Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khalani Wodzicepetsa ndi Wacifundo Monga Yesu

Khalani Wodzicepetsa ndi Wacifundo Monga Yesu

“Kristu anavutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiyilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.”—1 PET. 2:21.

1. Kodi kutengela zocita za Yesu kudzatithandiza bwanji kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova?

NTHAWI zambili, timakonda kutengela zocita za anthu amene timakonda. Pa anthu onse amene anakhalapo padziko lapansi, Yesu Kristu ndiye munthu wofunika kwambili kumutsatila. N’cifukwa ciani tikutelo? Panthawi ina, Yesu mwini anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Yesu anatengela kwambili umunthu wa Atate wake cakuti tikamaphunzila za iye timakhala ngati tikuphunzila za Yehova. Motelo, kutengela zocita za Yesu kudzatithandiza kukhala paubwenzi wolimba ndi Yehova, amene ndi wamkulu mu cilengedwe conse. Umenewu ndi mwai wamtengo wapatali.

2, 3. (a) N’cifukwa ciani Yehova anatifotokozela bwino kwambili za umoyo wa Yesu m’Baibulo? Nanga Yehova afuna kuti ticite ciani? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino ndiponso yotsatila?

2 Nanga tingamudziŵe bwanji Yesu? Baibulo limafotokoza bwino kwambili ponena za Yesu. Zili telo cifukwa cakuti Yehova amafuna kuti timudziŵe bwino Mwana wake kotelo kuti titengele makhalidwe ake. (Ŵelengani 1 Petulo 2:21.) Baibulo limayelekezela citsanzo cimene Yesu anasiya ndi  “mapazi,” kapena zidindo za mapazi. M’mau ena, Yehova akutiuza kuti tizitsatila Yesu ndi kuponda mapazi athu pamene iye anaponda. N’zoona kuti Yesu anali munthu wangwilo ndipo Yehova sayembekezela kuti titengele Mwana wake mwangwilo. Koma Mulungu amafuna kuti tizitsatila Mwana wake mmene tingathele.

3 Tsopano tiyeni tikambilane makhalidwe ena a Yesu ocititsa cidwi. M’nkhani ino, tidzakambilana za kudzicepetsa ndi cifundo. Ndiyeno m’nkhani yotsatila, tidzakambilana za kulimba mtima ndi kuzindikila. Pa khalidwe lililonse, tidzakambilana mafunso atatu otsatilawa: Kodi khalidwe ili limatanthauza ciani? Kodi Yesu anaonetsa bwanji khalidwe limeneli? Nanga tingatengele bwanji citsanzo cake?

YESU NDI WODZICEPETSA

4. Kodi kudzicepetsa kumatanthauza ciani?

4 Kodi kukhala wodzicepetsa kumatanthauza ciani? Anthu ambili onyada amaganiza kuti kudzicepetsa ndi kukhala wopola kapena wodzikaikila. Koma kodi zimenezo n’zoona? Kunena zoona, kuti munthu akhale wodzicepetsa afunika kukhala wolimba mtima. Kukhala wodzicepetsa kumatanthauza kupewa kudzikuza kapena kunyada. Kuti tikhale odzicepetsa, tiyenela kuziona moyenela. Mwacitsanzo, dikishonale ina inati “kukhala wodzicepetsa kumatanthauza kuziona kuti ndife acabecabe pa maso pa Mulungu.” Ngati ndife odzicepetsadi, tidzapewanso kuganiza kuti ndife oposa anzathu. (Rom. 12:3) N’zovuta kuti anthu opanda ungwilo akhale odzicepetsa. Koma kukumbukila mmene timaonekela pa maso pa Mulungu ndi kutsatila mapazi a Mwana wake kungatithandize kukhala odzicepetsa.

5, 6. (a) Kodi Mikayeli ndani? (b) Kodi Mikayeli anaonetsa bwanji kuti ndi wodzicepetsa?

5 Kodi Yesu anaonetsa bwanji kudzicepetsa? Mwana wa Mulungu wakhala akuonetsa kuti ndi wodzicepetsa kuyambila ali kumwamba monga colengedwa cauzimu, ndiponso panthawi imene anali padziko lapansi monga munthu wangwilo. Tiyeni tikambilane zitsanzo zoŵelengeka.

