Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tsanzilani Cikhulupililo Cao | Debora

“Ine Ndinauka Monga Mai mu Isiraeli”

“Ine Ndinauka Monga Mai mu Isiraeli”

DEBORA akuyang’ana asilikali amene asonkhana pamwamba pa Phili la Tabori. Iye akusangalala ndipo akulimbikitsidwa poona kulimba mtima ndi cikhulupililo ca asilikaliwo. Kutacha m’maŵa, iye anaganizila za kulimba mtima ndi cikhulupililo ca mtsogoleli wao Balaki. Kulimba mtima komanso cikhulupililo ca asilikaliwo cinali kudzayesedwa patsikuli ngakhale kuti anali 10,000 cabe. Iwo anali kudzamenyana ndi gulu lankhondo loopsa, anali ocepa komanso analibe zida za nkhondo zokwanila. Ngakhale n’telo, io anapitabe kunkhondo cifukwa ca cilimbikitso ca mkaziyu.

Ganizilani kuti mukuona Debora ndi Baraki akuyang’ana pamwamba pa Phili ndipo zovala zao zikuuluzika ndi mphepo yamphamvu. Phili la Tabori ndi lalikulu koma lafulati pamwamba pake. Munthu angathe kuona cigwa ca Esdraelon cimene cili pamtunda wa mamitala 400 kum’mwela cakumadzulo kwa Phili limenelo. Mtsinje wa Kisoni unali kudutsa cigwa cimeneci kuloŵela Kunyanja Yaikulu ku Phili la Karimeli. Mtsinjewo unalibe madzi patsikuli, koma cinthu cina cinali kunyezimila m’cigwa cimeneco. Gulu la nkhondo la Sisera linali kubwela ndipo zida zao zankhondo zinali kuwala kwambili. Gulu la nkhondo la Sisera linali la mphamvu, ndipo linali ndi magaleta 900 amene anali ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo ake. Sisera anafuna kuphelatu gulu la nkhondo la Aisiraeli mwamsanga ndi mosavuta monga mmene zimakhalila pokolola balele.

Debora anadziŵa kuti Baraki ndi gulu lake lankhondo akuyembekezela mau kapena cizindikilo kucokela kwa iye. Kodi anali yekha mkazi kumeneko? Nanga anamva bwanji kaamba ka udindo waukulu umene anali nao pa cocitika cimeneco? Kodi anacita mantha? Ai ndithu. Yehova Mulungu wake, ndi amene anamuuza kumenya nkhondo imeneyi, ndipo ananenelatu kuti mkazi ndi amene adzathetsa nkhondoyi. (Oweruza 4:9) Kodi kulimba mtima kwa Debora ndi amuna amenewa kukutiphunzitsa ciani ponena za cikhulupililo?

“MUKASONKHANE PAPHILI LA TABORI”

Baibulo limatiuza kuti Debora anali “mneneli wamkazi.” Zimenezi zinacititsa Debora kukhala wapadela m’nkhani za m’Baibulo, komabe sanali yekha. * Debora analinso ndi udindo wina. Iye anali kuweluza milandu m’malo mwa Yehova.—Oweruza 4:4, 5.

Debora anali kukhala pakati pa mzinda wa Rama ndi Beteli m’dela la maphili la Efuraimu. Iye anali kukhala patsinde pa mtengo wa kanjedza ndipo anali kutumikila anthu malinga ndi zigamulo zocokela kwa Yehova. Nchito yake inali yovuta kwambili, koma sinamucititse mantha. Nchito imene iye anali kucita inali yofunika kwambili. Pambuyo pake, anathandiza kupeka nyimbo yonena za kusakhulupilika kwa anthu ake kuti: “Anayamba kusankha milungu yatsopano. Atatelo m’pamene nkhondo inafika m’mizinda.” (Oweruza 5:8) Yehova anapeleka Aisiraeli m’manja mwa adani ao, cifukwa anayamba kutumikila milungu ina. Mfumu yacikanani dzina lake Yabini anayamba kuwalamulila kudzela mwa mkulu wa asilikali, Sisera.

