Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Thai Liang Lim/E+ via Getty Images

KHALANI MASO!

Kodi Masamba a Mcezo Akuwononga Mwana Wanu?—Mmene Baibo Ingathandizile Makolo

Kodi Masamba a Mcezo Akuwononga Mwana Wanu?—Mmene Baibo Ingathandizile Makolo

 “Matenda a maganizo pakati pa acinyamata ni vuto lofunika kulithetsa mwamsanga, ndipo tapeza kuti kambili masamba a mcezo ndiwo amapangitsa vutoli.”—Anatelo Dokotala wamkulu wacipatala ca asilikali ku America dzina lake Dr. Vivek Murthy, mu nyuzipepala yochedwa New York Times, pa June 17, 2024.

 Kodi makolo angawateteze bwanji ana awo ku zoopsa za pa masamba a mcezo? Baibo imapeleka malangizo amene angawathandize.

Zimene makolo angacite

 Ganizilani mfundo za m’Baibo izi.

 “Wocenjela amaganizila zotsatila za zimene akufuna kucita.”—Miyambo 14:15.

 Poona kuopsa kumene kulipo, musakakamizike kulola mwana wanu kugwilitsa nchito masamba a mcezo. Musanamulole kutelo, coyamba tsimikizilani kuti ni wokhwima maganizo moti angathe kutsatila malamulo anu pa nkhani ya nthawi imene munamuikila, komanso kupitiliza kukhala na mabwenzi abwino na kupewa zosayenela.

 “Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.”—Aefeso 5:16.

 Ngati mwalola mwana wanu kuseŵenzetsa masamba a mcezo, muikileni malamulo a kaseŵenzetsedwe, ndipo mufotokozeleni mmene malamulowo angamuthandizile kukhala wotetezeka. Khalani chelu kuti muone ngati mwana wanu akusintha khalidwe. Kucita izi kudzakuthandizani kuona ngati mufunika kumucepetsela nthawi yokhala pa masamba a mcezo.

Dziŵani zambili

 Baibo imakamba kuti tikukhala “nthawi yapadela komanso yovuta.” (2 Timoteyo 3:1-5) Pa nthawi imodzimodzi imapeleka malangizo amene amatithandiza kupilila. Mndandanda wa nkhani za m’Baibo zoposa 20 zothandiza makolo na ana awo upezeka mnkhani iyi yokamba za matenda a maganizo a acinyamata.