6 Khalidwe lake. Wolemba Baibulo Yuda analemba za kudzicepetsa kwa Yesu asanabwele padziko lapansi. (Ŵelengani Yuda 9.) Pokhala Mikayeli mkulu wa angelo, Yesu “anasemphana maganizo ndi Mdyerekezi ndipo anakangana” ndi woipayo. Nkhani yake inali yokhudza “mtembo wa Mose.” Kumbukilani kuti pamene Mose anamwalila, Yehova anaika mtembo wake m’manda amene palibe akudziŵa. (Deut. 34:5, 6) Mwina Mdyelekezi anali kufuna kuyesa Aisiraeli kuti agwilitsile nchito mtembo wa Mose pa kulambila konyenga. Kaya colinga ca Mdyelekezi cinali cotani, Mikayeli molimba mtima anam’kaniza Mdyelekezi. Buku lina linakamba kuti mau akuti “anasemphana maganizo” ndi akuti “anakangana,” amagwilitsidwanso nchito pofotokoza “kukangana kumene kumakhala m’khoti,” ndipo zimenezi zikusonyeza kuti “Mikayeli ‘sanalole Mdyelekezi’ kutenga mtembo wa Mose.” Koma Mkulu wa Angelo anadziŵa kuti mphamvu zake zili ndi polekezela. Conco, anapeleka mlandu umenewu kwa Woweluza wa Mkulu, Yehova, amene ali ndi mphamvu zonse zoweluza Satana. Apa Yesu anaonetsa kuti ndi wodzicepetsa kwambili.

7. Kodi mau ndi zocita za Yesu zinaonetsa bwanji kuti ndi wodzicepetsa?

7 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti ndi wodzicepetsadi mwa mau ake ndi zocita zake. Mau ake. Iye sanali kufuna kuti anthu azimutama. Koma  anali kufuna kuti ulemelelo wonse uzipita kwa Atate wake. (Maliko 10:17, 18; Yoh. 7:16) Yesu sanali kulankhula ndi ophunzila ake m’njila yowapangitsa kuzimva kuti ndi acabecabe kapena otsika kwambili. M’malo mwake, iye anali kuwalemekeza, kuwayamikila pa zabwino zimene anali kucita, ndi kuwaonetsa kuti amawakhulupilila. (Luka 22:31, 32; Yoh. 1:47) Zocita zake. Yesu anasankha kukhala umoyo wosalila zambili. (Mat. 8:20) Iye anadzipeleka kugwila nchito zotsika. (Yoh. 13:3-15) Anaonetsa kuti ndi wodzicepetsa mwa kukhala womvela. (Ŵelengani Afilipi 2:5-8.) Mosiyana ndi anthu odzikuza amene amakana kukhala omvela, Yesu modzicepetsa anagonjela kucita cifunilo ca Mulungu ndipo anakhala “womvela mpaka imfa.” Motelo, n’zoonekelatu kuti Yesu, Mwana wa munthu, anali “wodzicepetsa.”—Mat. 11:29.

KHALANI WODZICEPETSA MONGA YESU

8, 9. Tingaonetse bwanji kuti ndife odzicepetsa?

8 Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pankhani yokhala wodzicepetsa? Zocita zathu. Ngati ndife odzicepetsa, tidzazindikila kuti tilibe ulamulilo wonse. Ngati tikumbukila kuti tilibe mphamvu zoweluza ena, sitidzawasuliza kapena kukaikila zolinga zao. (Luka 6:37; Yak. 4:12) Kudzicepetsa kudzatithandiza kupewa kukhala “wolungama mopitilila muyezo,” ndi kunyoza anthu ena amene alibe maluso kapena maudindo amene tili nao. (Mlal. 7:16) Akulu odzicepetsa samaona kuti amaposa Akristu ena. M’malo mwake amaona ena kukhala owaposa ndipo amakhala ngati wamng’ono.—Afil. 2:3; Luka 9:48.

9 Ganizilani za m’bale Walter J. Thorn, amene anali woyang’anila woyendela kuyambila mu 1894. Atagwila nchitoyo kwa zaka zambili, anapemphedwa kukagwila nchito m’khola la nkhuku pa famu yochedwa Kingdom Farm, ku New York. Iye anati: “Ndikayamba kuganiza molakwika ponena za nchito imene ndinapatsidwa, ndimangoziuza kuti: ‘Iwe fumbi lacabecabe, uli ndi ciani conyadila?’” (Ŵelengani Yesaya 40:12-15.) Ndithudi, iye analidi wodzicepetsa.