Ku Isiraeli, anthu akamva dzina lakuti Sisera anali kucita mantha kwambili. Cipembedzo ndi cikhalidwe ca Akanani cinali cankhanza, anali kupeleka ana nsembe ndipo anali kucita ciwelewele pakacisi. Nanga zinthu zinali bwanji pamene Sisera ndi asilikali ake anali kulamulila dziko? Nyimbo ya Debora imafotokoza kuti kuyenda m’njila kunali kovuta ndipo panalibe aliyense amene anali kukhala m’midzi. (Oweruza 5:6, 7) Anthu anali kubisala m’nkhalango ndi m’maphiri. Iwo sanali kulima ndipo anacita mantha kukhala m’midzi yopanda citetezo ndiponso sanali kuyenda pamseu kuopa kuti ana ao angatengedwe ndipo akazi ao angagwililidwe. *

Anapitiliza kukhala mwamantha kwa zaka 20 kufikila pamene Yehova anaona kuti anthu ake ouma khosi anali kufuna kusintha. Nyimbo youzilidwa ya Debora ndi Baraki imati: “Kufikila pamene ine Debora ndinauka, kufikila pamene ine ndinauka monga mai mu Isiraeli.” Sitikudziŵa ngati Debora mkazi wa Lapidoti anali ndi ana, koma cimene tikudziŵa n’cakuti mau amenewa ndi ophiphilitsa. Yehova anapatsa udindo Debora woteteza mtunduwo monga mmene mai amatetezela mwana wake. Yehova anacititsa Debora kulimbikitsa ndi kutsogolela woweluza Baraki, munthu wa cikhulupililo, kukamenyana ndi Sisera.—Oweruza 4: 3, 6,  7; 5:7.

Debora analimbikitsa Baraki kuti apulumutse anthu a Mulungu

Kudzela mwa Debora, Yehova analamula kuti: “Mukasonkhane paphili la tabori.” Baraki anafunika kusonkhanitsa amuna 10,000 kucokela m’mafuko aŵili a Isiraeli. Debora anawauza lonjezo la Mulungu lakuti adzagonjetsa Sisera ndi magaleta ake 900. Lonjezo limeneli linadabwitsa Baraki. Aisiraeli analibe gulu lankhondo lamphamvu komanso analibe zida zankhondo zokwanila. Ngakhale n’telo, Baraki anavomela kupita kunkhondo, koma anafuna kupitila limodzi ndi Debora.—Oweruza 4: 6-8; 5: 6-8.

Anthu ena amakamba kuti Baraki analibe cikhulupililo cifukwa ca kupempha Debora kuti apitile naye limodzi, koma zimenezo sizoona. Iye sanapemphe Mulungu kumupatsa zida zambili zankhondo. Baraki, monga munthu wa cikhulupililo anaona kufunika kopita ndi munthu woimilako Yehova, kuti iye ndi gulu lake la nkhondo alimbikitsidwe. (Aheberi 11:32, 33) Yehova anayankha mwa kulola Debora kupitila limodzi ndi Baraki. Koma, Yehova anauzila Debora kulosela kuti ulemelelo sudzakhala wa mwamuna aliyense. (Oweruza 4:9) Mulungu anasankha kuti mkazi adzaphe munthu woipa, Sisera.

M’dziko loipali, akazi amacitilidwa zinthu zoipa monga kupanda cilungamo, ciwawa, ndi nkhanza. Iwo sapatsidwa ulemu mmene Mulungu amafunila. Komabe, Mulungu amaona akazi ndi amuna mofanana pamaso pake. (Aroma 2:11; Agalatiya 3:28) Nkhani ya Debora imatikumbutsa kuti Yehova amadalitsa akazi ndi mwai wautumiki ndipo amawakonda ndi kuwakhulupilila. Conco, ndi kwanzelu kusatengela tsankho limene lafala m’dzikoli.

“DZIKO LINAGWEDEZEKA, KUMWAMBA KUNAGWETSA MADZI”

Baraki anasonkhanitsa gulu lake lankhondo. Anasonkhanitsa amuna olimba mtima okwanila 10,000 kuti akamenyane ndi gulu lankhondo loopsa la Sisera. Pamene Baraki anali kutsogolela gulu lake ku Phili la Tabori, anakondwela popeza anali ndi wowalimbikitsa. Baibulo limati: “Debora nayenso anapita nao.” (Oweruza 4:10) N’zosakaikitsa kuti asilikali analimbikitsidwa kwambili, kuona kuti mkazi wolimba mtima ameneyu akupita nao kunkhondo. Iye anaika moyo wake pangozi cifukwa ca cikhulupililo cake mwa Yehova Mulungu.

