolo kukubwela “cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka lelo, ndipo sicidzacitikanso.” (Mat. 24:21) Tifuna adziŵe kuti panthawi ya ciweluzo, cipembedzo conyenga cidzacotsedwapo, kenako dongosolo loipali la zinthu lidzawonongedwa pa Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16; 17:16, 17; 19:11, 19, 20) Pemphelo lathu n’lakuti anthu ambili alabadile cenjezo limeneli na kugwilizana nafe pa kulambila koona pali pano. Nanga bwanji za anthu amene sakulabadila cenjezo lathu pali pano, kuphatikizapo acibale athu okondeka?
10. N’cifukwa ciyani sitiyenela kucepetsa cangu ca kucenjeza anthu?
10 Monga tinafotokozela m’nkhani yapita, n’kutheka kuti Yehova angadzapulumutse anthu amene adzayambe kuonetsa cikhulupililo mwa iye ataona kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Conco, tiyenela kuwonjezela cangu cathu pocenjeza anthu za ciwonongeko cimene cikubwela. Ganizilani izi: Zimene tikuwauza pali pano, zidzawathandiza akadzazikumbukila panthawiyo. (Yelekezelani na Ezekieli 33:33.) Iwo angadzakumbukile cenjezo limene anamva kwa ife, ndipo izi zingadzawasonkhezele kugwilizana nafe pa kulambila koona nthawi isanathe. Woyang’anila ndende wa ku Filipi anasintha mtima wake pambuyo poona “civomezi camphamvu.” Mofananamo, mwina ena amene sakulabadila uthenga wathu pali pano angadzasinthe mitima yawo podzaona cocitika cimene cidzagwedeze dziko lonse. Cocitikaco, ndico kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu.—Mac. 16:25-34.
TIMALALIKILA CIFUKWA COKONDA YEHOVA NA DZINA LAKE
11. Kodi Yehova timam’patsa bwanji ulemelelo, ulemu na mphamvu? (Chivumbulutso 4:11) (Onaninso cithunzi.)
11 Cifukwa copambana cimene timalalikila uthenga wabwino n’cakuti timamukonda Yehova Mulungu na dzina lake loyela. Timaona ulaliki wathu monga njila imene timatamandila Mulungu amene timam’konda. (Ŵelengani Chivumbulutso 4:11.) Timavomeleza na mtima kuti Yehova Mulungu ni woyenela kulandila ulemelelo, ulemu, na mphamvu kwa alambili ake okhulupilika. Timam’patsa ulemelelo na ulemu tikamauzako ena umboni wosatsutsika wakuti ‘analenga zinthu zonse’ komanso kuti tilipo cifukwa ca iye. Timam’patsa mphamvu—mphamvu zathu—tikamaseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso zinthu zathu potengako mbali mokwanila m’nchito yolalikila malinga na mmene zinthu zilili kwa ife. (Mat. 6:33; Luka 13:24; Akol. 3:23) Mwacidule, tinganene kuti timakonda kukamba za Mulungu amene timakonda. Timalimbikitsidwanso kuuzako ena za dzina lake komanso zimene limatanthauza. Cifukwa ciyani?
12. Kodi timaliyeletsa motani dzina la Yehova mu ulaliki?
12 Cikondi cathu pa Yehova cimatilimbikitsa kuyeletsa dzina lake. (Mat. 6:9) Timafuna kutengapo gawo pa nchito yoyeletsa dzina la Mulungu ku citonzo cimene Satana wabweletsa pa dzinalo cifukwa ca mabodza ake oipa. (Gen. 3:1-5; Yobu 2:4; Yoh. 8:44) Tikakhala mu ulaliki, timakhala ofunitsitsa kumukhalila kumbuyo Mulungu wathu, na kuuzako amene afuna kumvetsela coonadi cokhudza iye. Tifuna kuti munthu aliyense adziŵe kuti khalidwe lake lalikulu ni cikondi, komanso kuti amalamulila mwacilungamo. Tifunanso kuti adziŵe kuti posacedwa, Ufumu wake udzathetsa mavuto onse na kubweletsa mtendele, komanso cimwemwe kwa anthu onse. (Sal. 37:10, 11, 29; 1 Yoh. 4:8) Tikawadziŵitsa zimenezi, timayeletsa dzina lake. Timakhalanso okhutila tikadziŵa kuti timacita zinthu mogwilizana na dzina lathu. Motani?