10. Tingaonetse bwanji kuti ndife odzicepetsa mwa mau ndi zocita zathu?

10 Mau athu. Ngati ndife odzicepetsa, mau athu adzaonetsa zimenezo. (Luka 6:45) Pokambilana ndi ena, tidzapewa kukamba kwambili pa zinthu zimene tacita ndi maudindo amene tili nao. (Miy. 27:2) M’malo mwake, tidzayesetsa kuona zabwino mwa abale ndi alongo athu, ndi kuwayamikila pa makhalidwe ao abwino, maluso ao, ndi zimene akwanitsa kucita paumoyo wao. (Miy. 15:23) Zocita zathu. Akristu odzicepetsa amapewa kufuna kukhala ochuka m’dziko lino. Iwo amasankha kukhala ndi umoyo wosalila zambili, ndi kugwila nchito imene dzikoli limaona kuti ndi yotsika kwambili. Amacita zimenezi kuti akwanitse kutumikila Yehova mmene angathele. (1 Tim. 6:6, 8) Koposa zonse, tingaonetse kuti ndife odzicepetsa mwa kukhala omvela. Kudzicepetsa n’kofunika kuti ‘tizimvela amene akutsogolela’ mumpingo ndi kutsatila malangizo amene gulu la Yehova limapeleka.—Aheb. 13:17.

YESU NDI WACIFUNDO

11. Kodi kukhala wacifundo kumatanthauza ciani?

11 Kodi kukhala wacifundo kumatanthauza ciani? Munthu wacifundo amasonyeza kuti ali ndi cikondi. Baibulo limakamba kuti Yehova ndi Yesu amaonetsa cifundo ndi cikondi cacikulu. (Luka 1:78; 2 Akor. 1:3; Afil. 1:8) Buku  lina lofotokoza Baibulo linati: “Kuonetsa cifundo kumafuna zambili kuposa kungomvela cisoni anthu osoŵa.” Linafotokoza kuti kukhala wacifundo kumatanthauza “kukhuzika mtima ndi kupeleka thandizo” kwa ovutikawo. Cifundo ndi khalidwe limene limasonkhezela munthu kuthandiza ena kuti akhale ndi umoyo wabwino.

12. N’ciani cionetsa kuti Yesu anali kumvela cifundo ena? Nanga cifundo cinam’limbikitsa kucita ciani?

12 Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti ndi wacifundo? Cifundo ndiponso zocita zake. Yesu anali kumvela cifundo anthu ena. Ataona bwenzi lake Mariya ndi anthu ena akulila imfa ya Lazaro, Yesu “anagwetsa misozi.” (Ŵelengani Yohane 11:32-35.) Mosakaikila cifundo cimene cinam’cititsa kuukitsa mwana wa mkazi wamasiye, ndi cimene cinam’cititsanso kuukitsa Lazaro. (Luka 7:11-15; Yoh. 11:38-44) Cifundo cimene Yesu anaonetsa Lazaro mwa njila imeneyi, ciyenela kuti cinacititsa Lazaro kuti akhale ndi mwai wodzalandila moyo kumwamba. Nthawi ina izi zisanacitike, Yesu ‘anamvela cifundo’ khamu la anthu limene linabwela kwa iye. Cifukwa ca cifundo, iye “anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.” (Maliko 6:34) Anthu amene anatsatila ziphunzitso zake anasintha umoyo wao. Yesu sanali kungomvela ena cifundo, koma cifundo cinali kum’limbikitsa kuthandiza ena.—Mat. 15:32-38; 20:29-34; Maliko 1:40-42.

13. Kodi Yesu analankhula bwanji mwacifundo kwa ena. (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

13 Mau ake acifundo. Cifukwa ca cifundo, Yesu anali kulankhula ndi ena mokoma mtima makamaka ovutika. Mtumwi Mateyu anagwila mau a Yesaya ponena za Yesu kuti: “Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo cingwe ca nyale comwe catsala pang’ono kuzima sadzacizimitsa.” (Yes. 42:3; Mat. 12:20) Kodi mauwa akutanthauza ciani? Yesu sanali kuvutitsa anthu kapena kuwazunza. Koma anali kuwalimbikitsa ndi mau ake. Ndipo anali kulalikila uthenga wa ciyembekezo kwa “osweka mtima.” (Yes. 61:1) Iye anaitana onse “ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa” kupita kwa iye kuti ‘akatsitsimulidwe.’ (Mat. 11:28-30) Ndiyeno, anatsimikizila ophunzila ake kuti Mulungu anali kumvela cifundo wolambila Wake aliyense kuphatikizapo ‘tiana’ kutanthauza anthu amene dziko limaona kuti ndi osafunikila kwenikweni.—Mat. 18:12-14; Luka 12:6, 7.