Sisera atamva kuti Aisiraeli akufuna kumenyana naye, anacitapo kanthu mofulumila. Mafumu acikanani anagwilizana ndi Mfumu Yabini amene anali wamphamvu kwambili kuposa mafumu onse. Gulu la nkhondo la Sisera ndi magaleta ake ambili anacititsa mantha dziko lonse. Iwo anayenda kudutsa cigwa uku akukuwa kwambili. Akanani anali otsimikiza kuseselatu adani ao mosavuta ndi mofulumila kwambili cifukwa analibe mphamvu.—Oweruza 4:12, 13; 5:19.

Nanga Baraki ndi Debora anacita ciani pamene adani ao anali kubwela? Aisiraeli akanakhala munsi mwa Phili la Tabori, zinthu sizikanawayendela bwino cifukwa magaleta ankhondo a Akanani anali kufuna malo afulati kuti amenye bwino nkhondo. Koma, Baraki anayembekezela citsogozo kucokela kwa Yehova kudzela mwa Debora. Pambuyo pake Debora anati: “Nyamuka, pakuti lelo ndi tsiku limene Yehova adzapeleka Sisera m’manja mwako. Yehova akuyendatu patsogolo pako. Ndipo Baraki anatsikadi m’phili la Tabori, amuna 10,000 akum’tsatila.”—Oweruza 4:14. *

Gulu la nkhondo la Aisiraeli linatsika m’philimo ndi kupita kukakumana ndi gulu lankhondo loopsa la adani ao. Kodi Yehova anawathandiza [Oweruza 4:14] malinga ndi lonjezo lake kudzela mwa Debora? Baibulo limayankha kuti: “Dziko linagwedezeka, kumwamba kunagwetsa madzi.” Gulu la nkhondo lamphamvu la Sisera linasokonezedwa. Kunagwa cimvula cacikulu ndipo madzi anadzala ponseponse mofulumila, cakuti magaleta ao sanathenso kuyenda cifukwa anali kumila m’matope.—Oweruza 4:14, 15; 5:4.

Baraki ndi gulu lake sanavutike ndi mvula imeneyi cifukwa anadziŵa kumene inali kucokela. Iwo anathamangila akananiwo ndi kuwapha ndipo sanasiyeko ngakhale mmodzi wa asilikali a Sisera. Mtsinje wa Kisoni unadzaza madzi ndi kukokolola onse ophedwa n’kukawasiya m’nyanja yaikulu.—Oweruza 4:16; 5:21.

Yehova anagonjetsa gulu la nkhondo la Sisera monga mmene Debora analoselela

Masiku ano, Yehova salola atumiki ake kumenya nkhondo yakuthupi. Koma amalimbikitsa anthu ake kumenya nkhondo yakuuzimu. (Mateyu 26:52; 2 Akorinto 10:4) Lelolino, tikumenya nkhondo imeneyi mwa kumvela Mulungu. Onse amene amamvela Mulungu ayenela kukhala olimba mtima cifukwa angatsutsidwe koopsa. Komabe, Yehova sanasinthe. Yehova amatetezabe anthu amene amam’khulupilila ndi kum’dalila monga mmene Debora, Baraki ndi asilikali olimba mtima aciisiraeli anacitila.

“AKHALE WODALITSIKA PAKATI PA AKAZI ONSE”

Mdani wao woipa kwambili wacikanani anathaŵa. Sisera, wopondeleza wamkulu wa adani a anthu a Mulungu, anathaŵa wapansi kucoka kumalo omenyela nkhondo. Iye anasiya anthu ake akuphedwa m’matope, ndipo anazemba asilikali aciisiraeli n’kuthaŵila kouma kwa anthu apafupi amene anali kugwilizana nao. Anathamanga kwa makilomita ambilimbili kudutsa cipululu ali ndi mantha kuti asilikali aciisiraeli am’peza. Iye anathamangila kuhema wa Hiberi mkeni amene anapatukana ndi anthu ake n’kukakhala ca kum’mwela kwa dziko lao. Hiberi anali kugwilizana ndi Mfumu Yabini.—Oweruza 4:11, 17.

