Khalani na Cikhulupililo m’Malonjezo a Yehova
“Cikhulupililo ndico . . . umboni wooneka wa zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.”—AHEB. 11:1.
1. Kodi cikhulupililo ca Mkhiristu tiziciona bwanji?
CIKHULUPILILO ca Mkhiristu ni khalidwe la mtengo wapatali kwambili. Si anthu onse ali nalo. (2 Ates. 3:2) Komabe, Yehova wapatsa mlambili wake aliyense “cikhulupililo.” (Aroma 12:3; Agal. 5:22) Conco, onse amene ali na cikhulupililo afunika kuyamikila ngako.
2, 3. (a) Kodi munthu amene ali na cikhulupililo adzalandila madalitso yabwanji? (b) Ni mafunso yanji amene tiyamba kukambilana?
2 Yesu Khiristu anakamba kuti Atate wake wakumwamba amakoka anthu kupitila mwa Mwana Wake. (Yoh. 6:44, 65) Conco, kukhala na cikhulupililo mwa Yesu kumacititsa munthu kukhululukiwa macimo. Ndipo izi zimacititsa munthu kukhala na mwayi wokhala paubwenzi na Yehova kwamuyaya. (Aroma 6:23) Kodi pali cimene tinacita kuti tilandile dalitso limenelo? Ife tonse ndife ocimwa, conco tinali oyenelela kufa. (Sal. 103:10) Koma Yehova anaona zabwino mwa ife. Ndipo cifukwa ca cisomo cake, anatsegula mitima yathu kuti tilandile uthenga wabwino. Conco, tinayamba kuonetsa cikhulupililo mwa Yesu. Tinakhalanso na mwayi wodzalandila moyo wosatha.—Ŵelengani 1 Yohane 4:9, 10.
3 Koma kodi cikhulupililo n’ciani kweni-kweni? Kodi cimatanthauza cabe kuvomeleza kuti Mulungu adzatipatsadi zimene walonjeza? Ndipo koposa zonse, tingaonetse bwanji cikhulupililo?
KHULUPILILA MUMTIMA MWAKO
4. Fotokozani cifukwa cake cikhulupililo si maganizo cabe.
4 Cikhulupililo cimaloŵetsamo zambili osati cabe kungomvetsa colinga ca Mulungu. Cikhulupililo ni mphamvu imene imasonkhezela munthu kucita zinthu zogwilizana na cifunilo ca Mulungu. Kukhala na cikhulupililo mwa Yesu amene ni njila ya Mulungu yotipulumutsila, kumasonkhezela wokhulupilila kuuzako ena uthenga wabwino. Paulo anafotokoza kuti: “Pakuti ngati ukulengeza kwa anthu ‘mau amene ali m’kamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndiye Ambuye, ndipo mumtima mwako ukukhulupilila kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. Munthu amakhala ndi cikhulupililo mumtima mwake kuti akhale wolungama, koma ndi pakamwa pake amalengeza poyela cikhulupililo cake kuti apulumuke.”—Aroma 10:9, 10; 2 Akor. 4:13.
5. N’cifukwa ciani cikhulupililo n’cofunika? Nanga tingacite ciani kuti cikhalebe colimba? Pelekani citsanzo.
5 Ciyembekezo cathu codzakhala ndi moyo wosatha m’dziko latsopano la Mulungu, cidalila pa kukhala na cikhulupililo colimba ndi kucisunga. Kukhala na cikhulupililo colimba tingakuyelekezele na mmene maluŵa amafunila madzi. Mosiyana na maluŵa opanga, maluŵa eni-eni amasintha. Iwo angafote kapena kufa kumene ngati sathiliwa madzi. Koma angaphukile ngati asamalidwa bwino. Ni mmene cikhulupililo cathu cilili. Cingafooke na kufa ngati siticilimbitsa. (Luka 22:32; Aheb. 3:12) Koma ngati ticiikako nzelu, cikhulupililo cathu cidzapitiliza “kukula,” cakuti tidzakhala “acikhulupililo colimba.”—2 Ates. 1:3; Tito 2:2.
