KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBO
Miyambo 3:5, 6—“Usamadalile Luso Lako Lomvetsa Zinthu”
“Uzikhulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukila mʼnjila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako”—Miyambo 3:5, 6, Baibulo la Dziko Latsopano.
“Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, osacilikizika pa luntha lako; Umlemekeze m’njila zako zonse, ndipo iye adzaongola mayendedwe ako.”—Miyambo 3:5, 6, Buku Lopatulika.
Tanthauzo la Miyambo 3:5, 6
Tizidalila Yehova a Mulungu kuti atipatse malangizo, m’malo modzidalila pamene tikufuna kupanga zisankho zofunika kwambili.
“Uzikhulupilila Yehova ndi mtima wako wonse.” Timaonetsa kuti timakhulupilila Mulungu tikamacita zinthu mmene iye akufunila. Tifunika kukhulupilila Mulungu ndi mtima wathu wonse. M’Baibulo, mawu akuti mtima nthawi zambili amanena za munthu wamkati, zimene ziphatikizapo mmene munthu amamvela, zolinga zake, mmene amaganizila, komanso mmene amaonela zinthu. Conco, kukhulupilila Mulungu ndi mtima wonse kumaphatikizapo zambili kuposa cabe mmene timamvela. Ndi cisankho cimene timapanga tili otsimikiza kuti Mlengi wathu adziwa zomwe zili zabwino kwa ife.—Aroma 12:1.
“Usamadalile luso lako lomvetsa zinthu.” Popeza ndife opanda ungwilo, tiyenela kudalila Mulungu m’malo modalila luso lathu la kuganiza. Tikamadzidalila kapena kumangocita zinthu potengela mmene tikumvela, tingapange zisankho zomwe poyamba zingaoneke zabwino koma zotsatila zake zingakhale zoipa. (Miyambo 14:12; Yeremiya 17:9) Nzelu za Mulungu n’zapamwamba kwambili kuposa zathu. (Yesaya 55:8, 9) Tikamatsogoleledwa ndi maganizo ake, zinthu zidzatiyendela bwino pa umoyo.—Salimo 1:1-3; Miyambo 2:6-9; 16:20.
“Uzimukumbukila mʼnjila zako zonse.” Tifunika kudziwa maganizo a Mulungu pa nkhani iliyonse yofunika pa umoyo wathu komanso popanga zisankho zofunika kwambili. Timacita izi tikamamupempha kuti atitsogolele komanso tikamacita zimene amatiuza m’Mawu ake, Baibulo.—Salimo 25:4; 2 Timoteyo 3:16, 17.
“Iye adzawongola njila zako.” Mulungu amawongola njila zathu mwa kutithandiza kuti tizitsatila mfundo zake zolungama pa umoyo wathu. (Miyambo 11:5) Zimenezi zimatithandiza kuti tisakumane ndi mavuto omwe tingathe kuwapewa ndipo timakhala ndi cimwemwe coculuka pa moyo wathu.—Salimo 19:7, 8; Yesaya 48:17, 18.
Nkhani yonse ya pa Miyambo 3:5, 6
Buku la m’Baibulo la Miyambo lili ndi mfundo zotithandiza kukhala ndi umoyo wacimwemwe komanso wosangalatsa Mulungu. Macaputala 9 oyambilila analembedwa monga kuti bambo akupeleka malangizo kwa mwana wake wamwamuna. Caputala 3, cimafotokoza madalitso amene munthu amapeza akamakonda nzelu zocokela kwa Mlengi wathu ndi kumazigwilitsa nchito.—Miyambo 3:13-26.
a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.