Mvetsela na Kuona
Daunilodi
1. Si-siya kutinika Foni uceze
Na mabwenzi musangalaledi.
Cifukwa zilipo zambili zopindulitsadi
Kuposa kuceza pa foni yako.
Mabwenzi apafoni simabwenzi azoona.
Sakila mabwenzi eni-eni.
(KOLASI)
Mvetsela
Uone
Mabwenzi
Acimwemwe; osangalaladi.
Mvetsela—
Nipempha
Kuti ‘we
Usiye foni kuti nikambe nawe.
2. Kha-khala wothandiza.
Usalephele
Cifukwa cabe cokonda foni.
Ungaŵapeze mabwenzi
Okonda Yehova; othandizanso kuti um’tumikile.
Sungaŵapeze ngati uceza cabe pafoni.
Sakila mabwenzi eni-eni.
(KOLASI)
Mvetsela
Uone
Mabwenzi
Acimwemwe; osangalaladi.
Mvetsela—
Nipempha
Kuti ‘we
Usiye foni kuti nikambe nawe.
Isiye foni ticeze.
(KANSINJILO)
Ucenjeledi.
(BILIJI)
Inde, ena amanama ngati ali pafoni
Udzakhala wokondwa
Mabwenzi ukaŵapeza.
Usiye kuikonda foni.
3. Nimvetsele iwe!
Ni foni cabe’i yo;
Singakuthandize paumoyo
Zimene ufuna
Na zonse ukonda
Udzazipeza ukakumbukila kuti;
Ubwenzi wapafoni siubwenzi weniweni.
Mabwenzi alipo azoona
(KOLASI)
Mvetsela
Uone
Mabwenzi
Acimwemwe; osangalaladi.
Mvetsela—
Nipempha
Kuti ‘we
Usiye foni kuti nikambe nawe.
Uone
Mabwenzi
Acimwemwe; osangalaladi.
Mvetsela—
Nipempha
Kuti ‘we
Usiye foni kuti nikambe nawe.