MMENE BAIBO IMAFOTOKOZELA CIKHULUPILILO
6. Kodi Aheberi 11:1 imafotokoza cikhulupililo m’njila ziŵili ziti?
6 Lemba la Aheberi 11:1 (ŵelengani) limafotokoza bwino zimene cikhulupililo cimatanthauza. Cikhulupililo cimazikika pa zinthu ziŵili zimene sitingaone: (1) “zinthu zoyembekezeledwa.” Izi ziphatikizapo zinthu zimene Mulungu anatilonjeza kuti zidzacitika kutsogolo, koma zikalibe kucitika. Zinthu monga kucotsedwapo kwa zoipa zonse ndi kubwela kwa dziko latsopano. (2) “Zinthu zenizeni, ngakhale kuti n’zosaoneka.” Apa, liu la Cigiriki lomasulidwa kuti “umboni wooneka,” limatanthauza “umboni wokhutilitsa” wa zinthu zenizeni zosaoneka. Zinthuzo zimaphatikizapo kukhalako kwa Yehova Mulungu, Yesu Khiristu, angelo, komanso zocitika za Ufumu wa kumwamba. (Aheb. 11:3) Kodi tingaonetse bwanji kuti ciyembekezo cathu n’camoyo, ndi kuti timakhulupililadi zinthu zosaoneka zochulidwa m’Mau a Mulungu? Tingaonetse mwa zokamba ndi zocita zathu. Apo ayi, ndiye kuti cikhulupililo cathu sicokwanila.
7. Kodi citsanzo ca Nowa citithandiza bwanji kumvetsetsa zimene kukhala na cikhulupililo kumatanthauza? (Onani pikica kuciyambi kwa nkhani ino.)
7 Lemba la Aheberi 11:7 imakambapo za cikhulupililo ca Nowa, amene “atacenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke, anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga cingalawa kuti banja lake lipulumukilemo.” Pamene Nowa anamanga cingalawa, anaonetsa kuti anali na cikhulupililo. Mosakaikila, aneba ake anali kum’funsa cifukwa cake anali kupanga combo cacikuluco. Kodi nowa anangokhala zii kapena anali kuwauza kuti ‘aliyense adziŵe zake?’ Ai ndithu. Cikhulupililo cake cinam’limbikitsa kuwalalikila molimba mtima, na kuwacenjeza za ciweluzo cimene Mulungu anali kubweletsa. N’kutheka kuti Nowa anali kuuza anthu mobweleza-bweleza mau amene Yehova anamuuza akuti: “Nthawi yafika yakuti ndiwononge anthu onse, popeza dziko lapansi ladzaza ndi ciwawa cifukwa ca iwo . . . ndidzabweletsa cigumula camadzi padziko lapansi, kuti ciwononge camoyo ciliconse ca pansi pa thambo, cimene cili ndi mphamvu ya moyo m’thupi mwake. Ciliconse ca m’dziko lapansi cidzafa.” Ndiponso, n’zosakayikitsa kuti Nowa anafotokozela anthu njila imene ingawapulumutse mwa kuwauza lamulo la Mulungu lakuti: “Udzaloŵe m’cingalawaco.” Kuwonjezela apo, Nowa anaonetsanso cikhulupililo cake mwa kukhala “mlaliki wa cilungamo.”—Gen. 6:13, 17, 18; 2 Pet. 2:5.
8. N’ciani cimene wophunzila Yakobo anafotokoza pokamba za cikhulupililo ca Mkhiristu woona?
8 Zioneka kuti buku la Yakobo inalembedwa patapita nthawi yocepa Paulo atalemba za cikhulupililo. Monga Paulo, Yakobo anafotokoza kuti cikhulupililo ca Mkhiristu woona sicikhala copanda nchito. Anati: “Undionetse cikhulupililo cako popanda nchito zake, ndipo ine ndikuonetsa Yak. 2:18) Yakobo anaonetsanso kusiyana pakati pa kungokhulupilila zinthu ndi kuonetsa cikhulupililo. Viŵanda vimadziŵa kuti Mulungu aliko koma vilibe cikhulupililo mwa iye. M’malo mwake, vimacita nchito zoipa kuti cifuno ca Mulungu cisakwanilitsike. (Yak. 2:19, 20) Komabe, pokamba za munthu wina wakale wa cikhulupililo, Yakobo anafunsa kuti: “Kodi Abulahamu atate wathu sanayesedwe wolungama cifukwa ca nchito zake, atapeleka Isaki mwana wake nsembe paguwa? Waonatu kuti cikhulupililo cake cinayendela limodzi ndi nchito zake, ndipo mwa nchito zakezo cikhulupililo cakeco cinakhala cangwilo.” Pofuna kumveketsa bwino mfundo yakuti cikhulupililo ciyenela kuonetsedwa mwa nchito zathu, Yakobo anati: “Monga mmene thupi lopanda mzimu limakhalila lakufa, naconso cikhulupililo copanda nchito zake ndi cakufa.”—Yak. 2:21-23, 26.