KHALANI WACIFUNDO MONGA YESU

14. N’ciani cingatithandize kuti tizimvela ena cifundo?

14 Tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu pankhani yokhala wacifundo? Mtima wacifundo. Kuti munthu akhale wacifundo, khama ndi lofunika. N’cifukwa cake Baibulo limatilimbikitsa kuti tiyenela kuyesetsa kukhala ndi khalidwe limeneli. Kukhala ndi “cifundo cacikulu” ndi mbali ya umunthu watsopano umene Akristu onse ayenela kuvala. (Ŵelengani Akolose 3:9, 10, 12.) N’ciani cingakuthandizeni kuti muzimvela ena cifundo? Muyenela kufutukula mtima wanu. (2 Akor. 6:11-13) Muyenela kumvetsela mosamala kwambili wina akamakuuzani nkhawa zake. (Yak. 1:19) Kenako yelekezelani kuti ndinuyo, ndipo dzifunseni kuti: ‘Ndikanakhala kuti ndine, kodi ndikanamva bwanji? Nanga ndikanafuna kuti wina andicitile ciani?’—1 Pet. 3:8.

15. Tingathandize bwanji anthu amene ali monga bango lophwanyika kapena cingwe ca nyale comwe catsala pang’ono kuzima?

15 Zocita zathu zoonetsa cifundo. Kukhala wacifundo kudzatisonkhezela kuthandiza  anthu makamaka amene ali ngati bango lophwanyika, kapena cingwe ca nyale comwe catsala pang’ono kuzima. Nanga tingawathandize bwanji? Lemba la Aroma 12:15 limati: “Lilani ndi anthu amene akulila.” Kaŵilikaŵili, anthu opsinjika maganizo amafuna kungowaonetsa cifundo m’malo mowauza zocita. Mlongo wina amene anatonthozedwa ndi Akristu anzake mwana wake wa mkazi atamwalila anati: “Ndinali kuyamikila kwambili pamene anzanga ena anali kubwela kudzangolila nane basi.” Tingaonetsenso cifundo mwa kucitila anthu ena zinthu zabwino. Kodi pali mkazi wamasiye amene afuna kuti wina akamuthandize kukonza nyumba yake? Kodi pali wacikulile wina amene afunikila thandizo la mayendedwe popita ku misonkhano, muulaliki, ndi ku cipatala? Ngakhale titaonetsa mkristu mnzathu kukoma mtima pa mlingo wocepa, iye angasangalale kwambili. (1 Yoh. 3:17, 18) Koma njila yabwino kwambili yosonyezela ena cifundo ndi mwa kuwalalikila. Palibe njila ina yosonyezela cifundo anthu amene afuna kuphunzila Baibulo kuposa kuwalikila.

Kodi mumacitila cifundo abale anu mocokela pansi pamtima? (Onani ndime 15)

16. N’ciani cimene tingakambe kuti tilimbikitse a mtima wacisoni?

16 Mau athu acifundo. Kumvela ena cifundo kudzaticititsa ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wacisoni.’ (1 Ates. 5:14) N’ciani cimene tingakambe polimbikitsa anthu aconco? Tingawalimbikitse mwa kuwauza kuti timawakonda kwambili. Tingawayamikile mocokela pansi pamtima pa makhalidwe abwino ndi maluso amene ali nao. Tingawakumbutse kuti Yehova anawakokela kwa Mwana wake, ndipo ndi amtengo wapatali kwa iye. (Yoh. 6:44) Ndipo tingawatsimikizile kuti Yehova amawakonda kwambili atumiki ake a “mtima wosweka” kapena “odzimvela cisoni mumtima mwao.” (Sal. 34:18) Kulankhula mwa njila imeneyi kungalimbikitse aja amene akufunikila citonthozo.—Miy. 16:24.

17, 18. (a) Kodi Yehova amafuna kuti akulu azisamalila bwanji nkhosa zake? (b) Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Inu akulu, Yehova amafuna kuti muzicitila cifundo nkhosa zake. (Mac. 20:28, 29) Kumbukilani kuti ndi udindo wanu kuphunzitsa, kulimbikitsa, ndi kutsitsimula nkhosa zake. (Yes. 32:1, 2; 1 Pet. 5:2-4) Conco, mkulu wacifundo samalamulila abale ndi alongo, kupanga malamulo, kapena kuwapangitsa kudzimva kuti ali ndi mlandu mwa kuwakakamiza kucita zimene io sangakwanitse. M’malo mwake, iye amayesetsa kuwakondweletsa, ndi kukhulupilila kuti cikondi cao pa Yehova cidzawasonkhezela kum’tumikila mmene angathele.—Mat. 22:37.

18 Pamene tisinkhasinkha za makhalidwe a Yesu a kudzicepetsa ndi cifundo, timalimbikitsidwadi kupitiliza kutsatila mapazi ake. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana makhalidwe ena aŵili a Yesu ocititsa cidwi, omwe ndi kulimba mtima ndi kuzindikila.