Onani zimene zilipo

Kodi Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova N’ciyani?

Kodi Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova N’ciyani?

 Bungwe Lolamulila ni kagulu kocepa ka Akhristu okhwima omwe amapeleka malangizo kwa Mboni za Yehova pa dziko lonse. Iwo amagwila nchito zofunika ziŵili izi:

 Bungwe Lolamulila limatsatila citsanzo ca “atumwi ndi akulu ku Yerusalemu” a m’zaka za zana loyamba, amene anali kupanga zisankho zofunika zokhudza mpingo wonse wa Cikhristu. (Machitidwe 15:2) Mofanana na amuna okhulupilika amenewo, a m’Bungwe Lolamulila si ndiwo atsogoleli a gulu lathu. Iwo amatsatila malangizo a m’Baibo, ndipo amavomeleza kuti Yehova Mulungu anasankha Yesu Khristu kukhala Mutu wa mpingo.—1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:23.

Kodi n’ndani ali m’Bungwe Lolamulila?

 Amene ali m’Bungwe Lolamulila ni Kenneth Cook, Jr., Gage Fleegle, Samuel Herd, Geoffrey Jackson, Stephen Lett, Gerrit Lösch, Mark Sanderson, David Splane, na Jeffrey Winder. Amatumikila ku likulu lathu la padziko lonse ku Warwick, New York, m’dziko la America.

Kodi Bungwe Lolamulila limagwila bwanji nchito yake?

 Bungwe Lolamulila linakhazikitsa makomiti 6 amene amayang’anila mbali zosiyana-siyana za nchito yathu. Aliyense wa m’bungweli amakhala m’komiti imodzi kapena angapo.

  •   Komiti ya Agwilizanitsi: Imathandiza pa nkhani za malamulo, pakacitika matsoka acilengedwe, pakabuka nkhani za mwadzidzidzi zokhudza Mboni za Yehova komanso akamazunzidwa cifukwa ca zimene amakhulupilila.

  •   Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli: Imayang’anila nchito yosamalila atumiki a pa Beteli.

  •   Komiti Yofalitsa Mabuku: Imayang’anila nchito yopulinta mabuku ofotokoza Baibo, komanso kumanga malo a misonkhano, maofesi omasulila mabuku, na maofesi a nthambi.

  •   Komiti ya Utumiki: Imayang’anila nchito yathu yolalikila “uthenga wabwino . . . wa Ufumu.”—Mateyu 24:14.

  •   Komiti Yophunzitsa: Imayang’anila nchito yokonza malangizo auzimu amene amapelekedwa kupitila m’misonkhano, masukulu, komanso mavidiyo na zomvetsela.

  •   Komiti Yolemba Mabuku: Imayang’anila nchito yokonza malangizo auzimu amene amapezeka m’mabuku, m’magazini, na pa webusaiti. Imayang’anilanso nchito yomasulila.

 Kuwonjezela pa nchito zimene makomiti amenewa amagwila, Bungwe Lolamulila limakumana mlungu uliwonse kuti likambilane zofunikila za gulu. Pa misonkhanoyi, a m’bungweli amakambilana zimene Malemba amanena, ndipo amalola mzimu woyela wa Mulungu kuwatsogolela kuti apange zisankho mogwilizana.—Machitidwe 15:25.

Kodi ndani amathandiza a m’Bungwe Lolamulila?

 Awa ni Akhristu odalilika amene amathandizila makomiti a Bungwe Lolamulila. (1 Akorinto 4:2) Iwo ali na luso ndipo amaidziŵa bwino nchito imene iyang’anilidwa na komiti imene amathandiza. Mlungu uliwonse amapezekapo pa miting’i ya komiti imeneyo. Ngakhale kuti sapangako zigamulo, iwo amapelekapo malingalilo othandiza, amaonetsetsa kuti zimene komiti yasankha zikutsatilidwa na kuona mmene zinthu zimenezo zikuyendela. Nthawi zina, Bungwe Lolamulila limawatumiza kuti akayendele apaubale wathu m’madela osiyana-siyana pa dziko lonse. Angapatsidwenso nkhani zoti akakambe pa miting’i yapacaka kapena pa mwambo wa otsiliza maphunzilo a Giliyiadi.

MAYINA A OTHANDIZA

Komiti

Dzina

ya Agwilizanitsi

  • Ekrann, John

  • Gillies, Paul

  • Snyder, Troy

Yoona za Atumiki a pa Beteli

  • Grizzle, Gerald

  • LaFranca, Patrick

  • Molchan, Daniel

  • Scott, Mark

  • Walls, Ralph

Yofalitsa Mabuku

  • Butler, Robert

  • Corkern, Harold

  • Glockentin, Gajus

  • Gordon, Donald

  • Luccioni, Robert

  • Reinmueller, Alex

  • Sinclair, David

ya Utumiki

  • Breaux, Gary

  • Dellinger, Joel

  • Georges, Betty

  • Griffin, Anthony

  • Hyatt, Seth

  • Jedele, Jody

  • Mavor, Christopher

  • Perla, Baltasar, Jr.

  • Rumph, Jacob

  • Smith, Jonathan

  • Turner, William, Jr.

  • Weaver, Leon, Jr.

Yophunzitsa

  • Banks, Michael

  • Curzan, Ronald

  • Flodin, Kenneth

  • Malenfant, William

  • Noumair, Mark

  • Schafer, David

Yolemba Mabuku

  • Ahladis, Nicholas

  • Christensen, Per

  • Ciranko, Robert

  • Godburn, Kenneth

  • Mantz, James

  • Marais, Izak

  • Martin, Clive

  • Myers, Leonard

  • Smalley, Gene

  • van Selm, Hermanus