cikhulupililo canga mwa nchito.” (9, 10. Kodi mtumwi Yohane akutithandiza bwanji kumvetsetsa kufunika koonetsa cikhulupililo?
9 Patapita zaka zopitilila 30, mtumwi Yohane analemba buku ya Uthenga Wabwino ndi makalata atatu. Kodi iye anavomeleza zimene olemba Baibo ena anauzilidwa kulemba za tanthauzo la cikhulupililo ca Mkhiristu woona? Kuposa olemba onse a Baibo, Yohane anaseŵenzetsa velebu ya Cigiriki imene nthawi zina imamasulidwa kuti kuonetsa cikhulupililo.
10 Mwacitsanzo, Yohane anati: “Iye wokhulupilila mwa Mwanayo ali nawo moyo wosatha. Wosamvela Mwanayo sadzauona moyowu, koma mkwiyo wa Mulungu ukhalabe pa iye.” (Yoh. 3:36) Cikhulupililo ca Mkhiristu cimaphatikizapo kuonetsa kuti timamvela malamulo a Yesu. Kaŵili-kaŵili, Yohane anali kugwila mau a Yesu oonetsa kuti tifunika kuonetsa cikhulupililo nthawi zonse.—Yoh. 3:16; 6:29, 40; 11:25, 26; 14:1, 12.
11. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwayi wodziŵa coonadi?
11 Kukamba zoona, tiyenela kuyamikila kuti Yehova anaseŵenzetsa mzimu wake woyela kuti tiphunzile coonadi ndi kulabadila uthenga wabwino. (Ŵelengani Luka 10:21.) Tisaleke kumuyamikila Yehova potikokela kwa iye kupitila mwa Mwana wake, “Mtumiki Wamkulu ndi Wokwanilitsa cikhulupililo cathu.” (Aheb. 12:2) Kuti tionetse kuyamikila cisomo cake, tiyenela kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa kupemphela na kuphunzila Mau a Mulungu.—Aef. 6:18; 1 Pet. 2:2.
12. Kodi tingaonetse cikhulupililo m’njila ziti?
12 Tiyenela kumaonetsa kuti tili na cikhulupililo m’malonjezo a Yehova. Ndipo zimenezi zizionekela kwa anthu ena. Mwacitsanzo, tizilalikila za Ufumu wa Mulungu ndi kupanga ophunzila. Tizicitila “onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu m’cikhulupililo.” (Agal. 6:10) Ndiponso, tiziyesetsa ‘kuvula umunthu wakale pamodzi ndi nchito zake,’ zimene zingatifooketse mwauzimu.—Akol. 3:5, 8-10.
CIKHULUPILILO MWA MULUNGU NI MBALI YA MAZIKO ATHU
13. Kodi “cikhulupililo mwa Mulungu” n’cofunika bwanji? Nanga amaciyelekezela na ciani? Cifukwa?
13 Baibo imati: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6.) Mau a Mulungu amafotokoza kuti “cikhulupililo mwa Mulungu” ni “maziko” amene amafunika kuti munthu akhale Mkhiristu, ndi kuti apitilize kukhala Mkhiristu. (Aheb. 6:1) Pa maziko amenewo, Akhiristu ayenela “kuwonjezela pa cikhulupililo” cawo makhalidwe ofunika kuti ‘apitilize kucita zinthu zimene zingacititse Mulungu kuwakonda.’—Ŵelengani 2 Petulo 1:5-7; Yuda 20, 21.
14, 15. Cofunika kwambili n’citi pakati pa cikondi na cikhulupililo?
14 Akhiristu amene analemba Baibo anaonetsa kufunika kwa cikhulupililo mwa kucitomola kambili. Ngati pali khalidwe limene limachulidwa kaŵili-kaŵili m’Baibo, ni cikhulupililo. Kodi izi zitanthauza kuti cikhulupililo ndiye khalidwe lofunika kwambili pa makhalidwe a Akhiristu?