Sisera anafika kuhema wa Hiberi ali wotopa kwambili. Koma panthawiyo Hiberi sanali panyumba. Mkazi wa Hiberi, Yaeli ndi amene analipo. Sisera anaganiza kuti Yaeli adzalemekeza m’gwilizano wapakati pa mwamuna wake ndi Mfumu Yabini. Iye sanayembekezele Yaeli kucita zinthu zosiyana ndi zimene mwamuna wake akanacita. Sisera sanali kum’dziŵa Yaeli. Yaeli anaona mmene Akanani anali kupondelezela anthu ndipo iye anafunika kusankha cocita. Iye anafunika kusankha, kaya kuthandiza munthu woipa ameneyu kapena kukhala ku mbali ya Yehova ndi kupha mdani wa anthu Ake. Kodi anacita ciani? Kodi mkazi anagonjetsa bwanji m’silikali wodziŵa kumenya nkhondo ameneyu?

Coyamba, Yaeli anafunika kuganiza cocita mwamsanga. Iye anapatsa Sisera malo kuti apumule. Sisera analamula mkaziyo kuti kukabwela munthu aliyense womufunafuna, asamuulule. Yaeli anam’funditsa bulangete ndipo atam’pempha madzi akumwa, anam’patsa mkaka. Atamwa mkakawo, Sisera anagona tulo tofa nato. Zitatelo, Yaeli anatenga cikhomo ndi nsando zimene akazi okhala m’mahema anali kudziŵa kuziseŵenzetsa mwaluso. Pokhala wakupha woikidwa ndi Yehova, Yaeli anayenda mwakacetecete kufika pamene panali mutu wa Sisera. Iye akanacedwa pang’ono kapena kukaikila zinthu zikanaipilatu. Kodi anakumbukila mmene munthu ameneyu anavutitsila anthu a Mulungu kwa zaka zambili? Kapena kodi anaganizila za mwai umene anali nao wokhala kumbali ya Yehova? Baibulo silikamba ciliconse. Koma cimene tikudziŵa n’cakuti Yaeli anacitapo kanthu mwamsanga, ndipo Sisera anaphedwa.—Oweruza 4:18-21; 5:24-27.

Patapita nthawi, Baraki anafika kwa Yaeli kukafunafuna mdani wake ameneyu. Pamenepo Yaeli anaonetsa Baraki mtembo wa Sisera cikhomo cili m’mutu mwa Siserayo, ndipo Baraki anazindikila kuti ulosi umene Debora anakamba wakwanilitsidwa. Inde, mkazi anapha Sisera, m’silikali wankhondo wamphamvu. Masiku ano, anthu otsutsa amaitana Yaeli ndi maina oipa osiyanasiyana. Koma Debora ndi Baraki anali kum’dziwa bwino. M’nyimbo yao, io anauzilidwa kutamanda Yaeli monga “wodalitsika pakati pa akazi onse” cifukwa ca kulimba mtima kwake. (Oweruza 4:22; 5:24) Mungaone kuti Debora analibe nsanje. Iye sanacitile nsanje Yaeli n’kulephela kumutamanda, koma anakondwela kudziŵa kuti mau a Yehova akwanilitsidwa.

Sisera ataphedwa, Mfumu Yabini sinavutitsenso Aisiraeli. Akanani sanapondelezenso Aisiraeli. Aisiraeli anakhala pa mtendele kwa zaka 40. (Oweruza 4:24; 5:31) Cifukwa ca kukhulupilila Yehova Mulungu, Debora, Baraki, ndi Yaeli anadalitsidwa. Ngati titengela cikhulupililo ca Debora, mwa kukhala kumbali ya Yehova molimba mtima ndi kulimbikitsa anthu ena, Yehova adzatiteteza ndipo tidzakhala ndi mtendele wosatha.

^ par. 7 Ena amene anali aneneli aakazi ndi Miriamu, Hulida ndi mkazi wa Yesaya.—Ekisodo 15:20; 2 Mafumu 22:14; Yesaya 8:3.

^ par. 9 Nyimbo ya Debora ikuonetsa kuti Sisera anali kubwela ndi akazi ambili kucokela kunkhondo ndipo nthawi zina anali kubweletsela m’silikali aliyense akazi aŵili kapena atatu. (Oweruza 5:30) Mau akuti “mkazi” pa lemba limeneli akutanthauza “mimba.” Mauwa akuonetsa kuti akazi amenewa anali kugwililidwa.

^ par. 17 Nkhondo imene inatsatilapo ikuchulidwa kaŵili m’Baibulo, ikufotokozedwa m’caputala 4 ndi m’nyimbo ya Debora ndi Baraki m’caputala 5 ca buku la Oweluza. Macaputala aŵiliwa ndi ogwilizana kwambili, koma caputala ciliconse cikufotokoza zinthu zimene sizinachulidwe m’caputala cina.