NKHANI YA PACIKUTO MUNGACITE CIANI KUTI MUPINDULE NA ZIMENE MUŴELENGA M’BAIBO?
Mungayambe Bwanji Kuŵelenga Baibo?
N’ciani cingakuthandizeni kuti muzisangalala poŵelenga Baibo ndi kuti mupindule na zimene mumaŵelenga? Onani mfundo zisanu zimene zathandiza anthu ambili.
Pezani malo abwino. Pezani malo abata. Pewani zinthu zosokoneza n’colinga cakuti muike maganizo anu pa zimene muŵelenga. Ndiponso pezani malo owala bwino ndi opita kamphepo kabwino kuti mumvetsetse zimene muŵelenga.
Khalani na maganizo oyenela. Baibo ni yocokela kwa Atate wathu wa kumwamba. Conco, kuti mupindule kwambili poiphunzila, muyenela kukhala na maganizo monga a mwana, amene amakhala wokonzeka kuphunzila kwa tate wacikondi. Ngati muli na maganizo ena-ake olakwika ponena za Baibo, yambani mwawaika pambali kuti Mulungu akuphunzitseni.—Salimo 25:4.
Pemphelani musanayambe kuŵelenga. M’Baibo muli maganizo a Mulungu, conco tifunika thandizo lake kuti timvetsetse zimene tiŵelenga. Mulungu walonjeza kuti adzapeleka “mzimu woyela kwa amene akum’pempha.” (Luka 11:13) Mzimu woyela ungakuthandizeni kumvetsetsa maganizo a Mulungu. M’kupita kwa nthawi, udzatsegula maganizo anu kuti mumvetsetse “zinthu zozama za Mulungu.”—1 Akorinto 2:10.
Ŵelengani na colinga cakuti muimvetsetse. Pamene muŵelenga, musakhale cabe na colinga cofuna kutsiliza nkhaniyo. Koma muziganizila mozama zimene muŵelengazo, ndipo muzidzifunsa mafunso monga awa: ‘Ni makhalidwe abwanji amene naona mwa munthu amene nikuŵelenga nkhani yake? Kodi zimene naŵelenga ningaziseŵenzetse bwanji mu umoyo wanga?’
Khalani na colinga. Kuti mupindule ndi kuŵelenga Baibo, khalani na colinga cofuna kudziŵa cinacake cimene cingakuthandizeni pa umoyo. Mwacitanzo, mukhoza kukhala na zolinga monga izi: ‘Nifuna kudziŵa zambili ponena za Mulungu.’ ‘Nifuna kukhala munthu wabwino, mwamuna kapena mkazi wabwino.’ Ndiyeno sankhani Malemba amene angakuthandizeni kukwanilitsa zolinga zanuzo. *
Mfundo zisanu zimene tafotokoza zidzakuthandizani kuti muyambe kuŵelenga Baibo. Koma kodi mungacite ciani kuti muzisangalala pamene muŵelenga Baibo? Nkhani yotsatila idzafotokoza mfundo zimene zingakuthandizeni.
^ par. 8 Ngati simudziŵa Malemba amene angakuthandizeni kukwanilitsa zolinga zanu, pemphani a Mboni za Yehova kuti akuthandizeni.