15 Polinganiza cikhulupililo na cikondi, Paulo analemba kuti: “Ngati ndili ndi cikhulupililo conse coti n’kusuntha naco mapili, koma ndilibe cikondi, sindili kanthu.” (1 Akor. 13:2) Yesu anaonetsa kuti kukonda Mulungu n’kofunika kwambili pamene anayankha funso lakuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?” (Mat. 22:35-40) M’cikondi muli makhalidwe ambili a Cikhiristu, kuphatikizapo cikhulupililo. ‘Cikondi cimakhulupilila zinthu zonse,’ imatelo Baibo. Ico cimakhulupilila zinthu zonse zimene Mulungu anakamba m’Mau ake a coonadi.—1 Akor. 13:4, 7.
16, 17. Kodi cikhulupililo na cikondi amazichula bwanji m’Malemba? Nanga ni khalidwe liti lalikulu kwambili pa aŵiliwa? Cifukwa?
16 Cifukwa cakuti cikhulupililo na cikondi zonse n’zofunika, Akhiristu olemba Baibo anawalembela pamodzi makhalidwe amenewa. Amapezeka kaŵili-kaŵili m’sentensi imodzi kapena m’ciganizo cimodzi. Mwacitsanzo, Paulo anacenjeza abale ake kuvala “codzitetezela pacifuwa cacikhulupililo ndi cikondi.” (1 Ates. 5:8) Nayenso Petulo analemba kuti: “Ngakhale kuti simunamuonepo [Yesu], mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupilila mwa iye.” (1 Pet. 1:8) Ngakhale Yakobo anafunsa abale ake odzozedwa kuti: “Mulungu anasankha anthu amene ali osauka m’dzikoli kuti akhale olemela m’cikhulupililo ndi olandila colowa ca ufumu umene anaulonjeza kwa omukonda, sanatelo kodi?” (Yak. 2:5) Naye Yohane analemba kuti: “Lamulo [la Mulungu] ndi lakuti, tikhale ndi cikhulupililo m’dzina la Mwana wake Yesu Khiristu ndiponso tizikondana.”—1 Yoh. 3:23.
17 Olo kuti cikhulupililo n’cofunika, cidzatha panthawi imene tidzaona kukwanilitsika kwa malonjezo a Mulungu ndi kuona kuti zimene tinali kuyembekezela zacitika. Koma kukulitsa cikondi kwa Mulungu ndi kwa anzathu sikudzatha. N’cifukwa cake Paulo anati: “Tsopano patsala zitatu izi: Cikhulupililo, ciyembekezo, cikondi. Koma cacikulu pa zonsezi ndi cikondi.”—1 Akor. 13:13.
UMBONI WAMPHAMVU WA CIKHULUPILILO
18, 19. Ni umboni uti wa cikhulupililo umene tiona masiku ano? Nanga n’ndani ayenela kulemekezedwa cifukwa ca izi?
18 Masiku ano, anthu a Yehova akhala akuonetsa cikhulupililo cawo mu Ufumu wa Mulungu. Izi zacititsa kuti kukhale paradaiso wauzimu wa padziko lapansi umene uli na nzika zoposa 8 miliyoni. M’paradaiso wauzimu ameneyu ni modzala na makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Ha! Ukulilenji umboni woonetsa cikhulupililo na cikondi ceni-ceni ca Akhiristu!
19 Palibe munthu amene ayenela kulemekezedwa cifukwa ca izi. Mulungu wathu ndiye wacititsa kuti paradaiso wauzimu akule. Nchito yapadela imeneyi ‘ikuchukitsa Yehova, ndipo ni cizindikilo coti sicidzacotsedwa mpaka kalekale.’ (Yes. 55:13) Zoona, ni “mphatso ya Mulungu” kuti ‘tizapulumutsidwa kudzela m’cikhulupililo.’ (Aef. 2:8) Anthu m’paradaiso wathu wauzimu adzapitiliza kuculuka mpaka dziko lonse likadzale na anthu angwilo, acilungamo, ndi acimwemwe kuti dzina la Yehova likatamandike kwamuyaya. Tiyeni tipitilize kukhala na cikhulupililo m’malonjezo a Yehova.