13. N’cifukwa ciyani timanyadila kuchedwa Mboni za Yehova? (Yesaya 43:10-12)
13 Yehova anatisankha kukhala “mboni” zake. (Ŵelengani Yesaya 43:10-12.) Zaka zingapo kumbuyoku, kalata ina ya Bungwe Lolamulila inanena kuti: “Mwayi waukulu koposa umene aliyense wa ife angakhale nawo ni wodziŵika kuti Mboni ya Yehova.” c Tikutelo cifukwa ciyani? Ganizilani citsanzo ici. Mutafuna kusankha munthu kuti akhale mboni yanu m’khoti, mungasankhe munthu amene mum’dziŵa na kum’khulupilila, amenenso ali na mbili yabwino, imene ingacititse kuti anthu ena am’khulupilile. Potisankha kukhala Mboni zake, Yehova waonetsa kuti amatidziŵa bwino komanso kuti amatidalila kuti tipeleke umboni wakuti iye yekhayo ndiye Mulungu woona. Timaona kuti kukhala Mboni zake ni mwayi waukulu moti timaseŵenzetsa mpata ulionse kudziŵitsa anthu za dzina lake na kutsutsa mabodza onse amene anenedwa okhudza iye. Mwa kutelo, timakhala umoyo wogwilizana na dzina limene timanyadila ngako kudziŵika nalo, lakuti Mboni za Yehova!—Sal. 83:18; Aroma 10:13-15.
TIDZAPITILIZABE KULALIKILA MPAKA MAPETO
14. Ni zinthu zosangalatsa ziti zimene zidzacitika posacedwa?
14 Timayembekezela mwacidwi zinthu zimene zidzacitika posacedwa! Na dalitso la Yehova, tili na ciyembekezo cakuti anthu ambili adzalandila coonadi cisautso cacikulu cisanayambe. Cina, n’zosangalatsa ngako kuti pali kuthekela kwakuti ngakhale panthawi yovuta kwambili m’mbili yonse ya anthu—pa cisautso cacikulu—tingadzaone anthu ambili akucoka ku dziko la Satana limene latsala pang’ono kuwonongedwa na kugwilizana nafe pa kutamanda Yehova!—Mac. 13:48.
15-16. Kodi sitidzaleka kucita ciyani? Ndipo mpaka liti?
15 Koma pakali pano, tili na nchito yoti tigwile. Tili na mwayi wogwilako nchito imene siidzacitikanso—nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu padziko lonse. Koma panthawi imodzimodzi, tiyenela kupitiliza kupeleka cenjezo pa zimene zidzacitika posacedwa. Anthu ayenela kudziŵa kuti dongosolo la zinthu loipali latsala pang’ono kutha. Ndiyeno, nthawi ya ciweluzo ikadzafika, iwo adzadziŵa kuti uthenga wathu unali wocokela kwa Yehova Mulungu.—Ezek. 38:23.
16 Kodi tsopano ndife ofunitsitsa kucita ciyani? Cifukwa cokonda uthenga wabwino, anthu, koma maka-maka Yehova na dzina lake, sitidzaleka kulalikila mofunitsitsa, mwacangu, komanso mokangalika mpaka Yehova adzatiuze kuti, “kwatha!”
NYIMBO 54 “Njila ni Iyi”
a Msonkhano wa pacaka unacitika pa October 7, 2023, m’bwalo la Misonkhano la Mboni za Yehova ku Newburgh m’dziko la America. Pulogalamu yonse inaonetsedwa pa JW Broadcasting®—Mbali 1 mu November 2023, Mbali 2 mu January 2024.
b Onani nkhani yakuti “Baibulo Limasintha Anthu—Ndinasangalala ndi Mayankho Omveka Bwino a m’Baibulo,” mu Nsanja ya Mlonda ya March 1, 2015.
c Onani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2007, tsamba 3.