Dziko Latsopano Ili Pafupi Kwambili
Mawu a Nyimbo:
1. Mbalame ziimba nyimbo,
Mitambo ikuyenda.
Mukupita mucidikha,
Dzuŵa nayo yawala bwino.
Anzanu akuuka
Simukhulupilila.
Dziko la Paradaiso
Linalidi pafupi.
2. Mucidikha muli nyumba,
Ina ili paphili.
Anthu aimba mokondwa,
Pamene madzi akuyenda.
M’minda mwayela kale,
Ni nthawi yokolola.
Dziko lokongolali
Linalidi pafupi.
(BILIJI)
Tiuzeko anthu onse
Zimene tiyembekeza;
Sikudzakhala kulila
Zinthu zonse nzatsopano.
3. Anthu ni osangalala
Maluŵa anunkila.
Mukuitana anzanu
Pamene tsiku likuyamba.
Tiyamikila Yehova
Cifukwa cotikonda.
Madalitso onsewa
Analidi pafupi.
(BILIJI)
Nkhope yanu nthawi zonse
Imakhala yokondwela.
Siningakhulupilile
Kuti’we nakuonanso.
4. Dziko latsopano niliyembekezela.
M’lungu ndiye walonjeza
Izi zidzakwanilitsidwa.
Madalitso a m’tsogolo
Amanilimbikitsa.
Cifukwa Paradaiso
Ili pafupi kwambili.