Pamodzi Tilimba
Daunilodi:
(MAWU OYAMBA)
Abale athu mvelani!
Mvelani uthengawu:
1. Tili na M’lungu mmodzi.
Kulikonse ndife amodzi.
Ndife ogwilizana,
Tiimbila pamodzi mokondwa.
(MWANA WA KOLASI)
Olo zivute
Sitili tokha.
Indedi, sitili tokha.
(KOLASI)
Tonsefe, pamodzi, ndifedi amodzi.
Tonsefe, pamodzi, ndife olimbadi.
Tonse, capamodzi, tidzacilimika.
Tigwilane manja capamodzi,Pamodzi tilimba.
2. Konse-konse tiliko.
Tidziŵa ndife osiyana.
Zokonda tisiyana,
Koma timasungabe mtendele.
(MWANA WA KOLASI)
Abale athu
Konse aliko.
Ndipo timakondanadi.
(KOLASI)
Tonsefe, pamodzi, ndifedi amodzi.
Tonsefe, pamodzi, ndife olimbadi.
Tonse, capamodzi, tidzacilimika.
Tigwilane manja capamodzi,Pamodzi tilimba.
Indedi, ndifedi amodzi!
(KOLASI)
Tonsefe, pamodzi, ndifedi amodzi.
Tonsefe, pamodzi, ndife olimbadi.
Tonse, capamodzi, tidzacilimika.
Tigwilane manja capamodzi.
Pamodzi tilimba.
Pamodzi tilimba.