Ndani Amapita Kumwamba?
Yankho la m’Baibo
Mulungu amasankha Akhristu okhulupilika ocepa, amene akamwalila, amaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba. (1 Petulo 1:3, 4) Iwo akasankhidwa, amafunika kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cawo, komanso kukhala oyela m’makhalidwe awo kuti akayenelele kulandila coloŵa cawo kumwamba.—Aefeso 5:5; Afilipi 3:12-14.
Kodi amene adzapita kumwamba azikacita ciani?
Adzatumikila pamodzi na Yesu monga mafumu komanso ansembe kwa zaka 1,000. (Chivumbulutso 5:9, 10; 20:6) Iwo adzapanga “kumwamba kwatsopano,” kapena kuti boma lakumwamba limene lidzalamulila “dziko lapansi latsopano,” kutanthauza anthu. Mafumu akumwamba amenewo adzathandiza kuti zinthu padzikoli zikhale monga mmene Mulungu anali kufunila paciyambi.—Yesaya 65:17; 2 Petulo 3:13.
Ni angati adzaukitsidwa kupita kumwamba?
Baibo imaonetsa kuti anthu okwana 144,000 adzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba. (Chivumbulutso 7:4) M’masomphenya opezeka pa Chivumbulutso 14:1-3, mtumwi Yohane anaona “Mwanawankhosa ataimilila pa phili la Ziyoni. Limodzi naye panali enanso 144,000.” M’masomphenya amenewo, “Mwanawankhosa” aimila Yesu woukitsidwa. (Yohane 1:29; 1 Petulo 1:19) “Phili la Ziyoni,” liimila udindo wapamwamba wa Yesu komanso wa 144,000 amene adzalamulila naye kumwamba.—Salimo 2:6; Aheberi 12:22.
Aja oitanidwa komanso osankhidwa mwapadela kukalamulila na Khristu mu Ufumu, amachedwa “kagulu ka nkhosa.” (Chivumbulutso 17:14; Luka 12:32) Izi zionetsa kuti iwo adzakhala ocepa poyelekezela na nkhosa zina za Yesu.—Yohane 10:16.
Maganizo olakwika okhudza anthu amene amapita kumwamba
Maganizo olakwika: Anthu onse abwino amapita kumwamba.
Zoona zake: Mulungu analonjeza anthu ambili abwino kuti adzawapatsa moyo wosatha padziko lapansi.—Salimo 37:11, 29, 34.
Yesu anati: “Palibe munthu amene anakwela kumwamba.” (Yohane 3:13) Anaonetsa kuti anthu abwino amene anamwalila iye asanabwele padziko lapansi, monga Abulahamu, Mose, Yobu, na Davide, sanapite kumwamba. (Machitidwe 2:29, 34) M’malo mwake, anali ciyembekezo codzaukitsidwa kuti akhale na moyo padziko lapansi.—Yobu 14:13-15.
Kuuka kopita kumwamba kumachedwa “kuuka koyamba.” (Chivumbulutso 20:6) Izi zionetsa kuti padzakhalanso kuuka kwina, kumene n’kwa padziko lapansi.
Baibo imaphunzitsa kuti Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila, “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Lonjezo limeneli ni la padziko lapansi, cifukwa kumwamba sikunakhalepo imfa.
Maganizo olakwika: Munthu aliyense amacita kusankha yekha, kaya kulandila moyo padziko lapansi kapena kumwamba.
Zoona zake: Mulungu ndiye amasankha Akhristu okhulupilika amene adzalandila “mphoto ya ciitano . . . copita kumwamba.” (Afilipi 3:14) Pa nkhaniyi palibe munthu aliyense amene amacita kusankha yekha.—Mateyu 20:20-23.
Maganizo olakwika: Anthu onse amene akuyembekezela kudzakhala padziko lapansi ni otsika, ndipo ni osayenela kupita kumwamba.
Zoona zake: Mulungu amachula awo amene adzalandila moyo wosatha padziko lapansi kuti “anthu anga,” “anthu anga osankhidwa mwapadela,” komanso “odalitsidwa ndi Yehova.” (Yesaya 65:21-23) Iwo adzakhala na mwayi wokwanilitsa colinga ca Mulungu capoyamba ku mtundu wa anthu—moyo wosatha wangwilo m’paladaiso padziko lapansi.—Genesis 1:28; Salimo 115:16; Yesaya 45:18.
Maganizo olakwika: Nambala ya 144,000 yochulidwa m’buku la Chivumbulutso ni yophiphilitsa, si yeniyeni.
Zoona zake: Olo kuti m’buku la Chivumbulutso muli manambala ophiphilitsa, manambala ena amakamba za zinthu zenizeni. Mwacitsanzo, bukuli limakamba za “maina 12 a atumwi 12 a Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 21:14) Tiyeni tione umboni woonetsa kuti naconso ciŵelengelo ca 144,000 n’ceniceni.
Chivumbulutso 7:4 imakamba za “ciŵelengelo ca amene anadindidwa cidindo [kapena kuti amene anatsimikizilidwa kuti adzapita kumwamba], anthu okwana 144,000.” Ndipo mavesi otsatila, amakamba za gulu laciŵili limene ni “khamu lalikulu la anthu, limene palibe munthu aliyense amene anatha kuliŵelenga.” Nalonso “khamu lalikulu” limalandila cipulumutso kwa Mulungu. (Chivumbulutso 7:9, 10) Ngati nambala ya 144,000 inali yophiphilitsa pokamba za gulu la anthu lopanda ciŵelengelo, ndiye kuti sipakanakhala kusiyana pakati pa magulu aŵili amenewa. *
Kuwonjezela apo, a 144,000 amachulidwa kuti “anagulidwa kucokela mwa anthu, monga zipatso zoyambilila.” (Chivumbulutso 14:4) Mawu akuti “zipatso zoyambilila,” aimila ciŵelengelo cocepa ca anthu osankhidwa. Mawuwa amachulidwa kwa okhawo amene adzalamulila kumwamba pamodzi na Khristu. Iwo adzalamulila anthu padziko lapansi amene ciŵelengelo cawo sicikudziŵika.—Chivumbulutso 5:10.
^ ndime 16 Ponena za nambala ya 144,000 yochulidwa pa Chivumbulutso 7:4, Pulofesa wina dzina lake Robert L. Thomas anati: “Nambala yochulidwa pa lembali ni yeniyeni mosiyana na anthu ochulidwa pa Chivumbulutso 7:9. Ngati nambalayi ni yophiphilitsa, ndiye kuti manambala onse ochulidwa m’bukuli si enieni.”—Chivumbulutso 1–7: An Exegetical Commentary, tsamba 474.