Timadabwa Na Nchito Zanu
Daunilodi:
1. Zimene Ufumu wacita nizambili.
Waniphunzitsa co’nadi ca m’mawu a M’lungu.
Kapolo wanu wanzelu amatidyetsadi.
Apelekanso akulu kuti aniŵete.
Pamisonkano ikulu nimaphunzila
Ndipo nthawi zonse zimanikhudzadi mtima.
Mumaonetsa cikondi pamisonkhanoyi,
Ndipo nimaphunzilanso molalikilila.
(KOLASI)
Ufumu wa M’lungu
Wacitadi zodabwitsa.
Cikhulupililo cimalimba pophunzila
Za Yehova M’lungu.
Tiyembekezela madalitso a Ufumu
2. Mwatipatsa mwayi wogwila namwe nchito.
Timaonetsa cikondi cathu polalika.
Mtendele timapeza pokutumikilani
Umatithandiza kuti ticite zabwino.
Pamene nimvela nyimbo zotsitsimula
Nimalimba kwambili; inde nimakondwela.
M’gwilizano wathu niwapadela kwambili;
Ticokela kosiyana koma tikondana.
(KOLASI)
Ufumu wa M’lungu wacitadi zodabwitsa
Cikhulupililo cimalimba pophunzila
Za Yehova M’lungu
Tiyembekezela madalitso a Ufumu.